Yesaya 14:1-32
14 Pakuti Yehova adzachitira chifundo Yakobo+ ndipo adzasankhanso Isiraeli.+ Iye adzawapatsa mpumulo m’dziko lawo.+ Alendo adzakhala nawo limodzi ndipo adzadziphatika kunyumba ya Yakobo.+
2 Anthu a mitundu ina adzawatenga n’kubwerera nawo kwawo ndipo nyumba ya Isiraeli idzatenga anthuwo kuti akhale awo m’dziko la Yehova, ndiponso kuti akhale antchito awo aamuna ndi aakazi.+ Iwo adzagwira+ anthu amene anawagwira n’kupita nawo kudziko lina ndipo azidzalamulira anthu amene anali kuwagwiritsa ntchito.+
3 M’tsiku limene Yehova adzakupatseni mpumulo ku ululu wanu, ku nsautso yanu ndi ku ukapolo wowawa umene inu munalimo,+
4 mudzanene mwambi uwu wotonza mfumu ya Babulo:
“Uja ankagwiritsa ntchito anzakeyu wasiya ndithu! Wopondereza uja waleka ndithu!+
5 Yehova wathyola ndodo ya anthu oipa, ndodo ya anthu olamulira,+
6 amene anali kumenya mwaukali anthu a mitundu yosiyanasiyana powakwapula mosalekeza,+ ndiponso amene anali kugonjetsa mitundu ya anthu mokwiya, ndi chizunzo chopanda malire.+
7 Dziko lonse lapansi lapuma, lilibenso chosokoneza.+ Anthu akusangalala ndipo akufuula mokondwera.+
8 Ngakhale mitengo ya mlombwa+ yakondwa poona zimene zakuchitikira. Nayonso mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni yakondwa, ndipo yonseyi yanena kuti, ‘Kuyambira pamene unagona pansi, palibenso munthu wodula mitengo+ amene wabwera kudzatidula.’
9 “Ngakhale Manda+ amene ali pansi agwedezeka kuti akumane nawe ukamabwera. Chifukwa cha iwe, mandawo adzutsa akufa,+ adzutsa olamulira onse a padziko lapansi okhala ngati mbuzi.+ Achititsa mafumu onse a mitundu ya anthu kunyamuka pamipando yawo yachifumu.+
10 Onsewo akulankhula nawe kuti, ‘Kodi iwenso wafooketsedwa ngati ife?+ Kodi zoonadi wafanana ndi ife?+
11 Kunyada kwako kwatsikira ku Manda limodzi ndi phokoso la zoimbira zako za zingwe.+ Mphutsi zayalana pansi pako ngati bedi, ndipo nyongolotsi zasanduka chofunda chako.’+
12 “Wagwa kuchokera kumwamba,+ wonyezimirawe, iwe mwana wa m’bandakucha! Wadulidwa n’kugwera padziko lapansi,+ iwe amene unali kupundula mitundu.+
13 Iweyo wanena mumtima mwako kuti, ‘Ndikwera kumwamba.+ Ndikweza mpando wanga wachifumu+ pamwamba pa nyenyezi+ za Mulungu. Ndikhala paphiri lokumanapo+ kumapeto kwenikweni kwa madera a kumpoto.+
14 Ndikwera pamwamba pamalo okwezeka a m’mitambo.+ Ndidzipanga kukhala wofanana ndi Wam’mwambamwamba.’+
15 “Koma adzakutsitsira ku Manda,+ pansi penipeni pa dzenje.+
16 Okuona adzakuyang’ana modabwa. Adzakuyang’anitsitsa n’kunena kuti, ‘Kodi uyu ndi munthu amene anali kugwedeza dziko lapansi uja, amene anali kunjenjemeretsa maufumu,+
17 amene anachititsa nthaka kukhala ngati chipululu, amene anagonjetsa mizinda ya padziko lapansi,+ ndiponso amene sanali kutsegulira njira akaidi ake kuti azipita kwawo?’+
18 Mafumu ena onse a mitundu ya anthu anagona pansi mu ulemerero, aliyense m’manda ake.+
19 Koma iweyo watayidwa popanda kuikidwa m’manda,+ ngati mphukira yonyansa imene ili pakati pa anthu akufa ophedwa ndi lupanga, amene akutsikira kumiyala ya m’dzenje.+ Watayidwa ngati mtembo wopondedwapondedwa.+
20 Sudzakhalira nawo limodzi m’manda, chifukwa unawononga dziko lako lomwe, ndipo unapha anthu ako omwe. Mayina a ana a anthu ochita zoipa sadzatchulidwanso mpaka kalekale.+
21 “Anthu inu, konzekerani kupha ana ake chifukwa cha zolakwa za makolo awo,+ kuti asalandenso dziko lapansi n’kulidzaza ndi mizinda.”+
22 “Ine ndidzawaukira,”+ watero Yehova wa makamu.
“M’Babulo ndidzachotsamo dzina,+ anthu otsala, ana, ndi mbadwa,”+ watero Yehova.
23 “Babulo ndidzamusandutsa malo okhala nungu* ndiponso malo a zithaphwi. Ndidzamusesa ndi tsache* la chiwonongeko,”+ watero Yehova wa makamu.
24 Yehova wa makamu walumbira+ kuti: “Ndithu zimene ndaganiza zidzachitika, ndipo zimene ndakonza sizidzalephereka.+
25 Ndidzathyola Msuri amene ali m’dziko langa+ ndipo ndidzamupondaponda pamapiri anga.+ Goli lake lidzachoka pa iwo ndipo katundu wake adzachoka pamapewa awo.”+
26 Izi ndi zimene ndatsimikiza kuchitira dziko lonse lapansi, ndipo ili ndi dzanja limene latambasuka kuti likanthe mitundu yonse ya anthu.
27 Pakuti Yehova wa makamu wagamula,+ ndani angazilepheretse?+ Dzanja lake n’limene latambasuka, ndani angalibweze?+
28 M’chaka chimene Mfumu Ahazi inamwalira,+ uthenga wamphamvu uwu unaperekedwa:
29 “Usasangalale+ iwe Filisitiya,+ kapena aliyense wokhala mwa iwe chifukwa chakuti ndodo ya amene anali kukumenya yathyoka.+ Pakuti pamuzu wa njokayo+ padzaphuka njoka yapoizoni,+ ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yothamanga, yaululu wamoto.+
30 Ana oyamba kubadwa a anthu onyozeka, ndithu adzadya chakudya. Anthu osauka adzagona pansi popanda chowaopseza.+ Ndidzapha muzu wako ndi njala, ndipo amene adzatsale mwa iwe adzaphedwa.+
31 Fuula chipata iwe! Lira mokweza mzinda iwe! Nonsenu mudzataya mtima, inu anthu okhala m’Filisitiya! Pakuti utsi ukubwera kuchokera kumpoto, ndipo palibe msilikali amene akutsalira pa magulu ake ankhondo.”+
32 Kodi munthu adzawayankha chiyani amithenga+ a mitundu ya anthu? Adzawayankha kuti, Yehova waika maziko a Ziyoni,+ ndipo anthu ake osautsika adzathawira mmenemo.
Mawu a M'munsi
^ “Nungu” ndi nyama yam’tchire yomwe ili ndi minga zodzitetezera thupi lonse.
^ Ena amati “chipserero.”