Oweruza 20:1-48
20 Chotero ana onse a Isiraeli anatuluka,+ kuchokera ku Dani+ mpaka kumunsi ku Beere-seba,+ ndipo khamu lonselo linasonkhana pamodzi mogwirizana+ kwa Yehova ku Mizipa,+ pamodzinso ndi anthu a m’dera la Giliyadi.+
2 Zitatero, atsogoleri a anthu ndi mafuko onse a Isiraeli anaimirira pakati pa mpingo wonse wa anthu a Mulungu woona.+ Amuna ogwira lupanga oyenda pansi analipo 400,000.+
3 Ana a Benjamini anamva kuti ana a Isiraeli apita ku Mizipa.+
Pamenepo ana a Isiraeli anati: “Lankhulani, kodi chinthu choipachi chachitika bwanji?”+
4 Poyankha, Mleviyo,+ mwamuna wa mkazi wophedwayo, anati: “Ine pamodzi ndi mdzakazi wanga,+ ndinafika ku Gibeya,+ m’dera la Benjamini, kuti ndigone kumeneko.
5 Ndiyeno anthu a m’Gibeya anayamba kundiukira, ndipo usiku anazungulira nyumba imene ndinalimo. Iwo anali kufuna kupha ineyo, koma anagwirira mdzakazi wanga+ mpaka anafa.+
6 Choncho ndinatenga mdzakazi wanga ndi kum’duladula, n’kutumiza ziwalozo m’dera lililonse la cholowa cha Isiraeli.+ Ndinatero chifukwa iwo anachita khalidwe lotayirira+ komanso chinthu chopusa ndi chochititsa manyazi mu Isiraeli.+
7 Nkhani yaketu ndi imeneyi, inu nonse ana a Isiraeli. Nenanipo mawu anu ndi maganizo anu.”+
8 Pamenepo anthu onse ananyamuka mogwirizana,+ ndipo anati: “Aliyense wa ife sapitanso ku hema wake kapena kupatukira kunyumba yake.+
9 Koma Gibeya tim’chitire izi: Tichite maere+ ndi kupita kukamenyana naye.
10 Ndipo m’mafuko onse a Isiraeli titengemo amuna 10 mwa amuna 100 alionse, amuna 100 mwa amuna 1,000 alionse, amuna 1,000 mwa amuna 10,000 alionse. Amenewa azipezera anthu zofunika, kuti anthuwo achitepo kanthu mwa kupita ndi kukamenyana ndi Gibeya wa ku Benjamini, chifukwa cha chinthu chochititsa manyazi ndi chopusa+ chimene achita mu Isiraeli.”
11 Chotero amuna onse a Isiraeli anasonkhana mogwirizana kuti amenyane ndi mzinda wa Gibeya, atapanga gulu limodzi lankhondo.
12 Ndiyeno mafuko a Isiraeli anatumiza amuna kwa atsogoleri onse a fuko la Benjamini,+ kuti: “Kodi chinthu choipachi chimene chachitika pakati panu n’chiyani?+
13 Ndiyetu tipatseni amunawo,+ anthu opanda pakewo,+ amene ali mu Gibeya,+ kuti tiwaphe+ ndi kuchotsa choipachi mu Isiraeli.”+ Koma ana a Benjamini sanafune kumvera mawu a abale awo, ana a Isiraeli.+
14 Ndiyeno ana a Benjamini anasonkhana pamodzi ku Gibeya, kuchokera m’mizinda, kuti akamenyane ndi ana a Isiraeli.
15 Choncho ana a Benjamini anasonkhana pamodzi tsiku limenelo kuchokera m’mizinda. Iwo anali amuna ogwira lupanga okwanira 26,000,+ osawerengera anthu okhala m’Gibeya, mmene anasonkhanitsa amuna 700 osankhidwa mwapadera.
16 Pakati pa anthu onsewa, panali anthu amanzere+ 700 osankhidwa mwapadera. Aliyense wa anthu amenewa anali wamaluli poponya miyala*+ ndipo sanali kuphonya.
