Yesaya 41:1-29
41 “Zilumba inu,+ mvetserani mawu anga mutakhala chete, ndipo mitundu ya anthu+ ipezenso mphamvu. Ibwere pafupi,+ kenako ilankhule. Anthu inu bwerani kufupi nane kumalo oweruzira mlandu.+
2 “Kodi ndani anautsa winawake kuchokera kotulukira dzuwa?+ Kodi ndani anamuitana mwachilungamo kuti ayandikire kumapazi ake, kuti amupatse mitundu ya anthu pamaso pake, ndiponso kuti amuchititse kupita kukagonjetsa ngakhale mafumu?+ Kodi ndani amene anali kuwapereka kulupanga lake ngati fumbi, moti auluzika ndi uta wake ngati mapesi?+
3 Kodi ndani amene anali kuwathamangitsa? Ndani amene anali kuyenda mwamtendere ndi mapazi ake panjira imene anali asanadutsepo n’komwe?
4 Ndani wachita zimenezi,+ kuitana mibadwo kuyambira pa chiyambi?+
“Ndineyo Yehova, Woyamba,+ ndipo ndidzakhala chimodzimodzi ngakhale kwa omalizira.”+
5 Zilumba+ zinaona n’kuyamba kuopa. Malekezero a dziko lapansi anayamba kunjenjemera.+ Mitundu ya anthu inasonkhana pamodzi n’kumangobwerabe.
6 Aliyense anali kuthandiza mnzake, ndipo munthu anali kuuza mbale wake kuti: “Limba mtima.”+
7 Chotero mmisiri wa mitengo anali kulimbikitsa mmisiri wa zitsulo.+ Amene anali kusalaza zitsulo ndi nyundo anali kulimbikitsa amene anali kumenya zitsulo ndi nyundo. Ponena za ntchito yowotcherera zitsulo ndi mtovu, iye anati: “Zili bwino.” Pomalizira pake, wina anakhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwedezeke.+
8 “Koma iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga,+ iwe Yakobo amene ndakusankha,+ mbewu ya bwenzi langa+ Abulahamu.+
9 Ndakutenga kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+ ndiponso ndakuitana kuchokera kumadera akutali a dziko lapansi.+ Chotero ndinakuuza kuti, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga.+ Ndasankha iweyo+ ndipo sindinakutaye.+
10 Usachite mantha, pakuti ndili nawe.+ Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.+ Ndikulimbitsa.+ Ndithu ndikuthandiza.+ Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja+ lachilungamo.’+
11 “Taona! Onse okupsera mtima adzachita manyazi ndipo adzanyozeka.+ Anthu amene akukangana nawe sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.+
12 Anthu amene akulimbana nawe udzawafunafuna koma sudzawapeza. Anthu amene akumenyana nawe+ adzakhala ngati kulibeko ndipo sadzakhalanso ngati kanthu.+
13 Pakuti ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja.+ Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha.+ Ineyo ndikuthandiza.’+
14 “Usachite mantha, nyongolotsi iwe+ Yakobo, inuyo amuna a Isiraeli.+ Ineyo ndikuthandizani,” akutero Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli.
15 “Taona! Ndakusandutsa chopunthira mbewu,+ chida chatsopano chopunthira mbewu chokhala ndi mano. Udzapondaponda mapiri n’kuwaphwanya, ndipo zitunda udzazisandutsa mankhusu.+
16 Udzapeta+ mapiri ndi zitundazo ndipo mphepo idzaziuluza.+ Mphepo yamkuntho idzaziuluzira kumalo osiyanasiyana.+ Iweyo udzasangalala chifukwa cha Yehova.+ Udzadzitama chifukwa cha Woyera wa Isiraeli.”+
17 “Anthu ozunzika ndi osauka akufunafuna madzi,+ koma sakuwapeza. Lilime lawo lauma ndi ludzu.+ Ineyo Yehova ndidzawayankha.+ Ineyo Mulungu wa Isiraeli, sindidzawasiya.+
18 Ndidzatsegula mitsinje pamapiri opanda zomera zilizonse, ndipo pakatikati pa zigwa ndidzatsegulapo akasupe.+ Chipululu ndidzachisandutsa dambo lamadzi, ndipo dziko lopanda madzi ndidzalisandutsa pochokera madzi.+
19 M’chipululu ndidzabzalamo mtengo wa mkungudza, mtengo wa mthethe, mtengo wa mchisu, ndi mtengo wamafuta.+ M’dera lachipululu ndidzabzalamo mtengo wofanana ndi mkungudza, mtengo wa ashi,* ndi mtengo wa paini pa nthawi imodzimodziyo.+
20 Ndidzachita zimenezi kuti anthu onse pamodzi aone, adziwe, amve, ndiponso azindikire, kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi, ndiponso kuti Woyera wa Isiraeli ndi amene wachititsa zimenezi.”+
21 “Bweretsani kuno mlandu wanu wovuta,”+ akutero Yehova. “Nenani mfundo zanu,”+ ikutero Mfumu ya Yakobo.+
22 “Tionetseni ndipo mutiuze zinthu zimene zidzachitike. Tiuzeni kuti zinthu zoyambirira zinali zotani, kuti tiziganizire mozama mumtima mwathu ndi kudziwa tsogolo lake. Kapena mutiuze zinthu zimene zikubwera.+
23 Nenani zinthu zimene zikubwera m’tsogolo, kuti tidziwe kuti inu ndinu milungu.+ Inde, muyenera kuchita zabwino kapena zoipa, kuti tizionere limodzi ndi kuchita mantha.+
24 Taonani! Inuyo sindinu kanthu ndipo zimene mwachita si kanthu.+ Aliyense wokusankhani ndi wochititsa nyansi.+
25 “Ine ndautsa winawake kuchokera kumpoto, ndipo abwera.+ Iye adzaitana pa dzina langa kuchokera kotulukira dzuwa.+ Adzaukira atsogoleri ngati kuti ndi dongo+ ndiponso ngati kuti iyeyo ndi woumba amene amapondaponda dongo laliwisi.
26 “Kodi ndani wanenapo chilichonse kuchokera pa chiyambi kuti tidziwe, kapena kuchokera nthawi zakalekale kuti tinene kuti, ‘Akunena zoona’?+ Ndithu palibe amene akunena chilichonse. Ndithu palibe amene akulankhula chilichonse kuti anthu amve. Ndithu palibe aliyense amene akumva mawu alionse a anthu inu.”+
27 Pali woyamba, amene akunena kwa Ziyoni kuti: “Tamverani zimene zidzachitike!”+ Yerusalemu ndidzamupatsa munthu wobweretsa uthenga wabwino.+
28 Ndinapitiriza kuyang’ana, koma panalibe munthu aliyense. Pakati pa mafanowo panalibe aliyense amene anali kupereka malangizo,+ ndipo ndinapitiriza kuwafunsa kuti ayankhe.
29 Onsewo ali ngati chinthu choti kulibeko. Ntchito zawo si kanthu. Mafano awo opangidwa ndi zitsulo zosungunula ali ngati mphepo ndiponso zinthu zomwe si zenizeni.+
Mawu a M'munsi
^ Umenewu ndi mtengo waukulu umene umatalika mpaka mamita 15. Umakhala ndi masamba osabiriwira kwambiri ndi nthambi zotuwa ngati phulusa.