Oweruza 8:1-35
8 Pamenepo amuna a ku Efuraimu anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani watichitira zimenezi? Bwanji sunatiitane pokamenya nkhondo ndi Amidiyani?”+ Ndipo iwo anayesetsa mwamphamvu kuti achite naye mkangano.+
2 Chotero iye anawayankha kuti: “Kodi ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?+ Kodi zokunkha za Efuraimu+ si zabwino kwambiri kuposa mphesa zimene Abi-ezeri+ wakolola?
3 Kodi Mulungu sanapereke Orebi ndi Zeebi,+ akalonga a Midiyani m’manja mwanu? Ndipo ine ndachita chiyani poyerekeza ndi inu?” Atanena mawu amenewa, mkwiyo wawo unaphwa.+
4 Kenako, Gidiyoni anafika ku Yorodano n’kuwoloka mtsinjewo pamodzi ndi amuna 300 amene anali nawo aja, ali otopa koma akuthamangitsabe adaniwo.
5 Ndiyeno iye anapempha amuna a ku Sukoti+ kuti: “Chonde, patsaniko anthu amene akunditsatirawa+ mitanda yobulungira ya mkate chifukwa ndi otopa, pakuti ndikuthamangitsa Zeba+ ndi Zalimuna,+ mafumu a Midiyani.”
6 Koma poyankha, akalonga a ku Sukoti anati: “Tipatsirenji asilikali ako mkate ngati kuti wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?”+
7 Pamenepo Gidiyoni anawauza kuti: “N’chifukwa chake Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna m’manja mwanga, ndithu, ndidzakukwapulani ndi mitengo yaminga ya m’chipululu komanso ndi zitsamba zaminga.”+
8 Choncho anapitiriza ulendo wake kuchoka kumeneko n’kupita ku Penueli.+ Atafika ku Penueli, anawapemphanso chimodzimodzi, koma amuna a kumeneko anamuyankha mofanana ndi mmene amuna a ku Sukoti anamuyankhira.
9 Zitatero, anauzanso amuna a ku Penueli kuti: “Ndikabwerako bwino, ndidzagwetsa nsanja yanuyi.”+
10 Pamenepa n’kuti Zeba ndi Zalimuna+ ali ku Karikori pamodzi ndi asilikali awo okwana pafupifupi 15,000. Asilikaliwa ndi amene anatsala pa gulu lonse la asilikali a Kum’mawa,+ ndipo amene anali ataphedwa anali asilikali 120,000.+
11 Gidiyoni anayendabe panjira ya anthu okhala m’mahema, mpaka kukafika kum’mawa kwa Noba ndi Yogebeha.+ Kumeneko anathira nkhondo msasa wa adaniwo iwo asanakonzekere.+
12 Zeba ndi Zalimuna atathawa, iye mosazengereza anawathamangitsa mpaka kuwagwira mafumu a Midiyaniwa.+ Atatero, anachititsa gulu lawo lonse kunjenjemera ndi mantha.
13 Ndiyeno Gidiyoni mwana wa Yowasi anayamba kubwerera kuchokera kunkhondo, podzera njira yopita ku Heresi.
14 Ali m’njira, anagwira mnyamata wa ku Sukoti+ amene anam’funsa mafunso.+ Pamenepo, mnyamatayo analembera Gidiyoni mayina okwana 77 a akalonga+ ndi akulu a mzinda wa Sukoti.
15 Choncho, Gidiyoni anapita kwa amuna a mumzinda wa Sukoti ndi kuwauza kuti: “Kodi Zeba ndi Zalimuna si awa? Aja amene munandinyoza nawo ponena kuti, ‘Tipatsirenji anyamata ako otopawo mkate ngati kuti wagwira kale Zeba ndi Zalimuna?’”+
16 Ndiyeno anatenga akulu a mzindawo, n’kutenganso mitengo yaminga ya m’chipululu ndi zitsamba zaminga. Atatero, anaonetsa amuna a ku Sukotiwo zoopsa.+
17 Anagwetsanso+ nsanja ya ku Penueli+ ija, ndi kupha amuna a mumzindawo.
18 Tsopano Gidiyoni anafunsa Zeba ndi Zalimuna+ kuti: “Kodi amuna amene munapha ku Tabori+ anali otani?” Poyankha iwo anati: “Iwo anali ngati iweyo. Maonekedwe ake aliyense wa iwo anali ngati mwana wa mfumu.”
