Yesaya 2:1-22
2 Zinthu zimene Yesaya mwana wa Amozi anaona zokhudza Yuda ndi Yerusalemu:+
2 M’masiku otsiriza,+ phiri la nyumba+ ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa nsonga za mapiri,+ ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa mapiri ang’onoang’ono.+ Mitundu yonse idzakhamukira kumeneko.+
3 Anthu ochokera m’mitundu yosiyanasiyana adzabwera n’kunena kuti: “Bwerani+ anthu inu. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye akatiphunzitsa njira zake, ndipo ife tidzayenda m’njira zakezo.”+ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mawu a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.+
4 Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu+ ndipo adzakonza zinthu+ zokhudza mitundu yambiri ya anthu.+ Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+
5 Inu amuna a m’nyumba ya Yakobo, bwerani tidzayende m’kuwala kwa Yehova.+
6 Pakuti mwawanyanyala anthu anu, nyumba ya Yakobo.+ Iwo adzaza ndi zinthu zochokera Kum’mawa.+ Akuchita zamatsenga+ ngati Afilisiti ndiponso ali ndi ana ambiri a alendo.+
7 Dziko lawo ladzaza ndi siliva ndi golide, ndipo ali ndi chuma chopanda malire.+ Dziko lawo ladzaza ndi mahatchi,* ndipo ali ndi magaleta* osawerengeka.+
8 Dziko lawo ladzaza ndi milungu yopanda phindu.+ Iwo amagwadira ntchito ya manja awo. Amagwadira chinthu chimene zala zawo zapanga.+
9 Anthu ochokera kufumbi anyozeka. Iwo atsika ndipo simungathe kuwakhululukira.+
10 Lowani muthanthwe ndipo dzibiseni m’fumbi chifukwa cha kuopsa kwa Yehova, ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake.+
11 Maso odzikuza a munthu wochokera kufumbi adzatsika, ndipo anthu odzikweza adzawerama.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+
12 Pakuti ilo ndi tsiku la Yehova wa makamu.+ Tsikulo lidzafikira aliyense wodzitukumula ndi wodzikweza. Lidzafikiranso aliyense wokwezeka kapena wotsika.+
13 Lidzafikira mikungudza yonse ya ku Lebanoni+ yodzikweza ndi yokwezeka. Lidzafikiranso mitengo yonse ikuluikulu ya ku Basana.+
14 Lidzafikira mapiri onse akuluakulu odzikweza ndi mapiri onse ang’onoang’ono okwezeka.+
15 Lidzafikiranso nsanja iliyonse yaitali ndi khoma* lililonse lolimba kwambiri.+
16 Lidzafikira zombo zonse za ku Tarisi,+ ndi ngalawa zonse zabwinozabwino.
17 Munthu wodzikuza wochokera kufumbi adzawerama ndipo anthu odzikweza adzatsitsidwa.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+
18 Milungu yopanda phindu idzatheratu.+
19 Mulungu akadzaimirira kuti dziko lapansi linjenjemere, anthu adzalowa m’mapanga a m’matanthwe ndi m’mayenje a m’nthaka chifukwa cha kuopsa kwa Yehova,+ ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake.+
20 M’tsiku limenelo, munthu wochokera kufumbi adzataya milungu yake yasiliva yopanda pake ndi milungu yake yagolide yopanda phindu, imene anthu anamupangira kuti aziigwadira. Adzaitayira kumene kumakhala aswiswiri* ndi mileme,+
21 kuti iye abisale m’mayenje a m’matanthwe ndi m’ming’alu ya m’miyala ikuluikulu. Adzachita zimenezi chifukwa cha kuopsa kwa Yehova, ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake,+ Mulunguyo akadzaimirira kuti dziko lapansi linjenjemere.
22 Kuti zinthu zikuyendereni bwino, musadalire munthu wochokera kufumbi amene mpweya wake uli m’mphuno mwake,+ pakuti palibe chifukwa choti mum’ganizire iyeyo.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Ena amati “chipupa,” kapena “chikupa.”
^ Ena amati “akasusum’njira.”