Oweruza 1:1-36
1 Ndiyeno zinachitika kuti Yoswa atamwalira,+ ana a Isiraeli anafunsira+ kwa Yehova kuti: “Ndani wa ife adzayamba kupita kwa Akanani kukamenyana nawo?”
2 Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Fuko la Yuda ndilo lidzayamba kupita.+ Ndipo ndidzaperekadi dzikolo m’manja mwawo.”
3 Ndiyeno a fuko la Yuda anauza abale awo a fuko la Simiyoni kuti: “Tiyeni tipitire limodzi m’gawo la fuko lathu+ kuti tikamenyane ndi Akanani. Kenako ifenso tidzapita nanu kugawo lanu.”+ Choncho fuko la Simiyoni linapita nawo.+
4 Pamenepo fuko la Yuda linakwezeka mtunda, ndipo Yehova anapereka Akanani ndi Aperezi m’manja mwawo,+ mwakuti anagonjetsa amuna 10,000 ku Bezeki.
5 Atapeza Adoni-bezeki ku Bezeki anamenyana naye mpaka kugonjetsa Akanani+ ndi Aperezi.+
6 Pamenepo Adoni-bezeki anathawa, ndipo anam’thamangitsa ndi kum’gwira. Atam’gwira, anam’dula zala zamanthu za m’manja ndi zala zazikulu za kumapazi.
7 Zitatero, Adoni-bezeki anati: “Panali mafumu 70 odulidwa zala zamanthu za m’manja ndi zala zazikulu za kumapazi, amene anali kutola chakudya pansi pa tebulo langa. Mulungu wandibwezera zimene ndinachita.”+ Kenako anam’tengera ku Yerusalemu+ kumene anakafera.
8 Ndiyeno ana a Yuda anapitiriza kumenyana ndi mzinda wa Yerusalemu+ n’kuulanda. Anapha anthu okhala mmenemo ndi lupanga, ndipo mzindawo anautentha ndi moto.
9 Kenako ana a Yuda anatsika kukamenyana ndi Akanani okhala m’dera lamapiri, ku Negebu+ ndi ku Sefela.+
10 Motero fuko la Yuda linapita kukamenyana ndi Akanani amene anali kukhala ku Heburoni,+ (poyamba dzina la mzinda wa Heburoni linali Kiriyati-ariba).+ Iwo anapha Sesai, Ahimani ndi Talimai.+
11 Atachoka kumeneko anapita kukamenyana ndi anthu a mumzinda wa Debiri.+ (Poyamba dzina la mzinda wa Debiri linali Kiriyati-seferi.)+
12 Pamenepo Kalebe+ anati: “Ndithudi, aliyense amene amenyane ndi mzinda wa Kiriyati-seferi ndi kuulanda, ndim’patsa Akisa+ mwana wanga kuti akhale mkazi wake.”+
13 Ndipo Otiniyeli+ mwana wa Kenazi,+ mng’ono wake wa Kalebe, analanda mzindawo.+ Choncho, Kalebe anam’patsa Akisa mwana wake kuti akhale mkazi wake.+
14 Ndiyeno zinachitika kuti pamene Akisa anali kupita kunyumba, anali kulimbikitsa Otiniyeli kuti apemphe munda kwa Kalebe bambo ake. Kenako Akisa anawomba m’manja ali pabulu.*+ Atatero, Kalebe anamufunsa kuti: “Ukufuna chiyani?”
15 Ndipo iye anati: “Ndidalitseni,+ pakuti mwandipatsa malo akum’mwera, ndipo mundipatse Guloti-maimu.”* Pamenepo Kalebe anam’patsa Guloti Wakumtunda+ ndi Guloti Wakumunsi.
16 Ndiyeno ana a munthu wa mtundu wachikeni,+ amene anali apongozi ake a Mose,+ anatuluka mumzinda wa mitengo ya kanjedza+ pamodzi ndi ana a Yuda kukalowa m’chipululu cha Yuda, chimene chili kum’mwera kwa Aradi.+ Motero iwo anayamba kukhala pamodzi ndi anthuwo.+
17 Koma a fuko la Yuda anayendabe ndi abale awo a fuko la Simiyoni, ndipo anapha Akanani okhala ku Zefati ndi kuwononga mzindawo.+ N’chifukwa chake mzindawo unatchedwa Horima.*+
