Tito 3:1-15
3 Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera+ ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.+ Komanso akhale okonzekera ntchito iliyonse yabwino.+
2 Asamanenere zoipa munthu aliyense, ndipo asakhale aukali.+ Koma akhale ololera,+ ndi ofatsa kwa anthu onse.+
3 Pakuti ngakhale ife nthawi inayake tinali opanda nzeru, osamvera, osocheretsedwa, akapolo a zilakolako ndi zosangalatsa zosiyanasiyana, ochita zoipa, akaduka, onyansa ndiponso achidani.+
4 Komatu Mpulumutsi+ wathu Mulungu, anaonetsa+ kukoma mtima+ ndi kukonda anthu.
5 Iye sanatero chifukwa cha ntchito+ zolungama zimene tinachita+ ayi. Koma malinga ndi chifundo+ chake, anatipulumutsa mwa kutisambitsa+ ndipo chifukwa chakuti tinasambitsidwa choncho, tinafika ku moyo+ watsopano. Komanso, anatipulumutsa potisandutsa atsopano mwa mzimu woyera.+
6 Iye anatikhuthulira mzimu umenewu kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu,+
7 kuti titayesedwa olungama+ mwa kukoma mtima kwake kwakukulu,+ tikhale olandira cholowa+ mogwirizana ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.+
8 Mawu amenewa ndi oona,+ ndipo ndikufuna kuti nthawi zonse uzinena zinthu zimenezi motsindika, kuti amene akukhulupirira Mulungu nthawi zonse aziganiza za mmene angapitirizire kuchita ntchito zabwino.+ Zinthu izi n’zabwino ndi zothandiza kwa anthu.
9 Koma iwe pewa mafunso opusa,+ kukumba mibadwo ya makolo,+ mikangano+ ndi kulimbana pa za Chilamulo,+ chifukwa zimenezi n’zosapindulitsa ndiponso n’zachabechabe.
10 Munthu wolimbikitsa mpatuko,+ usagwirizane+ nayenso utamudzudzula koyamba ndi kachiwiri,+
11 podziwa kuti munthu wotero wapotozedwa ndipo amadziimba mlandu chifukwa akudziwa kuti akuchimwa.+
12 Ndikadzatuma Atema kapena Tukiko+ kwa iwe, udzachite chilichonse chotheka kuti udzandipeze ku Nikopoli, chifukwa ndaganiza zokakhala kumeneko nyengo yachisanuyi.+
13 Zena, wodziwa Chilamulo uja, komanso Apolo, uwapatse zofunika zokwanira zapaulendo, kuti asasowe kanthu.+
14 Koma abale athu aphunzire kugwira ntchito zabwino kuti athe kupeza zinthu zofunika,+ ndiponso kuti asakhale opanda phindu.+
15 Onse amene ali nane akupereka moni.+ Undiperekere moni kwa anthu amene amatikonda chifukwa cha chikhulupiriro.
Kukoma mtima kwakukulu kukhale ndi inu nonse.+