Yobu 15:1-35
15 Tsopano Elifazi wa ku Temani anayankha kuti:
2 “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi nzeru zopanda pake,+Kapena angadzaze mimba yake ndi mphepo ya kum’mawa?+
3 Kungodzudzula ndi mawu n’kopanda ntchito,Ndipo mawu ndi osathandiza paokha.
4 Koma chifukwa cha iweyo kuopa Mulungu kwatha,Ndipo ukupeputsa phindu losinkhasinkha pamaso pa Mulungu.
5 Chifukwa zolakwa zako zimaphunzitsa pakamwa pako zoti palankhule,Ndipo umasankha lilime la akathyali.
6 Pakamwa pako m’pamene pakunena kuti ndiwe wolakwa, osati ine,Ndipo milomo yako ikuyankha motsutsana nawe.+
7 Kodi iwe unali munthu woyamba kubadwa?+Kodi unabadwa ndi zowawa za pobereka, mapiri asanakhaleko?+
8 Kodi umamvetsera nkhani zachinsinsi za Mulungu?+Ndipo kodi umaona kuti iwe wekha ndiye wanzeru?
9 Ukudziwa chiyani chimene ife sitikudziwa?+Ndipo umamvetsa chiyani chimene ifeyo tilibe?
10 Aimvi ndi okalamba ali pakati pathu,+Omwe ali akale kuposa bambo ako.
11 Kodi chitonthozo cha Mulungu sichikukukwanira?Kapena kulankhula nawe mawu odekha sikunakukwanire?
12 N’chifukwa chiyani mtima wako ukudzikweza?Ndipo n’chifukwa chiyani maso ako akuwala?
13 Pakuti mtima wako watembenukira Mulungu,Ndipo iwe watulutsa mawu oipa ndi pakamwa pako.
14 Kodi munthu ndani kuti akhale woyera?+Kapena munthu wobadwa kwa mkazi kuti akhale wosalakwa?
15 Iyetu alibe chikhulupiririro mwa angelo* ake,+Ndipo kumwamba si koyera m’maso mwake.+
16 Nanga kuli bwanji munthu wonyansa ndi woipa,+Munthu yemwe amamwa zosalungama ngati madzi?
17 Inetu ndikuuza. Tamvera!+Dikira ndikuuze zimene ndaziona,
18 Zimene anzeru+ amanena,Ndiponso zimene sanabise, zochokera kwa makolo awo.
19 Dziko linaperekedwa kwa iwo okha,Ndipo palibe mlendo amene anadutsa pakati pawo.
20 Woipa amavutika ndi zowawa masiku ake onse,Ngakhale pa zaka zonse zimene zasungidwira wolamulira wankhanza.
21 Woipayo amamva phokoso la zoopsa m’makutu ake,Pa nthawi yamtendere wolanda amam’bwerera.+
22 Iye sakhulupirira kuti adzatuluka mu mdima,+Ndipo akudikira lupanga.
23 Amayendayenda pofunafuna chakudya. Kodi chili kuti?+Akudziwa bwino kuti tsiku la mdima+ layandikira.
24 Zowawa ndi zozunza zimangokhalira kumuchititsa mantha.+Zimamugonjetsa ngati mfumu yomwe yakonzekera nkhondo.
25 Popeza amatambasula dzanja lake motsutsana ndi Mulungu,Ndipo amayesera kuti akhale wamkulu kuposa Wamphamvuyonse,+
26 Popeza iye amalimbana ndi Mulungu mwaliuma,Ndi zishango zake zokhala ndi mfundo zochindikala,
27 Popeza nkhope yake yaphimbika ndi mafuta a m’thupi mwake,Ndipo wanenepa m’chiuno mwake,+
28 Iye amakhala m’mizinda imene idzafafanizidwe,M’nyumba zimene anthu sadzapitiriza kukhalamo,Zimene mosakayikira zidzakhala milu ya miyala.
29 Iye sadzalemera ndipo chuma chake sichidzachuluka.Zinthu zimene adzatenge kwa iwo, sadzazimwaza padziko lapansi.+
30 Iye sadzachoka mu mdima,Moto udzaumitsa nthambi yake,Ndipo adzachotsedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwa Mulungu.+
31 Iye asakhulupirire zopanda pake n’kusocheretsedwa,Chifukwa zopanda pake n’zimene zidzakhale malipiro ake.
32 Zimenezi zidzakwaniritsidwa tsiku la woipayo lisanafike,Ndipo mphukira yake sidzakula mosangalala.+
33 Adzathothola mphesa zake zosapsa ngati mtengo wa mpesa,Ndipo adzayoyola maluwa ake ngati mtengo wa maolivi.
34 Pakuti msonkhano wa ampatuko ndi wopanda phindu,+Ndipo moto uyenera kunyeketsa mahema a anthu aziphuphu.+
35 Iwo amatenga pakati pamavuto n’kubereka zopweteka,+Ndipo mimba yawo imakonza zachinyengo.”
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “oyera.”