Yesaya 66:1-24

66  Yehova wanena kuti: “Kumwamba ndiko mpando wanga wachifumu,+ ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.+ Kodi anthu inu mungandimangire nyumba yotani?+ Ndipo malo oti ine ndingapumulirepo, ali kuti?”+  “Zinthu zonsezi ndinazipanga ndi dzanja langa, choncho zinakhalapo,”+ akutero Yehova. “Ine ndidzayang’ana munthu amene ali wosautsidwa, wosweka mtima,+ ndiponso wonjenjemera ndi mawu anga.+  “Munthu amene akupha ng’ombe yamphongo ali ngati wopha munthu.+ Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati wothyola khosi la galu.+ Wopereka mphatso ali ngati wopereka magazi a nkhumba.+ Wopereka lubani wachikumbutso+ ali ngati wopereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga.+ Anthuwo asankha njira zawozawo, ndipo amasangalala ndi zinthu zawo zonyansa.+  Ineyo ndidzasankha njira zowazunzira.+ Ndidzawabweretsera zinthu zimene amachita nazo mantha+ chifukwa ndinaitana koma palibe amene anayankha. Ndinalankhula koma palibe amene anamvera.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga ndipo anasankha zinthu zimene sindisangalala nazo.”+  Inu amene mukunjenjemera ndi mawu ake, imvani mawu a Yehova:+ “Abale anu amene akudana nanu,+ amene akukusalani chifukwa cha dzina langa,+ anati, ‘Alemekezeke Yehova!’+ Mulungu adzaonekera ndipo inu mudzasangalala,+ koma iwowo ndi amene adzachite manyazi.”+  Mumzinda mukumveka phokoso lachisokonezo, phokoso lochokera kukachisi.+ Limeneli ndi phokoso losonyeza kuti Yehova akubwezera adani ake chilango chowayenerera.+  Mkazi anabereka asanayambe kumva zowawa za pobereka.+ Ululu wa pobereka usanamubwerere, iye anabereka mwana wamwamuna.+  Ndani anamvapo zinthu ngati zimenezi?+ Ndani anaonapo zinthu zoterezi?+ Kodi dziko+ limatulutsidwa ndi zowawa za pobereka tsiku limodzi lokha?+ Kapena kodi mtundu+ umabadwa nthawi imodzi?+ Pakuti Ziyoni wamva zowawa za pobereka ndipo wabereka ana ake aamuna.  “Kodi ine ndingachititse kuti chiberekero chitseguke koma osachititsa kuti mwana abadwe?”+ akutero Yehova. “Kapena kodi ndingachititse kuti mwana atsale pang’ono kubadwa kenako n’kutseka chiberekero?” watero Mulungu wanu. 10  Sangalalani ndi Yerusalemu ndipo kondwerani naye,+ inu nonse omukonda.+ Kondwerani naye kwambiri, inu nonse amene mukumulirira,+ 11  chifukwa mudzayamwa bere lake ndipo mudzakhuta kutonthoza kwake. Komanso mudzayamwa mkaka wake ndipo mudzasangalala kwambiri ndi bere lake laulemerero.+ 12  Pakuti Yehova wanena kuti: “Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje+ ndi ulemerero wa mitundu ya anthu ngati mtsinje wosefukira,+ ndipo inu mudzayamwadi.+ Adzakunyamulani m’manja ndipo adzakusisitani mwachikondi atakuikani pamwendo.+ 13  Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu,+ ndipo mudzatonthozedwa chifukwa cha Yerusalemu.+ 14  Mudzaona zimenezi ndipo mtima wanu udzasangalala.+ Mafupa anu+ adzakhala ndi mphamvu ngati udzu wobiriwira.+ Dzanja la Yehova lidzadziwika kwa atumiki ake,+ koma iye adzakwiyira adani ake.”+ 15  “Pakuti Yehova akubwera ngati moto,+ ndipo magaleta ake ali ngati mphepo yamkuntho+ kuti adzawabwezere mwaukali ndi mokwiya, ndiponso kuti adzawadzudzule ndi malawi a moto.+ 16  Pakuti ngati moto woyaka, Yehova adzaweruza anthu onse ndi lupanga lake,+ ndipo anthu ophedwa ndi Yehova adzakhala ambiri.+ 17  Anthu amene akudzipatula ndi kudziyeretsa kuti apite kuminda+ n’kukaima kuseri kwa fano limene lili pakati pa mundawo, amene akudya nyama ya nkhumba+ ndi chinthu chonyansa, amene akudya ngakhale makoswe,+ onsewo adzathera limodzi,” akutero Yehova. 18  “Popeza ndikudziwa ntchito zawo+ ndi maganizo awo,+ ine ndikubwera kudzasonkhanitsa pamodzi mitundu yonse ndi zilankhulo zonse za anthu,+ ndipo iwo adzabwera n’kuona ulemerero wanga.”+ 19  “Ndidzachita zinthu zazikulu pakati pawo monga chizindikiro.+ Opulumuka ena ndidzawatumiza ku mitundu ya anthu,+ ku Tarisi,+ ku Puli, ndi ku Ludi.+ Ndidzawatumiza kwa anthu odziwa kukoka uta ku Tubala ndi ku Yavani.+ Ndidzawatumiza kuzilumba zakutali,+ kwa anthu amene sanamve mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga.+ Iwo adzanenadi za ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu.+ 20  Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse+ monga mphatso kwa Yehova.+ Adzayenda pamahatchi, pangolo, pangolo zotseka pamwamba, panyulu,* ndi pangamila zazikazi zothamanga,+ popita kuphiri langa loyera,+ ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene ana a Isiraeli amabweretsera mphatso m’nyumba ya Yehova, ataiika m’chiwiya choyera,”+ watero Yehova. 21  “Pakati pawo ndidzatengapo anthu ena kuti akhale ansembe ndi Alevi,” watero Yehova. 22  “Pakuti monga momwe kumwamba kwatsopano+ ndi dziko lapansi latsopano+ zimene ndikupanga zidzakhalirebe pamaso panga,+ momwemonso ana anu+ ndi dzina lanu zidzakhalapo mpaka kalekale,”+ akutero Yehova. 23  “Kuyambira mwezi watsopano mpaka mwezi wina watsopano, ndiponso sabata ndi sabata, anthu onse adzabwera kudzagwada pamaso panga,”+ watero Yehova. 24  “Iwo adzapita kukaona mitembo ya anthu amene anali kuphwanya malamulo anga,+ pakuti mphutsi zodya mitemboyo sizidzafa. Moto woinyeketsa sudzazima+ ndipo idzakhala chinthu chonyansa kwa anthu onse.”+

Mawu a M'munsi

Imeneyi ndi nyama yooneka ngati hatchi.