Yobu 17:1-16

17  “Mzimu wanga wasweka,+ masiku anga atha.Kwanga n’kumanda.+   Ndithu, onyoza andizungulira,+Ndipo diso langa likuyang’anitsitsa khalidwe lawo lopanduka.   Chonde, mundisungire chotsimikizira changa.+Palinso ndani amene angagwirane nane chanza+ monga chikole?   Pakuti mtima wawo mwauchititsa kuti ukhale wopanda nzeru.+N’chifukwa chake simukuwakweza.   Munthu angauze anzake kuti atengepo mbali yawo,Koma maso a ana ake adzachita mdima.+   Iye wandisandutsa mwambi+ wa anthu,Mwakuti ndakhala munthu womulavulira kumaso.+   Chifukwa cha kuzunzika, diso langa layamba kuchita mdima.+Ziwalo zanga zonse zakhala ngati mthunzi.   Anthu owongoka mtima akuyang’ana zimenezi modabwa,Ndipo ngakhale munthu wosalakwa wakwiyira wopanduka.   Wolungama akuyendabe panjira yake,+Ndipo wa manja oyera+ akungowonjezeka mphamvu.+ 10  Komabe, amuna nonsenu mungathe kuyambiranso kundinena. Chotero pitirizani,Chifukwa sindikuonapo wanzeru pakati panu.+ 11  Masiku anga atha,+ zolinga zanga zasokonezedwa,+Zofuna za mtima wanga zasokonezedwa. 12  Anzanga akungokhalira kunena zabodza m’malo monena zoona.*+ Iwo akunena kuti:‘Kuwala kuli pafupi, pamene ine ndikungoona mdima wokhawokha.’ 13  Ndikapitiriza kudikira, ku Manda kukhala kunyumba kwanga.+Ndidzayala bedi langa mu mdima.+ 14  Ndidzaitana dzenje+ kuti, ‘Ndinu bambo anga!’Kwa mphutsi+ ndidzati, ‘Mayi anga ndi mlongo wanga!’ 15  Chotero, kodi chiyembekezo changa chili kuti?+Kodi pali amene akuona kuti ine ndili ndi chiyembekezo? 16  Iwo adzatsikira ku Manda otsekedwa ndi zitsulo,Pa nthawi imene tonsefe tidzatsikira limodzi kufumbi.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Anzanga akungokhalira kuika usiku m’malo mwa masana.”