Yobu 16:1-22
16 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Ndamva zinthu zambiri ngati zimenezi.Nonsenu ndinu otonthoza onditopetsa!+
3 Kodi mawu opanda pakewa saatha?+Kapena chikukupwetekani n’chiyani kuti muziyankha?
4 Inenso ndikanatha kulankhula ngati mmene mukuchitiramu,Moyo wanu ukanakhala ngati mmene ulili moyo wanga,Kodi ndikanalankhula mawu ogometsa okunenani?+Ndipo kodi ndikanakupukusirani mutu?+
5 Ndikanakulimbikitsani ndi mawu a m’kamwa mwanga,+Ndipo chitonthozo cha milomo yanga chikanachepetsa . . .
6 Ndikalankhula, ululu wanga sukuchepa.+Ndikasiya kutero, n’chiyani chikundichokera?
7 Koma tsopano Mulungu wanditopetsa.+Wawononga onse osonkhana nane.
8 Komanso inu mwandigwira. Umenewu wakhala umboni,+Mwakuti kuwonda kwanga kwandiukira ndipo kukuchitira umboni pankhope panga.
9 Mkwiyo wa Mulungu wandikhadzula. Iye ali nane chidani+Ndipo akundikukutira mano.+Mdani wanga akundiyang’ana ndi diso lozonda.+
10 Iwo ayasamula kukamwa kwawo kuti andimeze.+Andimenya mbama ndi mnyozo.Asonkhana ambirimbiri kuti alimbane nane.+
11 Mulungu wandipereka kwa anyamata,Ndipo wandiponya mwamphamvu m’manja mwa oipa.+
12 Ine ndinali pa mtendere koma iye anandikhutchumula.+Anandigwira kumbuyo kwa khosi n’kundimenyetsa pansi,Ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.
13 Anthu ake oponya mivi ndi uta+ andizungulira.Iye wandiboola impso+ koma osamva chisoni,Wakhuthulira ndulu yanga pansi.
14 Iye akungokhalira kundiboola ngati mpanda.Akundithamangira ngati mmene amachitira wamphamvu.+
15 Khungu langa ndalisokera ziguduli*+ zoti livale,Ndipo ndaika nyanga yanga m’fumbi.+
16 Nkhope yanga yafiira chifukwa cholira,+Ndipo pazikope zanga pali mdima wandiweyani,+
17 Chonsecho manja anga sanachite zachiwawa,Ndipo pemphero langa ndi loyera.+
18 Iwe dziko lapansi, usaphimbe magazi anga.+Pasapezeke malo osungira kulira kwanga.
19 Komanso, wochitira umboni za ine ali kumwamba,Ndipo mboni yanga ili m’mwamba.+
20 Anzanga asanduka ondilankhulira otsutsana nane.+Diso langa lakhala likuyang’ana kwa Mulungu osagona.+
21 Chiweruzo chiperekedwe pakati pa mwamuna wamphamvu ndi Mulungu,Mofanana ndi pakati pa mwana wa munthu ndi mnzake.+
22 Chifukwa pangotsala zaka zochepa,Ndipo ndidzapita ndi njira yomwe sindidzabwerera nayonso.+
Mawu a M'munsi
^ Ena amati “masaka.”