Yobu 2:1-13
2 Pambuyo pa zimenezi, linafika tsiku limene ana a Mulungu woona ankapita kukaonekera pamaso pa Yehova, ndipo nayenso Satana anapita nawo limodzi kukaonekera pamaso pa Yehova.+
2 Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anamuyankha Yehova kuti: “Ndinali kuzungulirazungulira m’dziko lapansi ndi kuyendayendamo.”+
3 Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu,+ poti palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi? Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima,+ woopa Mulungu+ ndiponso wopewa zoipa.+ Komabe iye akadali ndi mtima wosagawanika+ ngakhale kuti iweyo ukundiumiriza+ kuti ndimuwononge popanda chifukwa.”+
4 Koma Satana+ anamuyankha Yehova kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.+
5 Tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”+
6 Choncho Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, ndam’pereka m’manja mwako. Koma samala kuti usakhudze moyo wake.”
7 Kenako Satana anachoka pamaso pa Yehova+ n’kukagwetsera Yobu zilonda zopweteka,+ kuyambira kuphazi mpaka kumutu.
8 Ndiyeno Yobu anatenga phale loti azidzikanda nalo ndipo anali kukhala paphulusa.+
9 Patapita nthawi, mkazi wake anam’funsa kuti: “Kodi mukupitirizabe kukhala ndi mtima wosagawanika?+ Tukwanani Mulungu mufe!”
10 Koma Yobu anamuyankha kuti: “Ukulankhula ngati mmene amalankhulira akazi opusa.+ Kodi tizingolandira zabwino zokha kuchokera kwa Mulungu woona osalandiranso zoipa?”+ M’zonsezi Yobu sanachimwe ndi milomo yake.+
11 Tsopano anzake atatu a Yobu anamva za tsoka lonse limene linamugwera ndipo aliyense wa iwo anabwera kuchokera kwawo. Mayina awo anali Elifazi wa ku Temani,+ Bilidadi wa ku Shuwa+ ndi Zofari wa ku Naama.+ Iwo anakumana pamodzi atachita kupangana+ kuti apite kukazonda Yobu ndi kukamulimbikitsa.+
12 Atakweza maso awo ali chapatali, sanamuzindikire poyamba. Kenako anayamba kulira mokweza mawu ndipo aliyense anang’amba+ malaya ake akunja odula manja, n’kuwaza fumbi m’mwamba pamwamba pa mitu yawo.+
13 Kenako anakhala+ naye limodzi pansi masiku 7 usana ndi usiku, ndipo palibe amene anali kumulankhula chilichonse popeza iwo anaona kuti ululu+ wake unali waukulu kwambiri.