Yesaya 58:1-14
58 “Fuula mwamphamvu! Usabweze mawu.+ Kweza mawu ako ngati lipenga,+ ndipo uza anthu anga za kupanduka kwawo. A nyumba ya Yakobo uwauze machimo awo.
2 Koma tsiku ndi tsiku iwo anali kufunafuna ineyo. Anali kunena kuti amasangalala kudziwa njira zanga,+ ngati mtundu umene unali kuchita zolungama ndiponso ngati mtundu umene sunasiye chilungamo cha Mulungu wawo.+ Iwo ankangokhalira kundipempha chiweruzo cholungama, ndipo anali kuyandikira kwa Mulungu amene anali kumukonda.+
3 Tsopano iwo akunena kuti: “‘Kodi ifeyo tinavutikiranji kusala kudya inu osaona,+ ndipo tinadzisautsiranji+ inu osasamala n’komwe?’+
“Komatu anthu inu munali kusangalala tsiku limene munali kusala kudya, pamene antchito anu onse munali kuwagwiritsa ntchito yakalavulagaga.+
4 Ndithu inuyo munali kusala kudya n’cholinga choti muzikangana, kulimbana,+ ndiponso kuti muzimenyana ndi nkhonya zovulaza.+ Kodi inuyo simunali kusala kudya n’kumaganiza kuti inali nthawi yoti mawu anu amveke kumwamba?
5 Kodi kusala kudya kumene ine ndasankha kukhale kotere? Kodi likhale tsiku loti munthu wochokera kufumbi azisautsa moyo wake?+ Kodi likhale tsiku loti munthu aziweramitsa mutu wake ngati udzu, ndiponso loti aziyala chiguduli ngati bedi lake n’kuwazapo phulusa?+ Kodi limeneli ndi limene mumalitcha tsiku losala kudya ndi lovomerezeka kwa Yehova?+
6 “Kusala kudya kumene ine ndimafuna n’kotere: Mumasule maunyolo ozunzira anzanu,+ mumasule zingwe za goli,+ mumasule anthu opsinjika kuti azipita kwawo,+ ndipo goli lililonse mulithyole pakati.+
7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+ ndiponso kuti muziitanira m’nyumba zanu anthu osautsika ndi osowa pokhala.+ Ndimafuna kuti mukaona munthu wosavala muzimuveka+ ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.+
8 “Mukatero kuwala kwanu kudzaonekera ngati m’bandakucha,+ ndipo mudzachira mofulumira kwambiri.+ Chilungamo chanu chizidzayenda patsogolo panu,+ ndipo ulemerero wa Yehova uzidzalondera kumbuyo kwanu.+
9 Chotero inu mudzaitana ndipo Yehova adzakuyankhani. Mudzafuula popempha+ ndipo iye adzayankha kuti, ‘Ndikumva lankhulani!’
“Mukachotsa goli pakati panu,+ mukaleka kutosana chala+ ndi kulankhulana zopweteka,+
10 mukapatsa munthu wanjala zinthu zimene inuyo mumakonda,+ ndiponso mukakhutiritsa munthu amene akusautsidwa, kuunika kwanu kudzawala kuti ngwee! mu mdima, ndipo mdima wanu udzakhala ngati masana dzuwa likakhala paliwombo.+
11 Yehova azidzakutsogolerani+ nthawi zonse+ ndipo adzakukhutiritsani ngakhale m’dziko louma.+ Iye adzatsitsimula mafupa anu+ ndipo inu mudzakhala ngati munda wachinyontho chokwanira bwino,+ ndiponso ngati kasupe wamadzi yemwe madzi ake sanama.
12 Chifukwa cha inu, anthu adzamanga malo amene anawonongedwa kalekale.+ Inu mudzamanganso maziko amene akhalapo ku mibadwomibadwo.+ Mudzatchedwa otseka mipata ya mpanda,+ ndiponso okonzanso misewu yomwe anthu amakhala m’mphepete mwake.
13 “Mukabweza phazi lanu chifukwa cha sabata, kuti musiye kuchita zokonda zanu pa tsiku langa lopatulika,+ sabatalo mukalitcha tsiku losangalatsa kwambiri, tsiku lopatulika ndi lolemekezeka la Yehova,+ ndipo mukalilemekeza m’malo moyenda njira zanu, m’malo mopeza zinthu zosangalatsa inuyo, ndiponso m’malo molankhula zopanda pake,
14 pamenepo mudzasangalala kwambiri mwa Yehova.+ Ine ndidzakuchititsani kuti mukwere m’malo okwezeka a dziko lapansi,+ ndipo ndidzakuchititsani kuti mudye zochokera m’cholowa cha Yakobo kholo lanu,+ pakuti pakamwa pa Yehova panena zimenezi.”+