Yesaya 3:1-26

3  Tamverani! Ambuye woona,+ Yehova wa makamu, akuchotsa mu Yerusalemu+ ndi mu Yuda zinthu zonse zofunika pa moyo. Akuchotsa mkate, madzi,+  mwamuna wamphamvu, munthu wankhondo, woweruza, mneneri,+ wowombeza, mwamuna wachikulire,+  mtsogoleri wa anthu 50,+ munthu wolemekezeka kwambiri, mlangizi, katswiri wa matsenga ndi munthu wodziwa kuseweretsa njoka.+  Ndidzaika anyamata kuti akhale akalonga awo ndipo anthu ankhanza adzawalamulira.+  Anthu azidzalamulirana mwankhanza, ndipo munthu azidzachitira nkhanza munthu mnzake.+ Mnyamata adzaukira nkhalamba,+ ndipo wonyozeka adzaukira wolemekezeka.+  Aliyense adzagwira m’bale wake m’nyumba mwa bambo ake n’kumuuza kuti: “Iwe uli ndi nsalu. Choncho ukhale wolamulira+ wathu ndipo uzilamulira mulu wa bwinjawu.”  Iye adzakweza mawu ake m’tsiku limenelo n’kunena kuti: “Ine sindikufuna kukhala womanga zilonda ndipo m’nyumba mwanga mulibe mkate kapena nsalu. Musandiike kuti ndikhale wolamulira anthuwa.”  Yerusalemu wapunthwa ndipo Yuda wagwa,+ chifukwa lilime lawo ndiponso zochita zawo n’zotsutsana ndi Yehova.+ Iwo achita zinthu zomupandukira m’maso ake olemekezeka.+  Maonekedwe a nkhope zawo akuwachitira umboni wotsutsana nawo,+ ndipo anthuwo akunena za tchimo lawo lofanana ndi la Sodomu.+ Iwo sanalibise. Tsoka kwa iwo, chifukwa adzibweretsera mavuto.+ 10  Amuna inu, nenani kuti anthu olungama zidzawayendera bwino,+ chifukwa adzadya zipatso za zochita zawo.+ 11  Tsoka kwa anthu oipa! Iwo adzaona zoopsa, chifukwa zimene anachitira ena ndi manja awo, zidzawachitikira iwowo.+ 12  Amene amagawira anthu anga ntchito, akuwagwiritsa ntchito mwankhanza, ndipo akazi ndi amene akuwalamulira.+ Inu anthu anga, amene akukutsogolerani akukusocheretsani,+ ndipo asokoneza njira yanu.+ 13  Yehova wakhala pamalo ake kuti afotokoze mlandu wake, ndipo waimirira kuti aweruze mitundu ya anthu.+ 14  Yehova adzaweruza achikulire pakati pa anthu ake ndi akalonga ake.+ “Inuyo mwatentha munda wa mpesa. Zinthu zimene zinabedwa kwa anthu ovutika zili m’nyumba zanu.+ 15  Kodi amuna inu mukutanthauza chiyani pophwanya anthu anga ndi kupera nkhope za anthu ovutika?”+ akutero Yehova wa makamu, Ambuye Wamkulu Koposa. 16  Yehova wati: “Ana aakazi a Ziyoni ndi odzikuza. Iwo amayenda atasolola makosi awo ndiponso amakopa amuna ndi maso awo. Amayenda modzigomera, ndipo akamayenda mapazi awo amachita phokoso chifukwa cha zokongoletsera zimene amavala m’mapazi.+ 17  Choncho Yehova adzachititsa zipere+ m’mutu mwa ana aakazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzayeretsa pamutu pawo.+ 18  M’tsiku limenelo Yehova adzachotsa zokongoletsera zawo zonse: zibangili za m’miyendo, zinthu zomanga kumutu, zodzikongoletsera zooneka ngati mwezi,+ 19  ndolo,* zibangili za m’manja, nsalu zofunda,+ 20  nsalu zovala kumutu, matcheni ovala kumiyendo, malamba a pachifuwa,+ zoikamo mafuta onunkhira,* zigoba zodzikongoletsera,+ 21  mphete zovala m’zala, mphete zovala pamphuno,+ 22  mikanjo yovala pa nthawi zapadera, malaya ovala pamwamba, mikanjo yabwino kwambiri, tizikwama, 23  magalasi oonera a m’manja,+ zovala zamkati, nduwira,*+ ndi nsalu zofunda zikuluzikulu.+ 24  “Ndiyeno chidzachitike n’chakuti, m’malo mwa mafuta a basamu onunkhira+ padzangokhala fungo loipa, m’malo mwa lamba padzakhala chingwe, m’malo mwa tsitsi lokonzedwa bwino padzakhala mpala,+ m’malo mwa chovala chamtengo wapatali munthu adzavala chiguduli,*+ ndipo padzakhala chipsera*+ m’malo mwa kukongola. 25  Amuna ako adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu ako amphamvu adzaphedwa pa nkhondo.+ 26  Zipata zake zidzalira+ ndipo zidzamva chisoni. Iye adzatsala wopanda chilichonse. Adzakhala pansi, padothi penipeni.”+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masikiyo.”
Mawu ake enieni, “nyumba zimene mumakhala moyo.”
“Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.
Ena amati “saka.”
Chimenechi ndi chizindikiro chimene anali kuchiika pathupi la kapolo kapena mkaidi.