Yobu 12:1-25
12 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Zoonadi, amuna inu ndinu anthu,Ndipo nzeru zidzathera limodzi ndi inu.+
3 Inenso ndili ndi zolinga zabwino+ ngati inuyo.Si ine wonyozeka kwa inu,+Ndipo ndani amene alibe zinthu ngati zimenezi?
4 Ine ndakhala chinthu choseketsa kwa anthu anzanga,+Ndakhala munthu woitana kwa Mulungu kuti amuyankhe.+Munthu wolungama ndi wosalakwa wakhala choseketsa.
5 Amene ali pa mtendere amanyoza tsoka n’kumaganiza kuti+Limagwera okhawo amene mapazi awo amaterereka.+
6 Mahema a anthu olanda amakhala opanda nkhawa,+Ndipo anthu okwiyitsa Mulungu amakhala pa mtendereWofanana ndi wa munthu amene watenga mulungu* m’manja mwake.+
7 Koma funsa nyama zoweta ndipo zikulangiza.+Komanso zouluka zam’mlengalenga, ndipo zikuuza.+
8 Kapena chita chidwi ndi dziko lapansi, ndipo likulangiza.+Nsomba za m’nyanja+ zikuuza.
9 Ndani pa zonsezi sadziwa bwinoKuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi?+
10 Iye amene moyo+ wa aliyense uli m’dzanja lake,Ndiponso mzimu wa anthu onse.+
11 Kodi khutu si paja limasiyanitsa mawu+Ngati mmene m’kamwa+ mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya?
12 Kodi okalamba si paja amakhala ndi nzeru,+Ndipo amene akhala masiku ambiri si paja amamvetsa zinthu?
13 Iye ali ndi nzeru ndi mphamvu.+Amapereka malangizo ndipo amamvetsa zinthu.+
14 Iyetu amagwetsa zinthu kuti zisamangidwe,+Zimene iye watseka, palibe munthu amene angazitsegule.+
15 Amaletsa madzi ndipo amauma,+Amawatumiza ndipo madziwo amasintha dziko lapansi.+
16 Iye ali ndi mphamvu ndi nzeru zopindulitsa.+Kwa iye kuli wochimwa mosazindikira ndi wochimwitsa ena.+
17 Amachititsa alangizi kuyenda opanda nsapato,+Ndipo oweruza amawachititsa misala.
18 Zingwe za mafumu amazimasula,+Ndipo amawamanga lamba m’chiuno.
19 Amachititsa ansembe kuyenda opanda nsapato,+Ndipo amene akhazikika amawawononga.+
20 Okhulupirika, iye amawakhalitsa chete,Ndipo amuna okalamba, iye amawachotsera nzeru.
21 Iye amanyoza anthu olemekezeka,+Ndipo amakhwepetsa lamba wa anthu amphamvu.
22 Amavundukula zinthu zozama zimene zinali pamdima,+Ndipo amaunika pamdima wandiweyani.
23 Amapatsa mphamvu mitundu kuti aiwononge.+Amafutukula mitundu kuti aichotse.
24 Amachotsa nzeru za atsogoleri a anthuwo,Kuti iwo aziyendayenda kumalo kopanda kanthu,+ kumene kulibe njira.
25 Iwo amafufuzafufuza mu mdima+ mopanda kuwala,Kuti awachititse kuyendayenda ngati munthu woledzera.+
Mawu a M'munsi
^ Kutanthauza, “fano.”