Yobu 34:1-37
34 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:
2 “Mvetserani mawu anga, anthu anzeru inu.Ndipo anthu odziwa zinthu inu, ndimvereni.
3 Pakuti khutu limasiyanitsa mawu,+Monga mmene m’kamwa mumasiyanitsira kakomedwe ka chakudya.+
4 Tiyeni tidzisankhire chiweruzo.Tidziwe tokha pakati pathu chimene chili chabwino.
5 Pakuti Yobu wanena kuti, ‘Ndithu ine si ine wolakwa,+Koma Mulungu wapotoza chiweruzo changa.+
6 Kodi ndikunama za mmene chiweruzo changa chiyenera kukhalira?Chilonda changa chachikulu sichikupola ngakhale kuti sindinachimwe.’+
7 Kodi ndi mwamuna wamphamvu uti amene ali ngati Yobu,+Yemwe amamwa mnyozo ngati madzi?+
8 Iye ndithu ali pa ulendo wokachita ubwenzi ndi anthu ochita zopweteka ena,Komanso ali pa ulendo wokayenda ndi anthu oipa.+
9 Chifukwa wanena kuti, ‘Mwamuna wamphamvu sapindula kanthu+Akamachita zosangalatsa Mulungu.’
10 Choncho inu amuna a mtima+ womvetsa zinthu, ndimvereni.Mulungu woona sangachite zoipa m’pang’ono pomwe,+Ndipo Wamphamvuyonse sangachite zinthu zopanda chilungamo ngakhale pang’ono.+
11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake.
12 Ndithudi, Mulungu sachita zoipa,+Ndipo Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.+
13 Ndani wam’patsa dziko lapansi?Ndipo ndani wam’patsa ulamuliro panthaka yonse?
14 Akaika mtima wake pa munthu aliyense,Akatenga mzimu* ndi mpweya wa munthuyo,+
15 Zamoyo zonse zimafera limodzi,Ndipo munthu amabwerera kufumbi.+
16 Choncho ngati mumamvetsa zinthu, mvetserani izi.Mvetserani mawu anga.
17 Kodi zoonadi munthu wodana ndi chilungamo angalamulire?+Ngati munthu wamphamvu ali wolungama, kodi munganene kuti ndi woipa?+
18 Kodi munthu anganene kwa mfumu kuti, ‘Ndinu wopanda pake’?Kapena angauze anthu olemekezeka kuti, ‘Ndinu oipa’?+
19 Alipo amene sanakonderepo akalonga,Ndipo saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka,+Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+
20 Iwo amafa mwadzidzidzi,+ ngakhale pakati pa usiku.+Anthuwo amagwedezeka uku ndi uku n’kufa,Ndipo amphamvu amachoka popanda dzanja lowachotsa.+
21 Pakuti maso ake amayang’anitsitsa njira za munthu,+Ndipo amaona mayendedwe ake onse.
22 Kulibe mdima wandiweyaniWoti amene akuchita zopweteka ena abisaleko.+
23 Pakuti iye saikiratu nthawi yoti munthu aliyenseApite kukaweruzidwa ndi Mulungu.
24 Iye amaphwanya amphamvu+ popanda kuwafufuza,Ndipo amachititsa ena kuima m’malo mwawo.+
25 Chotero iye amazindikira ntchito zawo.+Amawagwetsa usiku ndipo iwo amatswanyidwa.+
26 Amawamenya monga oipa,Pamalo pomwe ena akuonerera.+
27 Chifukwa asiya kumutsatira,+Ndipo sasamala za njira zake zonse,+
28 Kuti achititse kulira kwa wonyozeka kupita kwa iye.Choncho iye amamva kulira kwa osautsika.+
29 Iye akachititsa bata, ndani angamudzudzule?Ndipo akabisa nkhope yake,+ ndani angamuone?Kaya abisire nkhope yake mtundu+ kapena munthu, n’chimodzimodzi.
30 Kuti munthu wopanduka asalamulire,+Ndi kuti pasakhale misampha+ ya anthu.
31 Kodi munthu ndithu anganene kwa Mulungu kuti,‘Ndapirira ngakhale kuti sindinachite cholakwa?+
32 Ngakhale kuti sindikuona chilichonse, inuyo ndiphunzitseni?Ngati ndachita chosalungama chilichonse,Sindidzachichitanso?’+
33 Kodi iye angakulipire mogwirizana ndi mmene ukuganizira, chifukwa chakuti ukukana chiweruzo chake?Chifukwa chakuti iweyo wasankha wekha, osati ine?Tsopano nena zimene ukudziwa.
34 Anthu a mtima womvetsa zinthu+ adzandiuza,Ngakhale munthu wanzeru komanso wamphamvu amene akundimvetsera adzandiuza kuti,
35 ‘Yobu sadziwa zimene akunena,+Ndipo amanena mawu osonyeza kuti iye ndi wosazindikira.’
36 Atate anga, Yobu ayesedwe mpaka pamapetoChifukwa cha zimene anali kuyankha pakati pa amuna ochita zopweteka anzawo.+
37 Chifukwa pa tchimo lake akuwonjezerapo kupanduka.+Akuwomba m’manja pakati pathu ndipo akuchulutsa zonena zake zotsutsana ndi Mulungu woona.”+
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 4.