Yesaya 35:1-10
35 Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala.+ Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.+
2 Deralo lidzachitadi maluwa.+ Lidzasangalala ndipo lidzakondwera n’kufuula ndi chisangalalo.+ Lidzapatsidwa ulemerero wa Lebanoni+ ndi kukongola kwa Karimeli+ ndiponso kwa Sharoni.+ Padzakhala anthu amene adzaone ulemerero wa Yehova+ ndi kukongola kwa Mulungu wathu.+
3 Anthu inu limbitsani manja ofooka ndiponso mawondo agwedegwede.+
4 Amene ali ndi nkhawa mumtima mwawo muwauze kuti:+ “Limbani mtima.+ Musachite mantha.+ Pakuti Mulungu wanu adzabwera n’kudzabwezera adani anu.+ Mulungu adzabwezera chilango.+ Iye adzabwera n’kukupulumutsani.”+
5 Pa nthawi imeneyo, maso a anthu akhungu adzatsegulidwa,+ ndipo makutu a anthu ogontha adzayamba kumva.+
6 Pa nthawiyo, munthu wolumala adzakwera phiri ngati mmene imachitira mbawala yamphongo.+ Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.+ Pakuti m’chipululu mudzatumphuka madzi ndipo m’dera lachipululu mudzayenda mitsinje.
7 Malo ouma chifukwa cha kutentha adzakhala dambo la madzi, ndipo malo aludzu adzakhala malo a akasupe amadzi.+ Kumalo okhala mimbulu,+ malo ake ousako, kudzakhala udzu wobiriwira, mabango ndi gumbwa.+
8 Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+ ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero.+ Munthu wodetsedwa sadzayendamo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera. Palibe anthu opusa amene azidzayendayendamo.
9 Kumeneko sikudzakhala mkango ndipo nyama zolusa zakutchire sizidzafikako.+ Nyama zotere sizidzapezekako.+ Anthu ogulidwanso adzayenda mumsewuwo.+
10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+