17 Amuna ogwira lupanga a mu Isiraeli amene anasonkhanitsidwa pamodzi anali 400,000,+ kupatulapo amuna a m’dera la Benjamini. Aliyense wa amenewa anali mwamuna wankhondo.
18 Ndipo ana a Isiraeli ananyamuka ndi kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu,+ kuti: “Ndani wa ife ayenera kutitsogolera kunkhondo yomenyana ndi ana a Benjamini?”+ Poyankha, Yehova anati: “Yuda akutsogolereni.”+
19 Zitatero, ana a Isiraeli ananyamuka m’mawa kwambiri ndi kukamanga msasa kuti amenyane ndi Gibeya.
20 Tsopano amuna a Isiraeli anapita kukamenyana ndi ana a Benjamini ku Gibeya, ndipo kumeneko amuna a Isiraeliwo anafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo.
21 Zitatero, ana a Benjamini anatuluka m’Gibeya+ ndi kupha amuna a Isiraeli 22,000 tsiku limenelo, n’kusiya mitembo yawo itagonagona pansi.+
22 Koma anthuwo, amuna a Isiraeli, analimba mtima ndipo anapitanso kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo pamalo omwe anafola tsiku loyamba lija.
23 Ndiyeno ana a Isiraeli anapita ku Beteli ndipo analira+ pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsira kwa Yehova, kuti: “Kodi ndipitenso kukamenyana ndi ana a m’bale wanga Benjamini?”+ Poyankha, Yehova anati: “Pita, kamenyane naye.”
24 Chotero ana a Isiraeli anapitanso kwa ana a Benjamini tsiku lachiwiri.+
25 Pamenepo ana a Benjamini anatuluka m’Gibeya kudzakumana nawo tsiku lachiwirilo, ndipo anaphanso amuna ena 18,000 mwa ana a Isiraeli, n’kusiya mitembo yawo itagonagona pansi.+ Ophedwa onsewa anali amuna ogwira lupanga.+
26 Zitatero, ana onse a Isiraeli,+ anthu onse, anapita mpaka anakafika ku Beteli. Kumeneko analira+ ndipo anakhala pansi pamaso pa Yehova ndi kusala kudya+ tsiku limenelo mpaka madzulo. Iwo anapereka nsembe zopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano+ kwa Yehova.
27 Kenako ana a Isiraeli anafunsira kwa Yehova,+ chifukwa masiku amenewo likasa la pangano+ la Mulungu woona linali ku Beteli komweko.
28 Masiku amenewo Pinihasi,+ mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni, ndiye anali kuimirira pafupi ndi likasalo.+ Chotero iye anafunsa kuti: “Kodi ndipitenso kukamenyana ndi ana a m’bale wanga Benjamini kapena ndisapite?”+ Poyankha, Yehova anati: “Pita, chifukwa mawa ndim’pereka m’dzanja lako.”+
29 Pamenepo Isiraeli anaika amuna kuti abisalire+ mzinda wonse wa Gibeya.
30 Chotero ana a Isiraeli anapita kwa ana a Benjamini tsiku lachitatu, n’kuyamba kufola mwa dongosolo lankhondo, kuti amenyane ndi Gibeya monga pa nthawi zina zoyamba zija.+
31 Ana a Benjamini atatuluka kuti akakumane ndi anthuwo, anakokedwera kutali ndi mzinda.+ Ndiyeno monga mmene zinachitikira maulendo oyamba aja, ana a Benjaminiwo anayamba kukantha ena mwa anthuwo, amuna a Isiraeli 30,+ pamisewu ikuluikulu yakunja kwa mzinda, ndi kuwavulaza koti sakanatha kuchira. Wina mwa misewu imeneyi unali wopita ku Beteli+ ndipo wina unali wopita ku Gibeya.+
32 Ndiyeno ana a Benjamini anayamba kunena kuti: “Tikuwagonjetsa mmene tinawagonjetsera ulendo woyamba uja.”+ Koma ana a Isiraeli anati: “Tiyeni tithawe+ kuti tiwakokere kumisewu ikuluikulu, kutali ndi mzindawu.”