18 Kenako fuko la Yuda linalanda Gaza+ ndi madera ake, Asikeloni+ ndi madera ake ndiponso Ekironi+ ndi madera ake.
19 Yehova anakhalabe ndi fuko la Yuda, moti linalanda dera lamapiri, koma silinathe kupitikitsa anthu okhala m’chigwa, chifukwa chakuti anthuwo anali ndi magaleta*+ okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo.+
20 Atapereka Heburoni kwa Kalebe monga mmene Mose analonjezera,+ Kalebe anapitikitsa ana atatu aamuna a Anaki amene anali kukhala mmenemo.+
21 Ana a Benjamini sanapitikitse Ayebusi amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ moti Ayebusiwo akukhalabe ndi ana a Benjamini m’Yerusalemu kufikira lero.+
22 Pa nthawi imeneyi, nawonso a nyumba ya Yosefe+ anapita kukamenyana ndi mzinda wa Beteli,+ ndipo Yehova anali nawo.+
23 Pamenepo a nyumba ya Yosefe anayamba kuchita ukazitape+ pamzinda wa Beteli (poyamba dzina la mzindawu linali Luzi).+
24 Ndiyeno azondi anaona mwamuna wina akutuluka mumzindawo, ndipo anamuuza kuti: “Tiuze mmene tingalowere mumzinda, ndipo tikukomera mtima.”+
25 Iye anawauzadi mmene angalowere mumzindawo, ndipo iwo anapha anthu a mumzindawo ndi lupanga,+ koma anasiya mwamunayo ndi banja lake lonse ali amoyo.+
26 Zitatero mwamunayo anapita kudziko la Ahiti+ ndi kumanga mzinda, n’kuutcha dzina lakuti Luzi. Limenelo ndilo dzina la mzindawo kufikira lero.
27 Manase+ sanatenge mzinda wa Beti-seani+ ndi midzi yake yozungulira, Taanaki+ ndi midzi yake yozungulira, ndipo sanapitikitse anthu okhala mumzinda wa Dori+ ndi midzi yake yozungulira, anthu a mumzinda wa Ibuleamu+ ndi midzi yake yozungulira, ndi anthu okhala mumzinda wa Megido+ ndi midzi yake yozungulira. Akananiwo anakakamirabe kukhala m’dziko limeneli.+
28 Ndiyeno zinachitika kuti Aisiraeli anakhala amphamvu,+ ndipo anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo,+ koma sanawachotseretu onse m’dzikolo.+
29 Fuko la Efuraimu nalonso silinapitikitse Akanani amene anali kukhala ku Gezeri, moti Akananiwo anakhalabe pakati pawo ku Gezeriko.+
30 Fuko la Zebuloni+ silinapitikitse anthu okhala mumzinda wa Kitironi ndi mzinda wa Nahaloli,+ moti Akananiwo anakhalabe pakati pawo+ ndipo a fuko la Zebuloni anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Akananiwo.+
31 Fuko la Aseri+ silinapitikitse anthu okhala mumzinda wa Ako ndi anthu okhala m’mizinda ya Sidoni,+ Alabu, Akizibu,+ Heliba, Afiki+ ndi Rehobu.+
32 Choncho Aaseri anapitirizabe kukhala pakati pa Akanani amene anali kukhala m’dzikolo, chifukwa chakuti sanawapitikitse.+
33 Fuko la Nafitali+ silinapitikitse anthu okhala m’mizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati,+ koma iwo anapitiriza kukhala pakati pa Akanani amene anali kukhala m’dzikolo.+ Ndipo fuko la Nafitali linayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo anthu okhala m’mizinda ya Beti-semesi ndi Beti-anati.+
34 Pamenepo Aamori anapitirizabe kupanikizira ana a Dani+ kudera lamapiri, ndipo sanawalole kutsikira m’chigwa.+
35 Choncho Aamori anakakamirabe kukhala m’phiri la Herese ndi m’mizinda ya Aijaloni+ ndi Saalibimu.+ Koma dzanja la nyumba ya Yosefe linakhala lamphamvu kwambiri, moti anayamba kugwiritsa ntchito yaukapolo Aamoriwo.+
36 Dera la Aamori linali kuyambira kuchitunda cha Akirabimu,+ komanso ku Sela kupita chakumtunda.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Kenako anatsetsereka (anatsika) pabulupo.”
^ Dzinali limatanthauza, “Dera la Madzi.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.