Yesaya 65:1-25
65 “Ine ndalola kuti anthu amene sanafunse za ine+ andifunefune.+ Ndalola kuti anthu amene sanandifunefune andipeze.+ Ndanena kuti, ‘Ndili pano, ndili pano!’+ kwa mtundu umene sunaitane pa dzina langa.+
2 “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,*+ amene akuyenda m’njira yoipa+ potsatira maganizo awo,+
3 anthu amene akundichitira mwano+ nthawi zonse m’maso muli gwa! Amene amapereka nsembe m’minda,+ amene amafukiza nsembe zautsi+ panjerwa,
4 amene amakhala pansi kumanda,+ amene amakhala usiku wonse m’tinyumba ta alonda, amene amadya nyama ya nkhumba,+ ndipo m’miphika mwawo muli msuzi wa zinthu zodetsedwa.+
5 Iwo amanena kuti, ‘Khala pawekha. Usandiyandikire, kuti ndingakupatsire chiyero changa.’+ Iwo ali ngati utsi m’mphuno mwanga,+ ngati moto woyaka tsiku lonse.+
6 “Taonani! Zalembedwa pamaso panga.+ Ine sindidzakhala chete,+ koma ndidzapereka mphoto.+ Mphotoyo ndidzaiika pachifuwa pawo,+
7 chifukwa cha zolakwa zawo ndi zolakwa za makolo awo pa nthawi imodzi,”+ watero Yehova. “Popeza afukiza nsembe zautsi pamapiri ndipo andinyoza+ pazitunda,+ ine ndidzawayezera mphoto yawo choyamba, n’kuiika pachifuwa pawo.”+
8 Yehova wanena kuti: “Monga momwe vinyo watsopano+ amapezekera m’tsango la mphesa ndipo wina amanena kuti, ‘Musaliwononge,+ pakuti muli dalitso mmenemu,’+ inenso ndidzachita zomwezo chifukwa cha atumiki anga, kuti ndisawawononge onse.+
9 Mwa Yakobo ndidzatulutsamo mwana,+ ndipo mwa Yuda ndidzatulutsamo yemwe adzalandire cholowa cha mapiri anga.+ Anthu anga osankhidwa mwapadera adzapatsidwa dziko lamapirilo,+ ndipo atumiki anga adzakhala mmenemo.+
10 Sharoni+ adzakhala malo odyetserapo nkhosa.+ Chigwa cha Akori+ chidzakhala malo opumulirapo ng’ombe za anthu anga amene andifunafuna.+
11 “Koma anthu inu mwamusiya Yehova.+ Mwaiwala phiri langa loyera.+ Inu mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi.+ Mumadzaza chikho ndi vinyo wosakaniza n’kupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.+
12 Choncho ine ndidzakonzeratu zoti anthu inu mudzaphedwe ndi lupanga.+ Nonsenu mudzawerama kuti akupheni,+ popeza ndinakuitanani+ koma simunayankhe. Ndinalankhula koma simunamvere.+ Munapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga+ ndipo munasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”+
13 Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Atumiki anga adzadya,+ koma inuyo mudzakhala ndi njala.+ Atumiki anga adzamwa,+ koma inuyo mudzakhala ndi ludzu.+ Atumiki anga adzasangalala,+ koma inuyo mudzachita manyazi.+
14 Atumiki anga adzafuula mokondwa chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima,+ koma inuyo mudzalira chifukwa chopwetekedwa mtima ndipo mudzafuula chifukwa chosweka mtima.+
15 Anthu inu mudzasiya dzina lanu kuti anthu anga osankhidwa mwapadera aziligwiritsa ntchito potemberera ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzakuphani mmodzi ndi mmodzi,+ koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.+
16 Chotero aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi adzadalitsidwa ndi Mulungu wokhulupirika.+ Aliyense wolumbira padziko lapansi adzalumbira pa Mulungu wokhulupirika,+ chifukwa masautso akale adzaiwalika ndipo sadzaonedwanso ndi maso anga.+
17 “Pakuti ndikulenga kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano.+ Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso+ ndipo sizidzabweranso mumtima.+
18 Koma kondwerani anthu inu,+ ndipo sangalalani kwamuyaya ndi zimene ndikulenga.+ Pakuti ndikulenga Yerusalemu kuti akhale chinthu chosangalatsa ndipo anthu ake akhale chinthu chokondweretsa.+
19 Ndidzasangalala ndi Yerusalemu ndipo ndidzakondwera ndi anthu anga.+ Mwa iye simudzamvekanso kulira kokweza mawu kapena kulira kwachisoni.”+
20 “Kumeneko sikudzakhalanso mwana woyamwa wongokhala ndi moyo masiku ochepa okha,+ kapena nkhalamba imene sidzakwanitsa masiku ake.+ Pakuti ngakhale munthu womwalira ali ndi zaka 100 adzaoneka ngati kamnyamata, ndipo wochimwa, ngakhale ali ndi zaka 100, temberero lidzamugwera.+
21 Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo.+ Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.+
22 Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo,+ ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.+
23 Sadzagwira ntchito pachabe+ komanso sadzaberekera tsoka,+ chifukwa iwo ndiponso ana awo+ ndi odalitsidwa ndi Yehova.+
24 Iwo asanandiitane, ine ndidzayankha.+ Asanamalize kulankhula, ine ndidzamva.+
25 “Mmbulu+ ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi.+ Mkango udzadya udzu ngati ng’ombe yamphongo,+ ndipo njoka izidzadya fumbi.+ Zimenezi sizidzapweteka aliyense+ kapena kuwononga chilichonse m’phiri langa lonse loyera,”+ watero Yehova.
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “anthota.”