Nyimbo ya Solomo 6:1-13

6  “Kodi wachikondi wako wapita kuti, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse?+ Kodi wachikondi wako walowera kuti, kuti tikuthandize kum’funafuna?”  “Wachikondi wanga watsetserekera kumunda wake,+ kumabedi am’munda a maluwa onunkhira,+ kuti akadyetse ziweto+ kuminda, ndiponso kuti akathyole maluwa.  Wachikondi wangayo, ine ndine wakewake ndipo iye ndi wangawanga.+ Iye akudyetsera ziweto msipu+ umene uli pakati pa maluwa.”  “Wokondedwa wangawe, ndiwe wokongola+ ngati Mzinda Wosangalatsa.+ Ndiwe wooneka bwino ngati Yerusalemu,+ ndipo ndiwe wogometsa ngati magulu a asilikali+ amene azungulira mbendera.+  Yang’ana kumbali kuti maso ako+ asandiyang’anitsitse, chifukwa akundichititsa mantha. Tsitsi lako likuoneka ngati gulu la mbuzi zimene zikudumphadumpha potsetsereka kuchokera ku Giliyadi.+  Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zazikazi zimene zikuchokera kozisambitsa, zonse zitabereka mapasa, popanda imene ana ake afa.+  M’mbali mwa mutu wako muli ngati khangaza logamphula pakati, munsalu yako yophimba kumutuyo.+  Pakati pa mafumukazi 60, adzakazi* 80 ndi atsikana osawerengeka,+  pali mmodzi yekha amene ali njiwa yanga,+ wopanda chilema.+ Iye ndiye mwana wamkazi wapadera kwambiri kwa mayi ake. Iyeyo ndi wosadetsedwa kwa mayi amene anam’bereka. Ana aakazi atamuona, anamutcha wodala. Mafumukazi ndi adzakazi anamutamanda+ kuti, 10  ‘Kodi mkazi+ amene akuyang’ana pansi ngati m’bandakuchayu ndani,+ wokongola ngati mwezi wathunthu,+ wosadetsedwa ngati dzuwa lowala,+ wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera?’”+ 11  “Ine ndinatsetserekera kumunda+ wa mitengo ya zipatso zokhala ngati mtedza, kuti ndikaone maluwa ake m’chigwa,*+ kuti ndikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira, ndiponso ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.+ 12  Mosazindikira, mtima wanga unandifikitsa kumagaleta a anthu olemekezeka a mtundu wanga.” 13  “Bwerera, bwerera iwe Msulami! Bwerera, bwerera kuti tikuone!”+ “Kodi anthu inu mukuona chiyani mwa ine Msulami?”+ “Tikuona ngati tikuonerera gule wa magulu awiri a anthu.”

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.