Yesaya 60:1-22
60 “Imirira+ mkazi iwe! Onetsa kuwala kwako,+ pakuti kuwala kwako kwafika,+ ndipo ulemerero wa Yehova wakuunika.+
2 Taona! Mdima+ udzaphimba dziko lapansi, ndipo mdima wandiweyani udzaphimba mitundu ya anthu. Koma kuwala kwa Yehova kudzafika pa iwe, ndipo ulemerero wake udzaonekera pa iwe.+
3 Mitundu ya anthu idzatsata kuwala kwako,+ ndipo mafumu+ adzatsata kunyezimira kwako.+
4 “Takweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira. Onse asonkhanitsidwa pamodzi.+ Abwera kwa iwe.+ Kuchokera kutali, ana ako aamuna akubwera limodzi ndi ana ako aakazi, amene adzasamalidwe atanyamulidwa m’manja.+
5 Pa nthawi imeneyo, nkhope yako idzasangalala ukadzaona zimenezi.+ Mtima wako udzanthunthumira ndi kufutukuka, chifukwa chuma cha m’nyanja chidzabwera kwa iwe. Katundu wa mitundu ya anthu adzabwera kwa iwe.+
6 Chikhamu cha ngamila zamphongo zing’onozing’ono za ku Midiyani ndi ku Efa+ chidzadzaza dziko lako. Anthu onse a ku Sheba+ adzabwera atanyamula golide ndi lubani. Iwo adzatamanda Yehova pamaso pa anthu onse.+
7 Nkhosa zonse za ku Kedara+ zidzasonkhanitsidwa kwa iwe. Nkhosa zamphongo za ku Nebayoti+ zidzakutumikira.+ Ine ndidzazilandira paguwa langa lansembe,+ ndipo ndidzakongoletsa nyumba yanga yokongola.+
8 “Kodi amene akubwera chouluka ngati mtambowa ndani?+ Ndani awa akubwera ngati nkhunda zimene zikuulukira kumakomo a makola awo?
9 Pakuti zilumba zidzayembekezera ine.+ Nazonso zombo za ku Tarisi+ zidzayembekezera ine ngati poyamba paja, kuti zikubweretsere ana ako aamuna kuchokera kutali.+ Iwo adzabwera atanyamula siliva ndi golide wawo,+ kuti alemekeze dzina+ la Yehova Mulungu wako ndi Woyera wa Isiraeli,+ pakuti iye adzakhala atakukongoletsa.+
10 Alendo adzamanga mipanda yako,+ ndipo mafumu awo adzakutumikira.+ Ine ndinakulanga mu mkwiyo wanga,+ koma chifukwa cha kukoma mtima kwanga ndidzakuchitira chifundo.+
11 “Zipata zako zidzakhala zotsegula nthawi zonse.+ Sizidzatsekedwa usana ndi usiku kuti chuma cha mitundu ya anthu chibwere kwa iwe,+ ndipo mafumu awo ndiwo adzakhale patsogolo pochita zimenezi.+
12 Pakuti mtundu uliwonse ndi ufumu uliwonse umene sudzakutumikira udzawonongedwa, ndipo mitundu ya anthu idzasakazidwa ndithu.+
13 “Ulemerero wa Lebanoni udzabwera kwa iwe. Mtengo wofanana ndi mkungudza, mtengo wa ashi, ndiponso mtengo wa paini zidzabwera pa nthawi imodzi,+ kuti zikongoletse malo anga opatulika,+ ndipo ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.+
14 “Ana a anthu okusautsa adzabwera kwa iwe atawerama.+ Onse amene anali kukuchitira chipongwe adzagwada pamapazi ako,+ ndipo adzakutcha mzinda wa Yehova, Ziyoni+ wa Woyera wa Isiraeli.
15 “M’malo mokhala wosiyidwa mpaka kalekale ndi wodedwa, popanda aliyense wodutsa mwa iwe,+ ine ndidzakuika monga chinthu chonyaditsa mpaka kalekale, ndiponso chinthu chokondweretsa ku mibadwomibadwo.+
16 Iwe udzayamwa mkaka wa mitundu ya anthu,+ ndipo udzayamwa bere la mafumu.+ Udzadziwadi kuti ine Yehova+ ndine Mpulumutsi wako,+ ndipo Wamphamvu+ wa Yakobo ndiye Wokuwombola.+
17 M’malo mwa mkuwa, ndidzabweretsa golide.+ M’malo mwa chitsulo, ndidzabweretsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweretsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweretsa chitsulo. Ndidzaika mtendere kuti ukhale ngati wokuyang’anira,+ ndi chilungamo kuti chikhale ngati wokupatsa ntchito.+
18 “M’dziko lako simudzamvekanso zachiwawa. Mkati mwa malire ako simudzakhalanso kusakaza kapena kuwononga.+ Mipanda yako udzaitcha Chipulumutso+ ndipo zipata zako udzazitcha Chitamando.
19 Dzuwa silidzakhalanso lokuunikira masana, ndipo mwezi sudzakuunikiranso. Kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale,+ ndipo Mulungu wako adzakhala kukongola kwako.+
20 Dzuwa lako silidzalowanso, ndipo mwezi wako sudzapitanso kumdima. Pakuti kwa iwe, Yehova adzakhala kuwala kosatha mpaka kalekale,+ ndipo masiku ako olira adzakhala atatha.+
21 Anthu ako onse adzakhala olungama.+ Iwo adzakhala m’dzikomo mpaka kalekale.+ Anthuwo adzakhala mmera wobzalidwa ndi ine+ ndiponso ntchito ya manja anga,+ kuti ineyo ndikongoletsedwe.+
22 Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.+ Ineyo Yehova ndidzafulumizitsa zimenezi pa nthawi yake.”+