Yesaya 43:1-28
43 Tsopano iwe Yakobo, mvera zimene wanena Yehova Mlengi wako,+ yemwe anakupanga+ iwe Isiraeli. Iye wanena kuti: “Usachite mantha, pakuti ine ndakuwombola.+ Ndakuitana pokutchula dzina.+ Iwe ndiwe wanga.+
2 Ukamadzadutsa pamadzi,+ ine ndidzakhala nawe.+ Ukamadzawoloka mitsinje, madzi sadzakumiza.+ Ukamadzayenda pamoto sudzapsa ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.+
3 Pakuti ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Isiraeli ndiponso Mpulumutsi wako.+ Ndapereka Iguputo monga dipo* lokuwombolera.+ Ndaperekanso Itiyopiya+ ndi Seba m’malo mwako.
4 Chifukwa chakuti ndiwe wamtengo wapatali kwa ine,+ ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.+ Ndidzapereka anthu m’malo mwa iwe, ndipo ndidzapereka mitundu ya anthu m’malo mwa moyo wako.+
5 “Usachite mantha chifukwa ine ndili nawe.+ Ndidzabweretsa mbewu yako kuchokera kotulukira dzuwa, ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kolowera dzuwa.+
6 Ndidzauza kumpoto kuti,+ ‘Abwezere kwawo!’ ndipo ndidzauza kum’mwera kuti, ‘Usawakanize! Bweretsa ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
7 Bweretsa aliyense amene amatchedwa ndi dzina langa,+ amene ndinamulenga chifukwa cha ulemerero wanga,+ amene ndinamuumba ndiponso amene ndinamupanga.’+
8 “Bweretsa anthu akhungu ngakhale kuti ali ndi maso, ndiponso anthu ogontha ngakhale kuti ali ndi makutu.+
9 Mitundu yonse isonkhanitsidwe pamalo amodzi, ndipo mitundu ya anthu ikhale pamodzi.+ Ndani pakati pawo amene anganene zimenezi?+ Kapena ndani amene angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+ Abweretse mboni zawo+ kuti akhale olungama ndipo mbonizo zimve ndi kunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+
10 “Inu ndinu mboni zanga,”+ akutero Yehova. “Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani+ kuti mundidziwe+ ndi kundikhulupirira,+ komanso kuti mumvetse kuti ine sindinasinthe.+ Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa,+ ndipo pambuyo panga palibenso wina.+
11 Ine ndine Yehova.+ Popanda ine palibenso mpulumutsi wina.”+
12 “Ine ndanena ndipo ndapulumutsa.+ Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo,+ ine ndinachititsa kuti chipulumutsocho chimveke. Choncho inuyo ndinu mboni zanga,+ ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.+
13 “Komanso, nthawi zonse ine sindisintha.+ Palibenso wina amene angathe kupulumutsa anthu m’dzanja langa.+ Ndikayamba kuchitapo kanthu,+ ndani amene angalimbane ndi dzanja langa?”+
14 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti: “Chifukwa cha inu, ndidzawatumiza ku Babulo. Ndidzachititsa kuti zitsulo za ndende zimasuke+ ndiponso ndidzagonjetsa Akasidi amene ali m’zombo ndi kuwachititsa kulira mokuwa.+
15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu,+ Mlengi wa Isiraeli+ ndiponso Mfumu yanu.”+
16 Izi n’zimene Yehova wanena, yemwe amapanga njira panyanja. Amapanga msewu ngakhale pamadzi amphamvu.+
17 Amatsogolera magaleta ankhondo ndi mahatchi, komanso gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu pa nthawi imodzi.+ Iye wanena kuti: “Iwo adzagona pansi,+ sadzadzuka+ ndipo adzatha.+ Adzazimitsidwa ngati chingwe cha nyale.”+
18 “Musakumbukire zinthu zoyambirira, ndipo musaganizirenso zinthu zakale.
19 Taonani! Ndikupanga zinthu zatsopano.+ Zimenezi zionekera ndipo anthu inu muzidziwa ndithu.+ M’chipululu, ine ndidzatsegulamo njira+ ndi mitsinje.+
20 Zilombo zakutchire zidzanditamanda.+ Mimbulu ndi nthiwatiwa+ zidzanditamanda chifukwa ndidzapereka madzi ndi mitsinje m’chipululu,+ kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe,
21 ndiponso kuti anthu amene ndinawapanga kuti akhale anga, anene za ulemerero wanga.+
22 “Koma iwe Yakobo, iwe Isiraeli, sunapemphe thandizo kwa ine+ chifukwa chakuti watopa nane.+
23 Iwe sunandibweretsere nkhosa zako zansembe zopsereza zathunthu. Sunandilemekeze ndi nsembe zako.+ Ine sindinakuumirize kuti uzindipatsa mphatso ndipo sindinakutopetse n’kukupempha lubani.*+
24 Iwe sunandigulire bango lonunkhira+ ndi ndalama iliyonse, ndipo sunandikhutitse ndi mafuta a nsembe zako.+ Koma m’malomwake, wandiumiriza ndi machimo ako kuti ndikutumikire. Wanditopetsa ndi zolakwa zako.+
25 “Ineyo ndi amene ndikufafaniza+ zolakwa zako,+ ndipo machimo ako sindidzawakumbukiranso.+
26 Tiye tikhale pa mlandu. Ndikumbutse.+ Fotokoza mbali yako kuti iweyo ukhale wosalakwa.+
27 Bambo wako, woyamba uja, anachimwa+ ndipo anthu okulankhulira andilakwira.+
28 Chotero ndidzadetsa akalonga a pamalo oyera. Yakobo ndidzamuwononga ndipo Isiraeli ndidzamunyozetsa.+