Yobu 1:1-22
1 Kudziko la Uzi+ kunali munthu wina dzina lake Yobu.+ Iye anali munthu wopanda cholakwa,+ wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndiponso wopewa zoipa.+
2 Yobu anali ndi ana aamuna 7, ndi ana aakazi atatu.+
3 Iye anali ndi ziweto+ izi: Nkhosa 7,000, ngamila 3,000, ng’ombe 1,000 zomwe zinali kugwira ntchito zili ziwiriziwiri, ndi abulu aakazi 500. Analinso ndi antchito ochuluka zedi, ndipo iye anali munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kum’mawa.+
4 Ana ake aamuna anali kuchita phwando+ kunyumba ya aliyense wa iwo, tsiku lina kwa wina, tsiku lina kwa wina, ndipo anali kuitana alongo awo atatu kuti adzadye ndi kumwera limodzi.
5 Akamaliza kuchita maphwando kunyumba zawo zonse, Yobu anali kutumiza uthenga n’kuwauza kuti adziyeretse.+ Kenako iye anali kudzuka m’mawa kwambiri n’kupereka nsembe zopsereza+ mogwirizana ndi chiwerengero cha ana ake onse, popeza iye ankati, “mwina ana anga achimwa ndipo anyoza+ Mulungu mumtima mwawo.”+ Umu ndi mmene Yobu anali kuchitira nthawi zonse.+
6 Tsopano linafika tsiku limene ana a Mulungu woona+ ankapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo ngakhalenso Satana+ anapita nawo limodzi.+
7 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anamuyankha Yehova kuti: “Ndinali kuzungulirazungulira m’dziko lapansi+ ndi kuyendayendamo.”+
8 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu, poti palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi?+ Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa+ ndi wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndi wopewa zoipa.”+
9 Pamenepo Satana anamuyankha Yehova kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pachabe?+
10 Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo?+ Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho. Mwadalitsa ntchito ya manja ake+ ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri padziko lapansi.
11 Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”+
12 Choncho Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, chilichonse chimene ali nacho chikhale m’manja mwako. Koma iyeyo usam’tambasulire dzanja lako ndi kum’khudza.” Pamenepo Satana anachoka pamaso pa Yehova.+
13 Tsopano linafika tsiku limene ana a Yobu, aamuna ndi aakazi, anali kudya ndi kumwa vinyo m’nyumba ya m’bale* wawo woyamba kubadwa.+
14 Kenako kunabwera munthu+ kwa Yobu kudzanena uthenga wakuti: “Ng’ombe zinali kulima+ ndipo abulu aakazi anali kudya msipu chapambali pake.
15 Ndiyeno kunabwera Asabeya+ omwe alanda ziwetozo n’kupha abusa ake ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”+
16 Uyu ali mkati molankhula kunabwera munthu wina kudzanena kuti: “Moto wa Mulungu watsika kuchokera kumwamba,+ ndipo wayaka pakati pa nkhosa ndi abusa n’kupsereza nkhosazo ndi abusawo. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”
17 Ameneyu ali mkati molankhula kunabwera munthu wina kudzanena kuti: “Kunabwera magulu atatu a Akasidi+ omwe anafika mwaliwiro kwambiri, n’kulanda ngamila ndi kupha abusa ake ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”
18 Ameneyu ali mkati molankhula kunabwera munthu winanso kudzanena kuti: “Ana anu aamuna ndi aakazi anali kudya ndi kumwa vinyo+ m’nyumba ya m’bale wawo woyamba kubadwa.
19 Kenako kunabwera chimphepo+ kuchokera kudera la kuchipululu chomwe chinawomba makona anayi a nyumbayo, ndipo nyumbayo yagwera anawo n’kuwapha. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka kuti ndidzakuuzeni.”
20 Yobu atamva zimenezi anaimirira n’kung’amba+ malaya ake akunja odula manja. Anametanso tsitsi+ kumutu kwake, kenako anagwada pansi+ n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi,+
21 n’kuyamba kunena kuti:“Ndinatuluka m’mimba mwa mayi anga ndili wamaliseche,+Ndipo ndidzabwerera mmenemo ndilinso wamaliseche.+Yehova wapereka,+ ndipo Yehova yemweyo watenga.+Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.”+
22 M’zonsezi Yobu sanachimwe, kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti “mchimwene.”