Yesaya 23:1-18
23 Uthenga wokhudza Turo:+ Lirani mofuula inu zombo za ku Tarisi,+ chifukwa chakuti mzindawo wasakazidwa ndipo sulinso doko. Sulinso malo oti mungafikepo.+ Anthu amva zimenezi ali kudziko la Kitimu.+
2 Khalani chete inu anthu okhala m’mphepete mwa nyanja. Amalonda a ku Sidoni,+ amene amawoloka nyanja, akulemeretsani.
3 Mbewu za ku Sihori+ ndi zokolola za kumtsinje wa Nailo, zimene zinali kuyenda pamadzi ambiri ndiponso zimene zinali kukubweretserani ndalama, zakhala phindu la mitundu ina ya anthu.+
4 Chita manyazi iwe Sidoni,+ ndiponso iwe malo achitetezo a m’mbali mwa nyanja, chifukwa nyanja yanena kuti: “Sindinamvepo zowawa za pobereka, ndipo sindinaberekepo. Sindinalerepo anyamata kapena anamwali.”+
5 Anthu adzamva chisoni chachikulu akadzamva za Turo,+ ngati mmene anamvera chisoni atamva za Iguputo.+
6 Wolokerani ku Tarisi. Lirani mofuula, inu anthu okhala m’mphepete mwa nyanja.
7 Kodi uwu ndi mzinda wanu uja, umene unali wosangalala kuyambira kalekale, kuyambira pa chiyambi pake? Mapazi ake anali kuutengera kutali kuti ukakhale ngati mlendo.
8 Ndani wapereka chigamulo+ chotsutsana ndi Turo, mzinda umene unali kuveka anthu zisoti zachifumu, umene amalonda ake anali akalonga, ndiponso umene ochita malonda ake anali anthu olemekezeka a padziko lapansi?+
9 Yehova wa makamu ndi amene wapereka chigamulo chimenechi,+ kuti anyansitse kukongola kwa mzindawo ndi kuchotsa kunyada kwake,+ ndiponso kuti anyoze anthu onse olemekezeka a padziko lapansi.+
10 Iwe mwana wamkazi wa Tarisi,+ sefukira m’dziko lako ngati kusefukira kwa mtsinje wa Nailo. Kulibenso doko la zombo zapanyanja.+
11 Mulungu watambasulira dzanja lake panyanja. Wagwedeza maufumu.+ Yehova walamula kuti malo achitetezo a ku Foinike awonongedwe.+
12 Iye wati: “Usadzakondwerenso+ namwaliwe, mwana wamkazi wa Sidoni+ woponderezedwa. Nyamuka, wolokera ku Kitimu.+ Koma ngakhale kumeneko, sukapezako mpumulo.”
13 Taonani dziko la Akasidi.+ Anthu awa, osati Asuri,+ ndi amene anapanga mzindawo kuti ukhale malo okhala nyama zam’chipululu.+ Amanga nsanja zawo zomenyerapo nkhondo.+ Agumula nyumba zake zachifumu.+ Iwo asandutsa mzindawo bwinja logumukagumuka.+
14 Inu zombo za ku Tarisi, lirani mofuula chifukwa malo anu achitetezo asakazidwa.+
15 M’tsiku limenelo, Turo adzaiwalidwa kwa zaka 70.+ Zimenezi ndi zaka za ulamuliro wa mfumu imodzi. Pamapeto pa zaka 70 zimenezo, Turo adzakhala ngati hule wa m’nyimbo yakuti:
16 “Iwe hule amene unaiwalidwa, tenga zeze n’kumazungulira mumzinda.+ Yesetsa kuimba zezeyo mwaluso. Imba nyimbo zambiri kuti ukumbukiridwe.”
17 Pamapeto pa zaka 70, Yehova adzakumbukira Turo. Mzindawo udzayambiranso kulandira malipiro+ ndipo udzachita uhule ndi maufumu onse a padziko lapansi.+
18 Phindu lake ndi malipiro ake+ zidzakhala zopatulika kwa Yehova. Phindu lakelo silidzasungidwa kapena kukundikidwa chifukwa malipiro ake adzakhala a anthu okhala pamaso pa Yehova,+ kuti anthuwo azidya mpaka kukhuta ndiponso kuti azivala zovala zokongola.+