Oweruza 21:1-25
21 Tsopano amuna a Isiraeli analumbira ali ku Mizipa+ kuti: “Aliyense wa ife sadzapereka mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi mwamuna wa fuko la Benjamini.”+
2 Ndiyeno anthuwo anapita ku Beteli+ ndi kukhala pansi kumeneko pamaso pa Mulungu woona+ mpaka madzulo. Iwo anali kulira kwambiri mofuula.+
3 Iwo anali kunena kuti: “N’chifukwa chiyani chinthu chimenechi chachitika mu Isiraeli, inu Yehova Mulungu wa Isiraeli? N’chifukwa chiyani lero fuko limodzi lasowa mu Isiraeli?”+
4 Ndiyeno tsiku lotsatira, anthuwo anadzuka m’mawa kwambiri ndi kumanga guwa lansembe pamenepo, ndipo anapereka nsembe zopsereza+ ndi nsembe zachiyanjano.+
5 Kenako ana a Isiraeli anati: “Ndani mwa mafuko onse a Isiraeli amene sanabwere kwa Yehova pamodzi ndi mpingo wonse? Pajatu tinachita lumbiro lalikulu+ lokhudza aliyense amene sanabwere kwa Yehova ku Mizipa, lakuti: ‘Ameneyo aphedwe ndithu.’”+
6 Ndipo ana a Isiraeli anayamba kumva chisoni chifukwa cha Benjamini m’bale wawo. Choncho anati: “Lero fuko limodzi ladulidwa ndi kuchotsedwa mu Isiraeli.
7 Tsopano popeza kuti ife talumbira+ pali Yehova kuti sitiwapatsa ana athu aakazi kuti akhale akazi awo,+ tichita chiyani ndi anthu amene atsala opanda akaziwa?”
8 Iwo anapitiriza kunena kuti: “Ndani mwa mafuko a Isiraeli amene sanabwere kwa Yehova ku Mizipa?”+ Pamenepo anaona kuti ku msasawo sikunabwere aliyense wochokera ku Yabesi-giliyadi+ kudzagwirizana ndi mpingowo.
9 Atawerenga anthuwo, anaona kuti panalibe ngakhale munthu mmodzi wochokera pakati pa anthu okhala ku Yabesi-giliyadi.
10 Chotero khamu la Isiraelilo linatumiza amuna amphamvu kwambiri okwana 12,000, ndipo anawalamula kuti: “Pitani, mukaphe ndi lupanga anthu okhala ku Yabesi-giliyadi. Mukaphe ngakhale akazi ndi ana aang’ono.+
11 Zoti mukachite ndi izi: Mukaphe mwamuna aliyense komanso mkazi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna.”+
12 Koma pakati pa anthu okhala ku Yabesi-giliyadi+ anapeza atsikana 400, anamwali+ amene anali asanagonepo ndi mwamuna. Amenewa anawabweretsa ku msasa ku Silo,+ m’dziko la Kanani.
13 Ndiyeno khamu lonse linatumiza anthu kukalankhula ndi ana a Benjamini amene anali kukhala kuthanthwe la Rimoni,+ ndi kuwalonjeza mtendere.
14 Choncho, Abenjaminiwo anabwerera pa nthawiyo. Ndipo anawapatsa akazi amene anawasunga ndi moyo pakati pa akazi a ku Yabesi-giliyadi,+ koma sanawapezere akazi okwanira.+
15 Anthuwo anamvera chisoni Abenjamini,+ chifukwa Yehova anawononga mgwirizano wa mafuko a Isiraeli.
16 Ndiyeno akulu a khamulo ananena kuti: “Tsopano popeza kuti akazi awonongedwa m’fuko la Benjamini, tichita chiyani ndi amuna amene atsala opanda akaziwa?”
17 Iwo anati: “Payenera kukhala cholowa kwa amene anathawa m’fuko la Benjamini,+ kuti fuko lililonse lisafafanizidwe mu Isiraeli.
18 Koma ife sitikuloledwa kuwapatsa ana athu aakazi kuti akhale akazi awo, chifukwa ana a Isiraeli analumbira kuti, ‘Aliyense wopereka mkazi kwa mwamuna wa fuko la Benjamini ndi wotembereredwa.’”+
19 Pamapeto pake anati: “Pajatu ku Silo+ kumachitika chikondwerero cha Yehova chaka ndi chaka. Mzinda wa Silo uli kum’mwera kwa Beteli, chakum’mawa kwa msewu waukulu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu,+ ndiponso chakum’mwera kwa Lebona.”
20 Choncho analamula ana a Benjamini kuti: “Pitani, mukawabisalire m’minda ya mpesa.
21 Ndiyeno mukakaona ana aakazi a ku Silo akubwera kuti adzavine+ magule ovina mozungulira, mukavumbuluke m’minda ya mpesayo, ndipo aliyense akagwire mkazi mokakamiza pakati pa ana aakazi a ku Silo, ndi kupita nawo kudziko la Benjamini.
22 Abambo awo kapena abale awo akabwera kudzatiimba mlandu, tidzawauza kuti, ‘Tikomereni mtima powathandiza iwowa, chifukwa chakuti panthawi ya nkhondo, ife sitinagwire akazi okwanira Abenjamini onse.+ Ndipotu inu simunawapatse ana anuwo kapena alongo anuwo mwa kufuna kwanu, zimene zikanachititsa kuti mukhale ndi mlandu chifukwa cha lumbiro limene tinapanga lija.’”+
23 Chotero ana a Benjamini anachitadi zomwezo. Pakati pa akazi amene anali kuvina+ mozungulira, anagwirapo akazi okwanira chiwerengero chawo.+ Atatero, anachoka ndi kubwerera kumalo awo ndipo anamanga mizinda+ ndi kukhalamo.
24 Pa nthawiyo, ana a Isiraeli anayamba kumwazikana kuchoka kumeneko, aliyense anapita ku fuko lake ndi ku banja lake. Iwo anachoka kumeneko, moti aliyense anapita ku cholowa chake.+
25 Masiku amenewo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Aliyense anali kuchita zimene anali kuona kuti n’zoyenera.+