Yobu 36:1-33
36 Elihu anapitiriza kunena kuti:
2 “Ndilezereni mtima kwa kanthawi kochepa ndipo ndikuuzaniKuti mawu alipobe oti ndinene m’malo mwa Mulungu.
3 Zimene ndinene ndizitenga kutali,Ndipo ndilengeza kuti amene anandipanga, ndiye mwiniwake wa chilungamo.+
4 Chifukwa mawu anga ndithu si onama.Wodziwa bwino zinthu kwambiri+ ali ndi inu.
5 Mulungutu ndi wamphamvu+ ndipo sadzakana munthu.Iye ali ndi mphamvu zazikulu zomvetsa zinthu.
6 Iye sadzasiya woipa aliyense ali wamoyo,+Koma adzapereka chiweruzo cholungama kwa osautsika.+
7 Sadzachotsa maso ake pa aliyense wolungama.+Adzaika mafumu pamipando yachifumu,+Adzawachititsa kuti alamulire kwamuyaya, ndipo iwo adzakhala ndi mphamvu zambiri.
8 Anthu akamangidwa m’matangadza,+Amagwidwa ndi zingwe za masautso.
9 Ndiyeno iye adzawauza za momwe iwo amachitira zinthuNdiponso zolakwa zawo, chifukwa iwo amadzikuza.
10 Iye adzatsegula makutu awo kuti iwo amve pamene iye akuwalimbikitsa,+Ndipo adzawauza kuti asiye kuchita zopweteka ena.+
11 Akamumvera ndi kumutumikira,Adzamaliza bwino masiku awo,Ndipo adzamaliza zaka zawo mosangalala.+
12 Koma akapanda kumvera, adzaphedwa+ ndi chida.+Iwo adzafa ali osadziwa.
13 Anthu ampatuko adzaunjika mkwiyo.+Iwo sadzalirira thandizo chifukwa chakuti iye wawamanga.
14 Iwo adzafa ali anyamata,+Ndipo moyo wawo udzathera pakati pa mahule aamuna a pakachisi.+
15 Iye adzapulumutsa wozunzika m’masautso ake,Ndipo adzatsegula makutu awo pamene akuponderezedwa.
16 Ndithu iye adzakukopani n’kukuchotsani pakamwa pa zowawa.+M’malomwake padzakhala malo otakasuka,+ osati opanikiza,Ndipo chitonthozo cha patebulo panu chidzakhala chodzaza ndi mafuta.+
17 Ndithu mudzakhutira woipa+ akadzaweruzidwa.Chiweruzo ndi chilungamo zidzakhazikika.
18 Samalani kuti mkwiyo+ usakuchititseni kuwomba m’manja chifukwa cha njiru,Ndipo dipo lalikulu+ lisakusocheretseni.
19 Kodi kulira kwanu kopempha thandizo kudzakupindulirani?+ Ayi, sikudzakupindulirani ngakhalenso pa mavuto,Ngakhale muyesetse mwamphamvu bwanji.+
20 Musapumire m’mwamba polakalaka usiku,Pamene anthu amabwera kuchokera kumene anali.
21 Samalani kuti musabwerere ku zinthu zopweteka ena,+Chifukwa mwasankha zimenezi m’malo mwa masautso.+
22 Mulungutu amachita zinthu zapamwamba ndi mphamvu zake.Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana naye?
23 Ndani wam’funsa kuti afotokoze za njira yake,+Ndipo ndani wamuuza kuti, ‘Mwachita zosalungama’?+
24 Kumbukirani kuti muyenera kutamanda ntchito zake,+Zimene anthu amaziimba.+
25 Anthu onse amaziyang’anitsitsa.Munthu amaziyang’ana ali patali.+
26 Mulungu ndi wokwezeka kuposa mmene tikudziwira.+Zaka zake n’zosawerengeka.+
27 Pakuti iye amakoka madontho a madzi.+Madonthowo amasefeka n’kutsika ngati mvula ndi nkhungu,
28 Moti mitambo imakha,+Imakhetsa madzi ochuluka pa anthu.
29 Zoonadi, ndani angamvetse mmene mitambo imatambasukira?Komanso kugunda kochokera kumsasa wake?+
30 Amaikuta ndi kuwala kwake,+Ndipo waphimba mizu ya nyanja.
31 Ndi zimenezi, iye amaweruza mokomera mitundu ya anthu.+Amapereka chakudya chochuluka.+
32 Iye wafumbata mphezi m’manja mwake,Ndipo amailamula kuti igwere woukira.+
33 Kugunda kwake+ kumanena za iye.Ziwetonso zimanena za amene akubwera.