Yesaya 46:1-13
46 Beli+ wawerama+ ndipo Nebo wagwada. Mafano awo+ akhala katundu wa nyama zakutchire ndi wa nyama zoweta. Mafanowo angokhala katundu wolemera kwa nyama zotopa.
2 Milungu imeneyi idzawerama, ndipo yonse pamodzi idzagwada pansi. Singapulumutse zifaniziro zawo+ zimene zanyamulidwa ngati katundu, koma idzatengedwa kupita ku ukapolo.+
3 “Inu a nyumba ya Yakobo ndimvetsereni. Ndimvetsereni inu nonse otsala a m’nyumba ya Isiraeli,+ inu amene ndinakunyamulani kuyambira pamene munabadwa, ndiponso inu amene ndinakusamalirani kuyambira pamene munatuluka m’mimba.+
4 Ine sindisintha ngakhale kwa wokalamba,+ ndipo munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.+ Ndithu ineyo ndidzachitapo kanthu+ kuti ndiwatenge, ndiwanyamule ndi kuwapulumutsa.+
5 “Kodi anthu inu mungandifanizire ndi ndani,+ kapena mungandiyerekezere ndi ndani?+
6 Pali anthu amene amakhuthula golide m’zikwama, ndi kuyeza siliva pasikelo. Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo iye amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+ Kenako anthuwo amayamba kuweramira ndi kugwadira mulunguyo.+
7 Iwo amamunyamula pamapewa awo.+ Amamutenga n’kukamuika pamalo ake ndi kumuimika bwinobwino. Mulunguyo sayenda kuchoka pamalo akewo.+ Ngakhale munthu atamufuulira, iye sayankha. Sapulumutsa munthu kumavuto ake.+
8 “Anthu inu kumbukirani izi kuti mulimbe mtima. Muziganizire mumtima mwanu,+ inu anthu ochimwa.+
9 Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,+ kuti ine ndine Mulungu+ ndipo palibenso Mulungu wina,+ kapena aliyense wofanana ndi ine.+
10 Ine ndi amene ndimanena za mapeto kuyambira pa chiyambi.+ Kuyambira kalekale, ndimanena za zinthu zimene sizinachitike.+ Ine ndiye amene ndimanena kuti, ‘Zolingalira zanga zidzachitikadi,+ ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+
11 Ine ndi amene ndidzaitane mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa.+ Ndidzaitana munthu kuti adzachite zolingalira zanga kuchokera kutali.+ Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita.+ Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.+
12 “Tamverani inu anthu osamva,+ inu anthu amene muli kutali ndi chilungamo.+
13 Ine ndabweretsa pafupi chilungamo changa.+ Chilungamocho sichili kutali,+ ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa.+ Ndidzapereka chipulumutso mu Ziyoni, ndipo Isiraeli ndidzam’patsa kukongola kwanga.”+