Yobu 10:1-22

10  “Ineyo ndikunyansidwa ndi moyo wanga.+Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga.Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.   Ndimuuza Mulungu kuti, ‘Musanene kuti ndine woipa.Ndiuzeni chifukwa chimene mukulimbanirana nane.   Kodi ndi bwino kuti inuyo muchite zoipa,+Kuti mukane chinthu chimene manja anu anagwira ntchito mwamphamvu pochipanga,+Ndiponso kuti muvomereze malangizo a anthu oipa?   Kodi maso anu+ ali ngati a munthu,Kapena kodi mumaona ngati mmene munthu amaonera?+   Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu,+Kapena kodi zaka zanu zili ngati masiku a mwamuna wamphamvu,   Kuti muyese kupeza cholakwa changa,Ndi kuti muzifunafuna tchimo langa?+   Chonsecho mukudziwa kuti ndine wosalakwa,+Ndipo palibe wondipulumutsa m’manja mwanu.+   Manja anu omwe ndi amene anandiumba, ndipo anandipanga+Kuzungulira thupi langa lonse, koma tsopano mukufuna kundimeza.   Chonde kumbukirani kuti munandiumba ndi dongo,+Ndipo mudzandibwezera kufumbi.+ 10  Kodi simunandikhuthule ngati mkakaNdi kundisefa ngati mkaka wosasa?+ 11  Munandiveka khungu ndiponso mnofu,Ndipo munandiluka ndi mafupa ndi mitsempha.+ 12  Mwandipatsa moyo ndi kundisonyeza kukoma mtima kosatha,+Ndipo mwa kundisamalira+ mumateteza moyo wanga. 13  Zinthu zimenezi mwazibisa mumtima mwanu.Ndikudziwa bwino kuti zinthu zimenezi zili ndi inu. 14  Ngati ndachimwa ndipo inu mwaona zonsezo,+Ndiponso simunandikhululukire zolakwa zanga,+ 15  Ngati ndine wolakwa, tsoka kwa ine!+Ngati ndine wosalakwa, ndisadzutse mutu wanga.+Ndachita manyazi kwambiri ndipo ndadzazidwa ndi mavuto.+ 16  Mutu wanga ukadzikweza,+ mudzandisaka ngati kuti ndinu mkango wamphamvu,+Ndipo mudzandichitira chinthu chinanso chodabwitsa. 17  Mudzabweretsa mboni zanu zatsopano pamaso panga,Ndipo mudzakulitsa mkwiyo wanu pa ine.Mavuto anga akungotsatizanatsatizana. 18  Kodi munanditulutsiranji m’mimba?+Zikanakhala bwino ndikanafa kuti diso ndi limodzi lomwe lisandione. 19  Bwenzi nditakhala ngati sindinakhaleko.Ndikanangochokera m’mimba n’kupita kumanda.’ 20  Kodi masiku anga si paja ndi ochepa?+ Iye andisiye,Asiye kundiyang’anitsitsa kuti ndisangalaleko+ pang’ono 21  Ndisanapite. Ndikapita sindibweranso,+Ndikapita kudziko lamdima wandiweyani,+ 22  Kudziko lopanda kuwala, lamdima wandiweyaniNdi lachisokonezo, losaona kuwala mofanana ndi malo amdima.”

Mawu a M'munsi