Yobu 23:1-17
23 Tsopano Yobu anayankha kuti:
2 “Ngakhale lero, sindikusangalala ndi mmene zinthu zilili pa moyo wanga. Chotero ndikudandaula.+Dzanja langa likulemera chifukwa chakuti ndikuusa moyo.
3 Ndikanadziwa kumene ndingamupeze,+Bwenzi nditapita kumalo kumene iye amakhala nthawi zonse.+
4 Bwenzi nditapita pamaso pake ndi nkhani yoti aweruze.M’kamwa mwanga bwenzi nditadzazamo mfundo zodziikira kumbuyo.
5 Bwenzi nditadziwa mawu amene amanena pondiyankha,Ndipo bwenzi nditaganizira zimene amandiuza.+
6 Kodi bwenzi iye atalimbana nane ndi mphamvu zambiri?Ayi ndithu! Iye akanandimvera.+
7 Kumeneko, wowongoka mtima adzathetsa nkhani zake ndi iye,Ndipo ine ndikanapulumuka kwa woweruza wanga mpaka kalekale.
8 Ndikapita kum’mawa, iye kulibe.Ndikabwerako, sindimuona.+
9 Ndimapita kumanzere kumene iye akugwira ntchito, koma sindimuona.Amatembenukira kudzanja lamanja, koma ine osamuona,
10 Pakuti iye amadziwa bwino njira imene ine ndimadutsa.+Akamaliza kundiyesa, ndidzakhala ngati golide.+
11 Mapazi anga amatsata mayendedwe ake.Ndasunga njira yake, ndipo sindipatukapo.+
12 Sindisiya malamulo otuluka pakamwa pake.+Ndasunga mosamala mawu a pakamwa pake+ kuposa zimene akufuna kuti ndichite.
13 Iye ali ndi maganizo amodzi, ndani angam’tsutse?+Zimene moyo wake umalakalaka amazichita.+
14 Iye adzachita zonse zimene wandikonzera,+Ndipo zinthu zoterezi n’zambiri kwa iye.
15 N’chifukwa chake ndikusokonezeka chifukwa cha iye.Ndikaganizira za iye, ndikumachita mantha.+
16 Mulungu wachititsa mantha mtima wanga.+Wamphamvuyonse wandisokoneza,+
17 Pakuti sindinaletsedwe kulankhula chifukwa cha mdima,Kapenanso chifukwa chakuti mdima wandiweyani waphimba nkhope yanga.