33 Amuna onse a Isiraeli ananyamuka pamalo awo, n’kukafola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ku Baala-tamara. Zili choncho, amuna a Isiraeli amene anali atabisalira+ mzinda anali kutuluka m’malo awo pafupi ndi Gibeya.+
34 Choncho amuna osankhidwa mwapadera a Isiraeli yense, okwana 10,000 anayandikira mzinda wa Gibeya, ndipo panaulika chinkhondo choopsa. Ana a Benjamini sanadziwe kuti tsoka+ latsala pang’ono kuwagwera.
35 Yehova anagonjetsa ana a Benjamini+ pamaso pa Aisiraeli, moti pa tsiku limeneli ana a Isiraeli anapha ana a Benjamini 25,100. Onsewa anali amuna ogwira lupanga.+
36 Ana a Benjamini ataona kuti amuna a Isiraeli akuthawa,+ anaganiza kuti akugonja. Koma iwo anali kuthawa chifukwa anali kudalira amuna amene anawaika kuti abisalire mzinda wa Gibeya.
37 Ndiyeno amuna amene anabisala aja, mwamsanga anathamanga kukalowa m’Gibeya.+ Atalowa mumzindamo,+ anamwazikana ndi kukantha mzinda wonse ndi lupanga.+
38 Tsopano ana a Isiraeli anali atagwirizana ndi amuna amene anabisala aja kuti akafukize utsi mumzindamo kuti ukhale chizindikiro.+
39 Ana a Isiraeli atatembenuka ndi kuyamba kuthawa, ana a Benjamini anayamba kukantha amuna 30 mwa amuna a Isiraeli, ndi kuwavulaza moti sakanachira.+ Ana a Benjaminiwo anali kunena kuti: “Mosakayikira akugonjanso ngati mmene anagonjera pa nkhondo yoyamba ija.”+
40 Zili choncho, utsi wa chizindikiro+ uja unayamba kukwera m’mwamba kuchokera mumzindawo, ndipo unali kuoneka ngati chipilala.+ Ana a Benjamini atatembenuka, anangoona mzinda wonse ukuyaka moto.+
41 Pamenepo amuna a Isiraeli anatembenuka,+ ndipo ana a Benjamini anasokonezeka+ chifukwa anaona kuti tsoka lawagwera.+
42 Tsopano ana a Benjamini anatembenuka ndi kuyamba kuthawa amuna a Isiraeli kulowera kuchipululu, moti anapanikizidwa kwambiri. Ndiyeno amuna a Isiraeli otuluka mumzinda anali kukantha ana a Benjamini pakati pawo.
43 Iwo anazungulira ana a Benjamini.+ Anawathamangitsa osawapatsa mpata wopuma.+ Anawapondaponda m’khonde mwenimweni mwa Gibeya,+ chakotulukira dzuwa.
44 Pamapeto pake, amuna 18,000 a fuko la Benjamini anaphedwa, ndipo onsewa anali amuna amphamvu zawo.+
45 Chotero anatembenuka ndi kuthawira kuchipululu, kuthanthwe la Rimoni.+ Aisiraeli anapululanso ana a Benjamini 5,000 m’misewu ikuluikulu,+ ndipo anapitiriza kuwathamangitsa mpaka kukafika ku Gidomu ndi kuphanso amuna ena 2,000.
46 Pamapeto pake, ana a Benjamini onse amene anaphedwa pa tsikulo, anakwana amuna 25,000 ogwira lupanga.+ Onsewa anali amuna amphamvu zawo.
47 Koma amuna 600 anatembenuka ndi kuthawira kuchipululu kuthanthwe la Rimoni. Iwo anapitiriza kukhala kuthanthwe la Rimoni+ kwa miyezi inayi.
48 Amuna a Isiraeli anabwerera kukaukira ana a Benjamini ndipo anakantha ndi lupanga zonse za m’mizinda, kuyambira anthu mpaka ziweto, ndi chilichonse chimene anapeza.+ Kuwonjezera apo, mizinda yonse imene anaipeza anaiyatsa moto.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “anali kutha kuponya mwala n’kulasa tsitsi limodzi.”