Yobu 22:1-30

22  Tsopano Elifazi wa ku Temani anayankha kuti:   “Kodi mwamuna wamphamvu angakhale waphindu kwa Mulungu?+Kodi aliyense wozindikira angakhale waphindu kwa iye?   Kodi Wamphamvuyonse amasangalala kuti ndiwe wolungama?+Kapena amapindula chilichonse chifukwa chakuti suchita cholakwa?+   Kodi adzakudzudzula chifukwa choopa Mulungu?Kodi adzapita nawe kwa woweruza?+   Kodi kuipa kwako sikwapitirira kale muyezo?+Kodi zolakwa zako sizidzatha?   Umalanda abale ako chikole popanda chifukwa,+Umalanda zovala anthu osauka n’kuwasiya ali maliseche.   Wotopa sum’patsa madzi akumwa,Ndipo wanjala sum’patsa chakudya.+   Munthu wamphamvu, dziko ndi lake.+Ndipo munthu amene amam’kondera amakhala mmenemo.   Akazi amasiye wawabweza chimanjamanja,Ndipo wafooketsa manja a ana amasiye.*+ 10  N’chifukwa chake misampha ya mbalame yakuzungulira,+Ndipo ukusokonezeka ndi zoopsa zadzidzidzi. 11  N’chifukwa chake pali mdima, moti sungathe kuona,Ndipo madzi osefukira akumiza. 12  Kodi Mulungu si wapamwamba kuposa kumwamba?+Onanso kuti nyenyezi+ zonse zili m’mwamba. 13  Komabe iwe wanena kuti: ‘Mulungu akudziwa chiyani?Kodi angathe kuweruza pali mdima wandiweyani? 14  Mitambo imamutchingira malo moti saona,Ndipo iye amayenda pamwamba pa thambo.’ 15  Kodi upitiriza kuyenda panjira yakalekaleImene anthu ochita zoipa anayendamo, 16  Anthu amene anatengedwa nthawi yawo isanakwane,+Amene maziko+ awo amakhuthulidwa ngati madzi a mumtsinje, 17  Ndiponso amene amauza Mulungu woona kuti: ‘Tichokereni!+Kodi Wamphamvuyonse angatichite chiyani?’ 18  Chonsecho iye wadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino,+Ndipo malangizo a anthu oipa ali kutali ndi ine.+ 19  Olungama adzaona chiwonongeko chawo n’kusangalala,+Ndipo wosalakwa adzawaseka kuti: 20  ‘Zoonadi adani athu afafanizidwa,Ndipo zimene azisiya, moto udzazinyeketsa.’ 21  Um’dziwe bwino Mulungu ndi kukhala naye pa mtendere.Ukatero zinthu zabwino zidzabwera kwa iwe. 22  Tenga malamulo pakamwa pake,N’kuika mawu ake mumtima mwako.+ 23  Ukabwerera kwa Wamphamvuyonse,+ udzabwezeretsedwa mwakale.Ukaika zosalungama kutali ndi hema wako, 24  Ndipo ukataya golide wako wamtengo wapatali m’fumbi,Ukataya golide wa ku Ofiri+ m’miyala ya m’zigwa,* 25  Ndithu Wamphamvuyonse adzakhala golide wako wamtengo wapatali,Ndiponso siliva wako wabwino kwambiri.+ 26  Kenako udzasangalala kwambiri ndi Wamphamvuyonse,+Ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu.+ 27  Udzamudandaulira ndipo adzakumvera.+Udzapereka kwa iye zimene unalonjeza.+ 28  Zimene waganiza kuti uchite zidzatheka,Ndipo kuwala kudzaunikira njira zako.+ 29  Ukamalankhula modzitukumula udzachititsidwa manyazi.+Koma iye adzapulumutsa wankhope yozyolika.+ 30  Adzapulumutsa munthu wosalakwa,+Ndipo iwe udzapulumutsidwa chifukwa chakuti manja ako ndi oyera.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”
Onani mawu a m’munsi pa Ge 26:17.