Yobu 35:1-16
35 Elihu anapitiriza kulankhula kuti:
2 “Kodi mukuona ngati chimenechi n’chilungamo?Inuyo mwanena kuti, ‘Ndine wolungama kuposa Mulungu.’+
3 Mwanena kuti, ‘Kodi kulungamako n’kwantchito yanji kwa inu?+Kodi kundipindulitsa chiyani kuposa chimene ndikanapindula pochimwa?’+
4 Ineyo ndikuyankhani inuyoNdi mabwenzi+ anu muli nawowo.
5 Yang’anani kumwamba+ muone.Muona kuti mitambo+ ili pamwamba kuposa inu.
6 Mukachimwa, kodi mumapindula chiyani chotsutsana naye?+Ndipo kupanduka kwanu kukawonjezeka, kodi mumam’chitira chiyani chomuipira?
7 Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa chiyani?Kodi amalandira chiyani kuchokera m’manja mwanu?+
8 Kuipa kwanu kungapweteke munthu ngati inu nomwe,+Ndipo chilungamo chanu chingakomere mwana wa munthu wochokera kufumbi.+
9 Chifukwa cha kuchuluka kwa kuponderezedwa, iwo amangokhalira kufuula popempha thandizo.+Amangokhalira kulirira thandizo chifukwa cha dzanja la amphamvu.+
10 Koma palibe wanena kuti, ‘Kodi Mulungu, Wondipanga Wamkulu,+ ali kuti,Amene amapatsa anthu nyimbo usiku?’+
11 Iye ndiye amatiphunzitsa+ zambiri kuposa nyama zakutchire,+Ndipo amatipatsa nzeru kuposa ngakhale zolengedwa zouluka m’mlengalenga.
12 Iwo amangokhalira kulirira thandizo, koma iye sawayankha+Chifukwa cha kunyada+ kwa anthu oipa.
13 Koma Mulungu samva kufuula kwa anthu olankhula zinthu zonama,+Ndipo Wamphamvuyonse sawaona.+
14 Nanga kuli bwanji mukanena kuti simumuona?+Mlanduwo uli pamaso pake, choncho muzimuyembekezera ndi nkhawa.+
15 Tsopano popeza sanakulangeni chifukwa cha mkwiyo wake,+Iye sanaonenso kupupuluma kwanu.+
16 Yobu akatsegula pakamwa pake amalankhula zopanda pake.Amachulukitsa mawu osonyeza kuti palibe chimene akudziwa.”+