Yesaya 56:1-12

56  Yehova wanena kuti: “Anthu inu, tsatirani chilungamo+ ndipo chitani zolungama.+ Pakuti chipulumutso changa chatsala pang’ono kubwera,+ ndipo chilungamo changa chatsala pang’ono kuonekera.+  Wodala ndi munthu amene amachita zimenezi,+ ndiponso mwana wa munthu amene amatsatira zimenezi,+ amene amasunga sabata kuti asalidetse,+ ndiponso amaletsa dzanja lake kuti lisachite choipa chilichonse.+  Mlendo yemwe wadziphatika kwa Yehova asanene kuti,+ ‘Ndithu Yehova adzandilekanitsa ndi anthu ake.’+ Nayenso munthu wofulidwa+ asanene kuti, ‘Ine ndiye ndine mtengo wouma basi.’”  Pakuti Yehova wanena kuti: “Anthu ofulidwa amene amasunga sabata langa, ndiponso amene asankha kuchita zimene ndimasangalala nazo,+ komanso amene amatsatira pangano langa,+  m’nyumba mwanga+ ndiponso mkati mwa makoma anga ndidzawapatsa chipilala chachikumbutso+ ndiponso dzina,+ zomwe ndi zabwino kuposa ana aamuna ndi aakazi.+ Ndidzawapatsa dzina limene silidzatha+ mpaka kalekale.+  “Alendo amene adziphatika kwa Yehova kuti am’tumikire+ ndiponso amene amakonda dzina la Yehova+ n’cholinga choti akhale atumiki ake, onse amene amasunga sabata kuti asalidetse ndiponso amene amatsatira pangano langa,+  ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+ ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo.+ Nsembe zawo zopsereza zathunthu+ ndi nsembe zawo zina+ ndidzazilandira paguwa langa lansembe.+ Pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+  Mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, amene akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli omwe anabalalitsidwa,+ ndi akuti: “Ine ndidzamusonkhanitsiranso anthu ena kuwonjezera pa anthu ake amene anasonkhanitsidwa kale.”+  Inu nyama zonse zakutchire, inu nyama zonse za m’nkhalango, bwerani mudzadye.+ 10  Alonda ake ndi akhungu+ ndipo sakudziwa chilichonse.+ Onsewo ndi agalu opanda mawu. Satha kuuwa.+ Amangokhalira kupuma wefuwefu ndi kugona pansi. Amakonda kugona tulo.+ 11  Iwo ndi agalu adyera kwambiri+ ndipo sakhuta,+ komanso ndi abusa osamvetsa zinthu.+ Aliyense wa iwo wapatukira kunjira yake n’cholinga chopeza phindu lachinyengo lochokera m’dera lake.+ Iwo amati: 12  “Tabwerani amuna inu! Dikirani kaye ndikatenge vinyo. Timwe mpaka kuledzera.+ Mawa lidzakhalanso ngati lero, mwinanso kuposa pamenepa.”+

Mawu a M'munsi