Yesaya 49:1-26
49 Ndimvereni zilumba inu,+ ndipo mvetserani, inu mitundu ya anthu akutali.+ Yehova anandiitana+ ndili m’mimba.+ Ndili mkati mwa mayi anga, anatchula dzina langa.+
2 Iye anachititsa m’kamwa mwanga kukhala ngati lupanga lakuthwa.+ Anandibisa mumthunzi+ wa dzanja lake.+ Anandisandutsa muvi wonola bwino. Anandibisa m’kachikwama kake koikamo mivi.
3 Kenako anandiuza kuti: “Iwe Isiraeli ndiwe mtumiki wanga.+ Ine ndidzaonetsera kukongola kwanga pa iwe.”+
4 Koma ine ndinati: “Ndangovutika pachabe.+ Mphamvu zanga ndangoziwonongera zinthu zopanda pake ndi zachabechabe.+ Ndithu, Yehova ndiye amene adzandiweruze+ ndipo Mulungu wanga ndiye amene adzandipatse mphoto yanga.”+
5 Tsopano Yehova, amene anandipanga ndili m’mimba kuti ndikhale mtumiki wake,+ wanena kuti ndimubwezere Yakobo,+ n’cholinga choti Isiraeli asonkhanitsidwe kwa iye.+ Ine ndidzakhala wolemekezeka pamaso pa Yehova ndipo Mulungu wanga adzakhala mphamvu yanga.
6 Ndiyeno iye anati: “Si nkhani yochepa kuti iweyo wakhala mtumiki wanga, n’cholinga choti ubwezeretse mafuko a Yakobo ndi kubweza Aisiraeli amene ali otetezeka.+ Ndakupereka kuti ukhale kuwala kwa mitundu ya anthu,+ kuti chipulumutso changa chifike mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”+
7 Yehova, Wowombola Isiraeli,+ Woyera wake, wauza yemwe ananyozedwa kwambiri,+ yemwe amadedwa ndi mtundu wa anthu,+ mtumiki wa atsogoleri,+ kuti: “Mafumu adzaimirira chifukwa cha zimene adzaone,+ ndipo akalonga adzagwada chifukwa cha Yehova. Iye ndi wokhulupirika,+ Woyera wa Isiraeli, amene anakusankha.”+
8 Yehova wanena kuti: “Pa nthawi yapadera yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha.+ M’tsiku la chipulumutso, ndinakuthandiza.+ Ndinakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,+ kuti ndikonzenso dzikolo,+ kuti anthu ayambirenso kukhala m’cholowa chawo chimene chinali bwinja,+
9 kuti ndiuze akaidi+ kuti, ‘Tulukani!’+ ndi amene ali mu mdima+ kuti, ‘Dziululeni!’+ Iwo adzadya msipu m’mphepete mwa msewu, ndipo m’mphepete mwa njira zonse zodutsidwadutsidwa mudzakhala malo awo odyeramo msipu.+
10 Iwo sadzakhala ndi njala+ ndipo sadzamva ludzu.+ Sadzamva kutentha kapena kupsa ndi dzuwa.+ Pakuti yemwe amawamvera chisoni adzawatsogolera+ ndipo adzapita nawo ku akasupe amadzi.+
11 Ndidzachititsa kuti mapiri anga onse akhale njira, ndipo misewu yanga yonse idzakhala pamalo okwera.+
12 Taonani! Awa adzachokera kutali,+ ndipo awa adzachokera kumpoto+ ndi kumadzulo.+ Awanso adzachokera kudziko la Sinimu.”
13 Fuulani mokondwa kumwamba inu,+ ndipo sangalala iwe dziko lapansi.+ Mapiri asangalale ndipo afuule ndi chisangalalo.+ Pakuti Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo amamvera chisoni anthu ake osautsidwa.+
14 Koma Ziyoni ankangonena kuti: “Yehova wandisiya+ ndipo Yehova wandiiwala.”+
15 Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa, osamvera chisoni mwana wochokera m’mimba mwake?+ Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala,+ koma ine sindidzakuiwala.+
16 Taona! Ndakudinda m’manja mwanga.+ Makoma ako ali pamaso panga nthawi zonse.+
17 Ana ako abwera mofulumira. Anthu amene anali kukukhadzula ndi kukuwononga adzakuchokera.
18 Takweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse asonkhanitsidwa pamodzi.+ Abwera kwa iwe. Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,+ onsewo udzadzikongoletsa nawo ngati zokongoletsera, ndipo udzawavala ngati ndiwe mkwatibwi.+
19 Ngakhale kuti panopa malo ako ndi owonongeka, osakazidwa ndiponso abwinja,+ ngakhale kuti panopa malo ako ndi osatakasuka mokwanira kuti n’kukhalamo bwinobwino, ndipo okumeza akhala kutali,+
20 koma ana ako amene unabereka ana ena onse atamwalira,+ adzakuuza kuti, ‘Malowa atichepera.+ Tipezereni malo oti tikhalemo.’+
21 Iweyo udzanenadi mumtima mwako kuti, ‘Kodi bambo wa ana amene ndaberekawa ndani, popeza ine ndine mayi woferedwa ana ndiponso wosabereka, mayi yemwe anatengedwa kupita kudziko lina ku ukaidi?+ Nanga ana awa, anawalera ndani?+ Inetu ndinasiyidwa m’mbuyo ndekhandekha.+ Ndiyeno ana awa anali kuti?’”+
22 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Taona! Ineyo ndidzakwezera dzanja langa mitundu ya anthu,+ ndipo anthu a mitundu yosiyanasiyana ndidzawakwezera chizindikiro.+ Iwo adzakubweretsera ana ako aamuna atawanyamulira pachifuwa, ndipo ana ako aakazi adzawanyamulira paphewa.+
23 Mafumu adzakhala okusamalira,+ ndipo ana awo aakazi adzakhala okuyamwitsira ana ako. Iwo adzakugwadira mpaka nkhope zawo pansi+ ndipo adzanyambita fumbi la kumapazi ako.+ Pamenepo, ndithu iweyo udzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndiponso kuti anthu okhulupirira mwa ine sadzachita nane manyazi.”+
24 Kodi anthu amene atengedwa kale angalandidwe m’manja mwa munthu wamphamvu,+ kapena kodi gulu la anthu amene agwidwa ndi wolamulira wankhanza lingathawe?+
25 Koma Yehova wanena kuti: “Ngakhale gulu la anthu ogwidwa ndi munthu wamphamvu lidzatengedwa,+ ndipo amene anatengedwa kale ndi wolamulira wankhanza adzathawa.+ Aliyense wolimbana nawe, ineyo ndidzalimbana naye,+ ndipo ana ako ndidzawapulumutsa.+
26 Amene akukuzunza ndidzawachititsa kuti adye mnofu wawo womwe, ndipo adzaledzera ndi magazi awo omwe ngati kuti amwa vinyo wotsekemera. Anthu onse ndithu adzadziwa kuti ine, Yehova,+ ndine Mpulumutsi wako+ ndiponso Wokuwombola,+ Wamphamvu wa Yakobo.”+