Yobu 42:1-17

42  Tsopano Yobu anamuyankha Yehova kuti:   “Ndadziwa kuti inu mumatha kuchita zinthu zonse,+Ndipo palibe zimene simungakwanitse.+   Inu munati, ‘Kodi amene akuphimba malangizo anga mopanda nzeruyu ndani?’+Chotero ine ndinalankhula, koma sindinali kuzindikiraZinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine, zimene sindikuzidziwa.+   Inu munati, ‘Tamvera, ndikufuna ndikulankhule.Ndikufunsa mafunso ndipo iweyo undiyankhe.’+   Ndinkangomva za inu,Koma tsopano diso langa lakuonani.   N’chifukwa chake ndikubweza mawu anga,Ndipo ndikulapa+ m’fumbi ndi m’phulusa.”  Yehova atanena mawu amenewa kwa Yobu, Yehovayo anauza Elifazi wa ku Temani kuti:“Mkwiyo wanga wayakira iweyo ndi anzako awiriwo+ chifukwa inu simunanene zoona za ine,+ monga wachitira Yobu mtumiki wanga.  Tsopano utenge ng’ombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.+ Upite nazo kwa mtumiki wanga Yobu,+ ndipo inuyo mukadziperekere nsembe yopsereza. Ndiyeno Yobu mtumiki wanga akakupemphererani.+ Ine ndimvera iye yekhayo basi kuti ndisakuchititseni manyazi chifukwa cha zopusa zimene mwachita, popeza simunanene zoona za ine monga wachitira Yobu mtumiki wanga.”+  Chotero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Shuwa ndi Zofari wa ku Naama anapita n’kukachita monga mmene Yehova anawauzira. Choncho Yehova anamva pemphero la Yobu. 10  Tsopano Yehova anathetsa masautso a Yobu+ pamene iye anapempherera anzake aja.+ Kuwonjezera pamenepo Yehova anayamba kum’patsa Yobu zonse zimene anali nazo, kuwirikiza kawiri.+ 11  Abale ake onse, alongo ake onse ndi onse amene anali kumudziwa kale+ ankabwera kwa iye. Iwo anayamba kudyera naye pamodzi mkate+ m’nyumba mwake, komanso anali kumulimbikitsa ndi kum’pepesa chifukwa cha tsoka lonse limene Yehova analola kuti lim’gwere. Aliyense wa iwo anapatsa Yobu mphatso ya ndalama ndi mphete yagolide. 12  Yehova anadalitsa+ kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake+ moti iye anakhala ndi nkhosa 14,000, ngamila 6,000, ng’ombe 2,000 zimene zinkagwira ntchito zili ziwiriziwiri, ndi abulu aakazi 1,000. 13  Anakhalanso ndi ana aamuna 7 ndi ana aakazi atatu.+ 14  Mwana wake wamkazi woyamba anam’patsa dzina lakuti Yemima, wachiwiri Keziya ndipo wachitatu Kereni-hapuki. 15  M’dziko lonselo munalibe akazi okongola ngati ana aakazi a Yobu, ndipo bambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi abale awo.+ 16  Pambuyo pa zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140+ ndipo anaona ana ake ndi zidzukulu zake+ mpaka m’badwo wachinayi. 17  Pomalizira pake Yobu anamwalira ali wokalamba ndiponso wokhutira ndi masiku ake.+

Mawu a M'munsi