Yesaya 31:1-9
31 Tsoka kwa anthu amene akupita ku Iguputo kukapempha thandizo.+ Iwo akudalira mahatchi wamba+ ndi kukhulupirira magaleta ankhondo,+ chifukwa chakuti ndi ambiri. Akudaliranso mahatchi akuluakulu chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri, koma sanayang’ane kwa Woyera wa Isiraeli ndipo sanafunefune Yehova.+
2 Iyenso ndi wanzeru+ ndipo adzabweretsa tsoka.+ Sadzabweza mawu ake+ ndipo adzaukira nyumba ya anthu ochita zoipa.+ Adzalepheretsa anthu amene amachita zopweteka anzawo, kupeza chithandizo chimene amafuna.+
3 Koma Aiguputowo ndi anthu ochokera kufumbi.+ Si Mulungu ayi. Mahatchi awo ndi zinyama,+ osati mzimu. Yehova akadzatambasula dzanja lake, amene akupereka thandizo adzapunthwa, ndipo amene akuthandizidwawo adzagwa.+ Onsewo adzatha nthawi imodzi.
4 Pakuti Yehova wandiuza kuti: “Mkango umalira moopseza, ngakhale mkango wamphamvu,+ poteteza nyama imene wagwira. Abusa ambirimbiri akaitanidwa kuti adzauthamangitse, ngakhale umve mawu awo suchita mantha ndipo ngakhale azichita phokoso suopa. M’njira yomweyo, Yehova wa makamu adzatsika kuti achite nkhondo poteteza phiri la Ziyoni ndiponso poteteza phiri lake laling’ono.+
5 Monga imachitira mbalame imene ikuuluka kuti iteteze ana ake, Yehova wa makamu adzateteza mzinda wa Yerusalemu.+ Iye adzauteteza n’kuupulumutsa.+ Adzausunga n’kuuthandiza kuti upulumuke.”
6 “Inu ana a Isiraeli, bwererani+ kwa amene mwamupandukira ndi kumulakwira kwambiri.+
7 Pakuti m’tsiku limenelo, aliyense wa inu adzataya milungu yake yasiliva yachabechabe, ndi milungu yake yagolide yopanda phindu,+ imene manja anu akupangirani n’kukuchimwitsani nayo.+
8 Msuri adzaphedwa ndi lupanga, koma osati la munthu. Lupanga lidzamudya, koma osati la munthu wochokera kufumbi.+ Iye adzathawa chifukwa cha lupangalo ndipo ana ake aamuna adzagwiritsidwa ntchito yaukapolo.
9 Thanthwe lake lidzachoka chifukwa cha mantha ndipo akalonga ake adzachita mantha chifukwa cha chizindikiro,”+ akutero Yehova, amene kuwala kwake kuli mu Ziyoni ndiponso amene ng’anjo+ yake ili mu Yerusalemu.