19 Pamenepo Gidiyoni anawauza kuti: “Anali abale anga, ana a amayi anga. Pali Yehova Mulungu wamoyo, sindikanakuphani mukanawasiya amoyo.”+
20 Ndiyeno anauza Yeteri mwana wake woyamba kuti: “Nyamuka uwaphe.” Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake chifukwa anachita mantha, pakuti anali akali wamng’ono.+
21 Choncho Zeba ndi Zalimuna anati: “Nyamuka iweyo utiphe wekha. Munthu amakhala ndi mphamvu+ zolingana ndi msinkhu wake.” Motero Gidiyoni ananyamuka ndi kupha+ Zeba ndi Zalimuna, ndipo anatenga zokongoletsa zooneka ngati mwezi zimene zinali pakhosi la ngamila zawo.
22 Kenako amuna a Isiraeli anauza Gidiyoni kuti: “Ukhale wotilamulira wathu,+ iweyo, mwana wako ndi mdzukulu wako, chifukwa watipulumutsa m’manja mwa Amidiyani.”+
23 Koma Gidiyoni anawayankha kuti: “Ineyo sindikhala wokulamulirani, ngakhalenso mwana wanga sakhala wokulamulirani.+ Yehova ndiye azikulamulirani.”+
24 Ndipo anawauzanso kuti: “Ndikupempheni chinthu chimodzi: Aliyense wa inu andipatse ndolo* yapamphuno+ kuchokera pa zimene wafunkha.” (Ogonjetsedwawo anali ndi ndolo zapamphuno zagolide, chifukwa anali Aisimaeli.)+
25 Pamenepo iwo anati: “Sitilephera, tipereka.” Atatero anafunyulula nsalu, ndipo aliyense anaponyapo ndolo yapamphuno kuchokera pa zimene anafunkha.
26 Kulemera kwa ndolo zapamphuno zagolide zimene anapempha, kunali masekeli* agolide 1,700, osawerengera zokongoletsa zooneka ngati mwezi,+ ndolo ndi zovala zaubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira+ zimene mafumu a Midiyani aja anali atavala, osawerengeranso mikanda imene inali pakhosi la ngamila zawo.+
27 Ndiyeno Gidiyoni anagwiritsa ntchito golideyo popanga chovala cha efodi,+ chimene anachisonyeza kwa anthu mumzinda wakwawo wa Ofira.+ Pamenepo Isiraeli yense anayamba kuchilambira ngati fano,*+ moti chinakhala msampha kwa Gidiyoni ndi nyumba yake.+
28 Choncho, Amidiyani+ anagonjetsedwa ndi ana a Isiraeli, ndipo Amidiyani sanakwezenso mutu wawo. Zitatero, dziko linakhala pa mtendere zaka 40 m’masiku a Gidiyoni.+
29 Ndipo Yerubaala,*+ mwana wa Yowasi, anabwerera kwawo ndipo anapitirizabe kukhala kunyumba kwake.
30 Gidiyoni anakhala ndi ana 70+ otuluka m’chiuno mwake, chifukwa anadzakhala ndi akazi ambiri.
31 Nayenso mdzakazi* wake wa ku Sekemu, anamubalira mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lakuti Abimeleki.+
32 M’kupita kwa nthawi, Gidiyoni mwana wa Yowasi anamwalira ali wokalamba, atakhala ndi moyo wabwino ndi wautali, ndipo anamuika m’manda a Yowasi bambo ake, mumzinda wa Ofira wa Aabi-ezeri.+
33 Ndiyeno zinachitika kuti Gidiyoni atangomwalira, ana a Isiraeli anayambanso kupembedza Abaala,+ moti anaika Baala-beriti* kukhala mulungu wawo.+
34 Ana a Isiraeliwo sanakumbukire Yehova Mulungu wawo,+ amene anawalanditsa m’manja mwa adani awo onse owazungulira,+
35 ndipo sanasonyeze kukoma mtima kosatha+ kwa anthu a m’nyumba ya Yerubaala, kapena kuti Gidiyoni, pa zabwino zonse zimene iye anachitira Isiraeli.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “masikiyo.”
^ “Sekeli” unali muyezo wachiheberi wa kulemera kwa chinthu ndiponso wotchulira ndalama. Sekeli limodzi linali lofanana ndi magalamu 11.4, ndipo mtengo wake unali wofanana ndi madola 2.20 a ku America.
^ Mawu ake enieni, “anayamba kuchita nacho chiwerewere.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Dzinali limatanthauza, “Mwini Pangano,” kapena “Baala wa Pangano.”