Yobu 29:1-25
29 Yobu anayambanso kulankhula mwandakatulo kuti:
2 “Ndikulakalaka ndikanakhala ngati mmene ndinalili m’miyezi yakale,+Ngati mmene ndinalili m’masiku amene Mulungu anali kundiyang’anira,+
3 Pamene anachititsa nyale yake kuwala pamutu panga,Pamene ndinkayenda mu mdima iye akundiunikira ndi kuwala kwake.+
4 Ngati mmene ndinalili m’masiku amene ndinali mnyamata,+Pamene Mulungu anali bwenzi langa lapamtima, ndipo anali pahema wanga,+
5 Pamene Wamphamvuyonse anali nane,Pamene antchito anga onse anandizungulira,
6 Pamene ndinkasambitsa mapazi anga m’mafuta a mkaka,Ndiponso pamene miyala inkanditulutsira mitsinje ya mafuta.+
7 Ndikapita kuchipata cha mzinda,+Ndinkakonzako malo anga okhala pabwalo la mzinda.+
8 Anyamata akandiona, ankabisala.Ngakhale okalamba ankanyamuka n’kuima chilili.+
9 Akalonga ankabweza mawu,Ndipo ankagwira pakamwa.+
10 Mawu a atsogoleri ankabisika,Ndipo lilime lawo linkamamatira m’kamwa mwawo.+
11 Khutu likamva, linkanena kuti ndine wodala,Ndipo diso likaona, linkandichitira umboni.
12 Pakuti ndinkapulumutsa wosautsika wopempha thandizo,+Ndiponso mwana wamasiye* ndi aliyense amene analibe womuthandiza.+
13 Madalitso+ a munthu amene watsala pang’ono kuwonongedwa ankabwera kwa ine,Ndipo ndinkasangalatsa mtima wa mkazi wamasiye.+
14 Ndinkavala chilungamo, ndipo icho chinkandiveka.+Chilungamo changa chinali ngati malaya akunja odula manja, ndi nduwira.*
15 Ndinali ngati maso kwa wakhungu,+Ndipo ndinali mapazi kwa wolumala.
16 Ndinali bambo weniweni kwa osauka,+Ndipo mlandu wa munthu amene sindinali kumudziwa ndinkaufufuza.+
17 Ndinkaphwanya nsagwada za wochita zoipa,+Ndipo wogwidwa, ndinkamulanditsa kukamwa kwa wochita zoipayo.
18 Ndinkati, ‘Ndidzafera m’chisa changa,+Ndidzachulukitsa masiku anga ngati mchenga.+
19 Muzu wanga ndi wotseguka kuti uyamwe madzi,+Ndipo mame akhala usiku wonse panthambi yanga.
20 Ulemerero wanga ndili nawobe,Ndipo uta umene uli m’manja mwanga uziponya mivi mobwerezabwereza.’
21 Anthu ankandimvera ndipo ankandidikirira.Ankakhala phee kuti amve malangizo anga.+
22 Ndikamaliza kulankhula, iwo sankalankhulanso.Ndipo mawu anga ankadonthera pa iwo.+
23 Iwo ankandidikirira ngati akudikira mvula,+Ndipo ankayasama kuti m’kamwa mwawo mugwere mvula yomalizira.+
24 Ndinkawamwetulira, koma iwo sankakhulupirira,Ndipo kuwala kwa pankhope+ panga sankakuzimitsa.
25 Ndinkawasankhira njira, ndipo ndinkakhala pansi patsogolo pawo.Ndinali ngati mfumu pakati pa asilikali ake,+Ndiponso ngati wotonthoza olira.+
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
^ “Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.