Numeri 31:1-54

31  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:  “Uwabwezere+ Amidiyani+ pa zimene anachitira ana a Isiraeli. Pambuyo pake udzaikidwa m’manda kuti ukagone ndi makolo ako.”+  Chotero Mose analankhula ndi anthuwo, kuti: “Konzekeretsani amuna pakati panu, apite kunkhondo. Apite kukamenyana ndi Amidiyani, kuti Yehova awalange Amidiyaniwo pobwezera zimene anachita.+  Mutenge amuna 1,000 pa fuko lililonse la mafuko onse a Isiraeli kuti apite kunkhondo.”  Choncho amuna 1,000 anatengedwa pa fuko lililonse mwa masauzande+ a Aisiraeliwo. Amuna onse opita kunkhondo anakwana 12,000.+  Ndiyeno Mose anatumiza amunawo kunkhondo, amuna 1,000 pa fuko lililonse. Anawatumiza limodzi ndi Pinihasi,+ mwana wa wansembe Eleazara. Pinihasi ananyamula ziwiya zopatulika ndi malipenga+ operekera zizindikiro.  Amunawo anakathira nkhondo Amidiyani, monga mmene Yehova analamulira Mose, ndipo anapha mwamuna aliyense.+  Anaphanso mafumu asanu achimidiyani.+ Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Hura ndi Reba. Komanso anapha Balamu+ mwana wa Beori ndi lupanga.  Koma akazi achimidiyani ndi ana awo anawagwira ndi kuwatenga kupita nawo kwawo.+ Anafunkhanso ziweto zawo zonse ndi chuma chawo chonse. 10  Mizinda yawo yonse imene anali kukhalamo, ndi misasa yawo yonse ya mipanda anaitentha ndi moto.+ 11  Anatenga zonse zimene anafunkha,+ zomwe zinaphatikizapo anthu ndi ziweto zomwe. 12  Anatengera anthu ogwidwawo limodzi ndi zofunkha zina zonse kwa Mose, wansembe Eleazara, ndi kwa khamu la ana a Isiraeli. Anapita nawo kumsasa wawo ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, m’chipululu cha Mowabu.+ 13  Atafika nawo kumeneko, Mose ndi wansembe Eleazara, limodzi ndi atsogoleri onse a anthuwo, anatuluka kukakumana nawo kunja kwa msasa. 14  Koma Mose anakwiya nawo kwambiri atsogoleri a nkhondowo,+ atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100, amene anachokera kunkhondo. 15  Ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi akazi onse mwawasiya amoyo?+ 16  Kodi mwaiwala kuti akaziwa ndi amene anatsatira mawu a Balamu? Si ndiwo kodi amene ananyengerera ana a Isiraeli kuti achimwire Yehova pa zochitika za ku Peori,+ kuti mliri ugwere khamu la anthu a Yehova?+ 17  Tsopano iphani mwana wamwamuna aliyense pakati pa anawa, ndiponso muphe mkazi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna.+ 18  Koma ana aakazi onse aang’ono amene sanagonepo ndi mwamuna musawaphe.+ 19  Mumange msasa kunja kwa msasawu, ndipo mukhalemo masiku 7. Aliyense amene wapha munthu,+ ndi aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu wophedwa,+ nonsenu, mudziyeretse+ pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku la 7. Mudziyeretse limodzinso ndi anthu amene mwawagwirawo. 20  Muyeretse chovala chilichonse, chinthu chilichonse chachikopa, chilichonse chopangidwa ndi ubweya wa mbuzi, ndi chilichonse chopangidwa ndi mtengo.”+ 21  Tsopano wansembe Eleazara anauza asilikali amene anapita kunkhondo aja kuti: “Tamverani zimene Yehova analamula Mose, 22  ‘Zinthu zagolide, zasiliva, zamkuwa, zachitsulo, zatini ndi zamtovu, 23  chilichonse chimene sichingapse ndi moto,+ chidutse pamoto kuti chikhale choyera. Muchiyeretsenso ndi madzi.+ Koma chilichonse chimene chingapse ndi moto muchiyeretse ndi madzi.+ 24  Mudzachape zovala zanu pa tsiku la 7 kuti mudzakhale oyera, pambuyo pake mudzalowe mumsasa.’”