Numeri 6:1-27
6 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:
2 “Lankhula ndi ana a Isiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Munthu aliyense, mwamuna kapena mkazi, akachita lonjezo lapadera lokhala Mnaziri+ kwa Yehova,
3 azisala vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa.+ Asamamwe ngakhale viniga* wochokera ku vinyo, kapena viniga wochokera ku zakumwa zina zoledzeretsa, kapenanso madzi a mphesa. Ndiponso asamadye mphesa zaziwisi kapena zouma.
4 Masiku ake onse okhala Mnaziri, asamadye chilichonse chochokera ku mtengo wa mpesa, kaya zikhale mphesa zosapsa kapena khungu lake.
5 “‘Masiku onse a lonjezo lake lokhala Mnaziri, lezala lisadutse kumutu kwake+ kufikira atatha masiku ake amene anadzipereka kwa Yehova. Azikhala woyera mwa kusiya tsitsi+ lake la kumutu kuti likule.
6 Masiku onse amene iye ali wodzipereka kwa Yehova, asamakhudze mtembo.+
7 Asadziipitse pokhudza ngakhale mtembo wa bambo ake, mayi ake, m’bale wake kapena mlongo wake, iwo akamwalira.+ Asadziipitse nawo chifukwa chizindikiro cha unaziri wake kwa Mulungu chili kumutu kwake.
8 “‘Iye ndi woyera kwa Yehova masiku onse a unaziri wake.
9 Koma ngati munthu wina wafera pambali pake mwadzidzidzi,+ moti Mnaziriyo waipitsa mutu umene uli ndi chizindikiro cha unaziri wake pokhudza mtembowo, amete tsitsi+ la kumutu kwake pa tsiku la kuyeretsedwa kwake. Alimete pa tsiku la 7.
10 Ndipo pa tsiku la 8, abweretse ana a njiwa awiri, kapena ana a nkhunda awiri kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako.+
11 Wansembeyo atenge mwana mmodzi wa njiwa kapena wa nkhunda n’kumupereka monga nsembe yamachimo.+ Atengenso mwana wa njiwa kapena wa nkhunda winayo n’kumupereka monga nsembe yopsereza.+ Achite zimenezi kuti aphimbe machimo a munthuyo, popeza wachimwa pokhudza mtembo. Akatero aziyeretsa mutu wake pa tsikulo.
12 Munthuyo ayambirenso masiku ake odzipereka kwa Yehova ngati Mnaziri,+ ndipo abweretse nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi monga nsembe ya kupalamula.+ Masiku oyamba aja sadzawerengedwa chifukwa anaipitsa unaziri wake.
13 “‘Nali lamulo lokhudza Mnaziri: Pa tsiku limene masiku a unaziri wake atha,+ amubweretse pakhomo la chihema chokumanako.
14 Ndipo apereke kwa Yehova nsembe ya iye mwini. Nsembeyo ikhale nkhosa yaing’ono yamphongo yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yopsereza.+ Aperekenso mwana wa nkhosa wamkazi wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yamachimo.+ Komanso apereke nkhosa yamphongo yopanda chilema, monga nsembe yachiyanjano.+
15 Aperekenso dengu la mikate yozungulira yoboola pakati. Mikateyo ikhale yopanda chofufumitsa, yophika ndi ufa wosalala,+ ndi yopaka mafuta.+ M’dengumo mukhalenso timikate topyapyala topanda chofufumitsa topaka mafuta,+ limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+
16 Wansembeyo abweretse zinthuzo pamaso pa Yehova, ndipo am’perekere nsembe yake yamachimo ndi nsembe yake yopsereza.+
17 Am’perekerenso nkhosa yamphongo monga nsembe yachiyanjano+ kwa Yehova, limodzi ndi dengu la mikate yopanda chofufumitsa ija. Kenako, wansembeyo apereke nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa, zimene zimayendera limodzi ndi nsembe yachiyanjanoyo.
18 “‘Mnaziriyo azimeta tsitsi+ la kumutu kwake, lomwe ndi chizindikiro cha unaziri wake. Azilimetera pakhomo la chihema chokumanako. Akatero, azitenga tsitsi la mutu wake wa unazirilo, n’kuliponya pamoto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.
19 Wansembe atenge mwendo wakutsogolo wa nkhosa yamphongo umene wawiritsidwa.+ Atengenso m’dengumo mkate woboola pakati wopanda chofufumitsa, ndi kamkate kopyapyala kopanda chofufumitsa.+ Zinthuzi aziike m’manja mwa Mnaziriyo atameta chizindikiro cha unaziri wake.
20 Tsopano wansembeyo aweyulire* zinthuzo uku ndi uku monga nsembe yoweyula kwa Yehova.+ Zinthuzi zipite kwa wansembeyo ngati mphatso yopatulika, limodzi ndi nganga+ ya nsembe yoweyulayo, komanso mwendo umene aupatula kuti ukhale chopereka.+ Pambuyo pake yemwe anali Mnaziriyo angathe kumwa vinyo.+
21 “‘Limeneli ndilo lamulo kwa Mnaziri+ amene anachita lonjezo, lamulo lokhudza nsembe zimene ayenera kupereka kwa Yehova, kupatula zina zowonjezera zimene angathe kupereka mwa iye yekha. Achite mogwirizana ndi lonjezo lake, popeza ndilo lamulo la unaziri wake.’”
22 Kenako Yehova analankhula ndi Mose, kuti:
23 “Lankhula ndi Aroni ndiponso ana ake kuti, ‘Muzidalitsa+ ana a Isiraeli motere:
24 “Yehova akudalitseni+ ndi kukusungani.+
25 Yehova akukomereni mtima,+ ndipo akuyanjeni.+
26 Yehova akuyang’aneni mokondwera+ ndipo akupatseni mtendere.”’+
27 Aroni ndi ana ake amveketse dzina langa+ pakati pa ana a Isiraeli kuti ndiwadalitse.”+
Mawu a M'munsi
^ “Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinali kupangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.