Yobu 31:1-40
31 “Ndachita pangano ndi maso anga.+Choncho ndingayang’anitsitse bwanji namwali?+
2 Kodi pali gawo lanji lochokera kwa Mulungu+ kumwamba,Kapena cholowa chochokera kwa Wamphamvuyonse m’mwamba?
3 Kodi si paja wochita zoipa amakumana ndi zosautsa,+Ndipo ochitira anzawo zopweteka tsoka limawagwera?
4 Kodi iye saona njira zanga,+Ndi kuwerenga masitepe anga onse?
5 Ngati ndayenda ndi anthu osanena zoona,+Ndipo phazi langa lathamangira ku chinyengo,+
6 Iye adzandiyeza pasikelo zolondola,+Ndipo Mulungu adzadziwa kuti ndili ndi mtima wosagawanika.+
7 Ngati ndaponda kumbali kusiya njira,+Kapena ngati mtima wanga ukungotsatira maso anga,+Kapenanso ngati cholakwa chilichonse chamatirira m’manja mwanga,+
8 Ine ndibzale mbewu wina n’kudya,+Ndipo mbadwa zanga zichotsedwe padziko.
9 Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi,+Ndipo ndinali kudikirira+ pakhomo lolowera kunyumba kwa mnzanga,
10 Mkazi wanga aperere ufa mwamuna wina,Ndipo amuna ena agone naye.+
11 Chifukwa limenelo lingakhale khalidwe lotayirira,Ndipo chimenecho chingakhale cholakwa chofunika kupita nacho kwa oweruza.+
12 Pakuti umenewu ndi moto umene unganyeketse zinthu mpaka kuziwononga,+Ndipo unganyeketse mbewu zanga zonse ndi mizu yomwe.
13 Ngati ndinkalepheretsa chiweruzo cha kapolo wanga wamwamuna,Kapena cha kapolo wanga wamkazi pa mlandu ndi ine,
14 Ndiye ndingatani Mulungu akaimirira,Ndipo akandifunsa ndingamuyankhe chiyani?+
15 Kodi amene anandipanga m’mimba si amene anapanganso iyeyo?+Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe m’mimba?
16 Ngati ndinkakaniza anthu onyozeka zopempha zawo,+Ndipo ngati ndinkachititsa chisoni maso a mkazi wamasiye,+
17 Ngati ndinkanyema chakudya changa n’kumadya ndekha,Mwana wamasiye* osadya nawo,+
18 (Pakuti kuyambira ubwana wanga iye wakula ndi ine ngati bambo ake,Ndipo kuyambira m’mimba mwa mayi anga ndakhala ndikutsogolera mkazi wamasiyeyo).
19 Ngati ndinkaona munthu akuzunzika chifukwa chosowa chovala,+Kapena kuona kuti wosauka alibe chofunda,
20 Ngati iye* sanandidalitse,+Ndipo ngati sanavale ubweya+ wometedwa ku nkhosa zanga zamphongo zazing’ono kuti afundidwe,
21 Ngati ndili pachipata ndinaonapo mwana wamasiye akufunika thandizo langa,+Koma ine n’kumuopseza ndi dzanja langa,+
22 Fupa la paphewa langa ligwe kuchoka m’malo mwake,Ndipo fupa lakumtunda la dzanja langa lithyoke.
23 Chifukwa ine ndinkaopa tsoka lochokera kwa Mulungu,Ndipo ulemu wake+ sindikanatha kulimbana nawo.
24 Ngati ndayesa golide chinthu chodalira,Kapena ngati ndanena kwa golide kuti, ‘Ndimadalira iwe,’+
25 Ngati ndinkasangalala chifukwa chakuti ndinali ndi katundu wambiri,+Ndiponso chifukwa chakuti dzanja langa linapeza zinthu zambiri,+
26 Ngati ndinkaona kuwala kukamanyezimira,Kapena mwezi wamtengo wapatali ukuyenda,+
27 Ndipo mtima wanga unayamba kukopeka mobisa,+Komanso dzanja langa linapsompsona pakamwa panga,
28 Chimenechonso chikanakhala cholakwa chofunika kupita nacho kwa oweruza,Chifukwa ndikanakhala nditakana Mulungu woona wakumwamba.
29 Ngati ndinkasangalala ndi kutha kwa munthu amene ankadana nane kwambiri,+Kapena ngati ndinkakondwera chifukwa chakuti zoipa zam’gwera . . .
30 Ine sindinalole m’kamwa mwanga kuchimwa,Popempha lumbiro loipira moyo wake.+
31 Ngati amuna a m’hema wanga sananene kuti,‘Ndani angabwere ndi munthu amene sanakhute chakudya cha iye?’+ . . .
32 Palibe mlendo amene ankagona panja usiku.+Zitseko zanga ndinkazisiya zotsegula kwa odutsa m’njira.
33 Ngati ndinabisa zolakwa zanga monga munthu wochokera kufumbi,+Pobisa machimo anga m’thumba la malaya . . .
34 Chifukwa choopa khamu lalikulu,Ndiponso chifukwa choopa kunyozedwa ndi mabanja,Ndinkakhala chete, sindinkatuluka pakhomo.
35 Ndikulakalaka ndikanakhala ndi wina wondimvetsera,+Kuti mogwirizana ndi chizindikiro changa chochita kulemba, Wamphamvuyonse andiyankhe.+Ndikulakalaka munthu amene ali nane pa mlandu akanalemba chikalata.
36 Ndithu ndikanachinyamula paphewa.Ndikanachizunguliza kumutu kwanga ngati chisoti chachikulu chachifumu.
37 Sindikanazengereza kumuuza za mayendedwe anga onse.+Ndikanapita kwa iye ngati kwa mtsogoleri.
38 Ngati nthaka yanga ikanandilirira popempha thandizo,Ndipo ngati mizere yake ikanalirira pamodzi,
39 Ngati ndadya zipatso zake osapereka ndalama,+Ndipo ndachititsa moyo wa olima ake kupumira m’mwamba,+
40 M’malo mwa tirigu, pamere chitsamba chaminga,+Ndipo m’malo mwa balere, pamere zitsamba zonunkha.”Mawu a Yobu athera pamenepa.
Mawu a M'munsi
^ Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
^ Mawu ake enieni, “chiuno chake.”