Yobu 24:1-25
24 “N’chifukwa chiyani Wamphamvuyonse sanakhazikitse nthawi yachiweruzo,+Ndipo n’chifukwa chiyani omudziwa sanaone masiku ake achiweruzo?+
2 Pali anthu amene amasuntha malire,+Iwo alanda gulu la ziweto kuti aziziweta.
3 Amathamangitsa ngakhale bulu wamphongo wa ana amasiye,*Amalanda ng’ombe yamphongo ya mkazi wamasiye ngati chikole.+
4 Amapatutsa osauka panjira,+Ndipo pa nthawi yomweyo ozunzika a padziko lapansi amakhala atabisala.
5 Monga mbidzi+ m’chipululu,Osaukawo amapita kukafunafuna chakudya.Chipululu chimapatsa aliyense chakudya cha ana ake.
6 M’munda wa munthu wina, osauka amakololamo chakudya cha ziweto,Ndipo iwo amalanda msangamsanga zinthu za m’munda wa mpesa wa munthu woipa.
7 Osaukawo amakhala usiku wonse ali maliseche,+Amakhala pamphepo opanda chofunda.+
8 Amanyowa ndi mvula yamkuntho ya m’mapiri,Ndipo chifukwa chakuti alibe pobisala,+ amakupatira thanthwe.
9 Oipa amalanda mwana wamasiye kum’chotsa pabere.+Amatenga ngati chikole chovala chimene wozunzika wavala.+
10 Ozunzika amayenda opanda chovala,Amasenza mitolo ya tirigu ali ndi njala.+
11 Nthawi ya masana amakhala pakati pa migula ya m’minda.Amaponda mphesa koma amakhala ndi ludzu.+
12 Anthu amene akufa amamveka kubuula kunja kwa mzinda,Moyo wa anthu amene akufa chifukwa chovulala umafuula popempha thandizo,+Ndipo Mulungu saziona ngati zolakwika.+
13 Oipawo amasonyeza kuti ali pakati pa opanduka omwe amatsutsana ndi kuwala.+Iwo sanazindikire njira zake,Ndipo sanakhale m’misewu yake.
14 Kukangocha, wakupha amadzukaKupita kukapha wozunzika ndi wosauka,+Ndipo usiku iye amakhala wakuba.+
15 Diso la wachigololo+ limadikira kuti mdima ugwe madzulo.+Iye amati, ‘Palibe diso limene lindione,’+Ndipo amaphimba kumaso kwake.
16 Mu mdima iye amathyola nyumba za anthu,Masana iwo amadzitsekera m’nyumba,Ndipo saona kuwala kwa masana.+
17 Kwa iwo m’mawa n’chimodzimodzi ndi mdima wandiweyani,+Chifukwa zoopsa zadzidzidzi za mu mdima wandiweyani amazidziwa.
18 Woipa amatengedwa mwamsanga ndi madzi.Malo awo adzakhala otembereredwa padziko lapansi.+Sadzapatukira kunjira yopita kuminda ya mpesa.
19 Chilala ndi kutentha zimatenga madzi a chipale chofewa.Ndi mmenenso Manda amachitira ndi anthu amene achimwa.+
20 Mimba idzamuiwala, mphutsi zidzamumva kutsekemera pomuyamwa,+Ndipo iye sadzakumbukiridwanso.+Kupanda chilungamo kudzathyoledwa ngati mtengo.+
21 Woipa amachita zoipa ndi mkazi wouma amene sabereka,Komanso ndi mkazi wamasiye+ amene woipayo sam’chitira zabwino.
22 Ndi mphamvu zake, Mulungu adzakoka anthu anyonga.Oipa adzakhala apamwamba n’kumakayikira za moyo wawo.
23 Mulungu adzachititsa oipawo kuti azidzidalira+ n’cholinga choti azitha kudzisamalira.Maso ake adzakhala panjira zawo.+
24 Oipawo amakhala okwezeka kwa kanthawi, kenako n’kutha.+Iwo amatsitsidwa,+ ndipo mofanana ndi wina aliyense amathotholedwa.Amadulidwa mofanana ndi nsonga ya ngala za tirigu.
25 Choncho ndani amene anganene kuti ndine wabodza?Kapena kunena kuti mawu anga ndi achabechabe?”
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”