+ 25  Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: 26  “Iweyo ndi wansembe Eleazara ndi atsogoleri a khamulo, mutenge zofunkha zonse, zomwe zikuphatikizapo anthu ndi ziweto. 27  Zofunkhazo muzigawe pawiri. Hafu iperekedwe kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, ndipo hafu inayo iperekedwe kwa khamu la anthuwo.+ 28  Monga msonkho+ kwa Yehova, pa gawo loperekedwa kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 500 zilizonse, pa anthu, ng’ombe, abulu, ndi nkhosa. 29  Zimenezi muzitenge pa hafu imene iwo ati alandire, ndipo muzipereke kwa wansembe Eleazara monga chopereka kwa Yehova.+ 30  Pa hafu imene ana a Isiraeli ati alandire, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu, ng’ombe, abulu, ndi nkhosa, ndi pa ziweto za mtundu uliwonse. Muzipereke kwa Alevi,+ amene amatumikira pachihema cha Yehova chopatulika.”+ 31  Choncho Mose ndi wansembe Eleazara anachita monga Yehova analamulira Mose. 32  Zofunkha zonse zimene analanda amene anapita kunkhondowo zinalipo nkhosa 675,000, 33  ng’ombe 72,000, 34  ndi abulu 61,000. 35  Anthu onse,+ kutanthauza atsikana amene sanagonepo ndi mwamuna,+ analipo 32,000. 36  Pa hafu imene inapatsidwa kwa amuna omwe anapita kunkhondo panali nkhosa 337,500. 37  Pa nkhosa zimenezi, 675 zinali za msonkho+ wa Yehova. 38  Pa hafuyo, ng’ombe zinalipo 36,000. Pa ng’ombe zimenezi, 72 zinali za msonkho wa Yehova. 39  Abulu analipo 30,500, ndipo 61 anali a msonkho wa Yehova. 40  Anthu analipo 16,000, ndipo 32 anali a msonkho wa Yehova. 41  Ndiyeno Mose anapereka msonkhowo kwa wansembe Eleazara+ ngati chopereka kwa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose.+ 42  Pa hafu imene Mose anagawira ana a Isiraeli, pa zofunkha zobwera ndi amuna ochokera kunkhondo, panali izi: 43  Nkhosa 337,500, 44  ng’ombe 36,000, 45  abulu 30,500, 46  ndipo anthu analipo 16,000. 47  Ndiyeno pa hafu yoperekedwa kwa ana a Isiraeliyo, Mose anatengapo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu ndi pa ziweto. Zimenezi anazipereka kwa Alevi+ otumikira pachihema cha Yehova chopatulika,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 48  Tsopano atsogoleri a masauzande a asilikali+ anafika kwa Mose. Iwowa anali atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100.+ 49  Atafika kwa Mose anati: “Atumiki anufe tawerenga amuna onse ankhondo amene tikuwayang’anira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene akusowapo.+ 50  Tsopano lolani kuti aliyense wa ife apereke zimene wabwera nazo monga chopereka kwa Yehova,+ zinthu zagolide, matcheni ovala m’miyendo, zibangili, mphete zachifumu,+ ndolo,* ndi zodzikongoletsera zina za akazi.+ Tipereke zimenezi kwa Yehova kuti ziphimbe machimo athu.” 51  Chotero Mose ndi wansembe Eleazara analandira golideyo kwa iwo,+ kutanthauza zokongoletsera zonse zamtengo wapatali. 52  Golide yense amene anam’pereka kwa Yehova anakwana masekeli 16,750. Uyu ndiye golide amene anaperekedwa ndi atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100. 53  Aliyense wa amuna amene anapita kunkhondowo anabwerako ndi zofunkha zake.+ 54  Choncho Mose ndi wansembe Eleazara analandira zinthu zagolidezo kwa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100. Ndipo zinthu zagolidezo anakaziika m’chihema chokumanako, kuti zikhale chikumbutso+ kwa ana a Isiraeli pamaso pa Yehova.

Mawu a M'munsi

Ena amati “masikiyo.”