Yesaya 63:1-19
63 Kodi amene akuchokera ku Edomuyu+ ndi ndani, amene akuchokera ku Bozira+ atavala zovala zowala zamitundumitundu, amene zovala zake ndi zolemekezeka, ndiponso amene akuyenda mwamphamvu chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake?
“Ndi ine, amene ndimalankhula mwachilungamo,+ amene ndili ndi mphamvu zambiri zopulumutsa.”+
2 N’chifukwa chiyani zovala zanu zili zofiira, ndipo n’chifukwa chiyani zovala zimene mwavala zikuoneka ngati za munthu woponda mphesa m’choponderamo mphesa?+
3 “Moponderamo mphesa ndapondapondamo ndekha,+ chifukwa palibe munthu amene anali nane wochokera pakati pa mitundu ya anthu. Iwo ndawapondaponda mu mkwiyo wanga,+ ndipo ndawapondereza mu ukali wanga.+ Magazi awo awazikira pazovala zanga,+ ndipo ndaipitsa zovala zanga zonse.
4 Pakuti tsiku lobwezera lili mumtima mwanga,+ ndipo chaka choti anthu anga awomboledwe chafika.
5 Ndinayang’anayang’ana, koma panalibe wondithandiza. Ndinayamba kudabwa, koma panalibe woti angandichirikize.+ Choncho ndinabweretsa chipulumutso ndi dzanja langa,+ ndipo ukali wanga+ ndi umene unandichirikiza.
6 Ndinapondaponda mitundu ya anthu mu mkwiyo wanga, ndipo ndinawaledzeretsa ndi ukali wanga.+ Ndinachititsa kuti magazi awo atuluke mwamphamvu n’kutayikira pansi.”+
7 Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+ Ndidzatamanda Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehova watichitira.+ Ndidzauza nyumba ya Isiraeli zabwino zochuluka+ zimene iye wawachitira chifukwa cha chifundo chake,+ komanso chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha ndiponso kwakukulu.
8 Iye anati: “Ndithu awa ndi anthu anga,+ ana amene sadzachita zachinyengo.”+ Choncho iye anakhala Mpulumutsi wawo.+
9 Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.+ Mthenga amene iye anawatumizira, anawapulumutsa.+ Chifukwa cha chikondi chake ndi chisoni chake, iye anawawombola.+ Anawakweza m’mwamba ndi kuwanyamula masiku onse akale.+
10 Koma iwo anapanduka+ ndi kukhumudwitsa mzimu wake woyera.+ Chotero iye anasintha n’kukhala mdani+ wawo ndipo anachita nawo nkhondo.+
11 Iwo anayamba kukumbukira masiku akale, masiku a Mose mtumiki wake, ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa m’nyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake uja, ali kuti?+ Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+
12 Ali kuti amene anachititsa mkono wake wokongola+ kupita kudzanja lamanja la Mose, amene anagawanitsa madzi pamaso pawo+ kuti adzipangire dzina lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+
13 amene anawawolotsa pamadzi amphamvu moti sanapunthwe, mofanana ndi hatchi m’chipululu?+
14 Monga momwe chilombo chakutchire chimatsetserekera kuchigwa, mzimu wa Yehova unawapumitsa.”+
Chotero inu munatsogolera anthu anu kuti mudzipangire dzina lokongola.+
15 Yang’anani muli kumwamba,+ ndipo muone kuchokera pamalo anu okhala apamwamba, oyera ndi okongola.+ Kodi mtima wanu wodzipereka kwambiri+ ndiponso mphamvu zanu zonse zili kuti? Kodi kubwadamuka kwa m’mimba mwanu+ ndi chifundo+ chanu zili kuti? Inuyo mwaleka kundichitira zimenezi.+
16 Inutu ndinu Atate wathu.+ Ngakhale kuti Abulahamu sanatidziwe ndipo Isiraeli sanatizindikire, inuyo Yehova ndinu Atate wathu. Dzina lanu ndinu Wotiwombola wakalekale.+
17 N’chifukwa chiyani inu Yehova mukutichititsa kuchoka panjira zanu? N’chifukwa chiyani mukuumitsa mtima wathu kuti tisakuopeni?+ Bwererani chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.+
18 Kwa kanthawi kochepa, anthu anu oyera+ anali ndi zinthu. Koma adani athu apondaponda malo anu opatulika.+
19 Kwanthawi yaitali, takhala ngati anthu amene simunawalamulirepo, ngati anthu amene sanatchedwepo ndi dzina lanu.+