Yobu 8:1-22

8  Kenako Bilidadi wa ku Shuwa+ anati:   “Kodi ukhala ukulankhula zimenezi mpaka liti,+Pamene zolankhula za m’kamwa mwako zili ngati mphepo yamphamvu?+   Kodi Mulungu angapotoze chiweruzo?+Ndipo kodi Wamphamvuyonse angapotoze chilungamo?+   Ngati ana ako amuchimwira,Mwakuti iye wawalanga chifukwa cha kupanduka kwawo,   Iweyo ukafunafuna Mulungu,+Ndi kuchonderera Wamphamvuyonse,   Ngati uli woyera ndi wowongoka mtima,+Bwenzi panopa atadzuka kuti akumvere,Ndipo ndithu akanabwezeretsa malo ako olungama pamene unali kukhala.   Komanso chiyambi chako chikanaoneka ngati chaching’ono,Koma mapeto ako akanakhala aakulu kwambiri.+   Tafunsa m’badwo wakale,+Ndipo ganizira zinthu zimene makolo awo anafufuza.+   Pakuti ife tabadwa dzulo,+ ndipo sitikudziwa kalikonse,Chifukwa masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi.+ 10  Kodi iwo sadzakulangiza, sadzakuuza?Ndipo kodi iwo sadzalankhula kuchokera mumtima mwawo? 11  Kodi gumbwa*+ amamera n’kutalika pamalo pamene si padambo?Ndipo kodi bango limakula popanda madzi? 12  Pamene ilo likadali ndi maluwa, lisanazulidwe,Lingaume msanga udzu wina wonse usanaume.+ 13  Ndi mmene zilili njira za onse oiwala Mulungu,+Ndipo chiyembekezo cha wampatuko chidzatha.+ 14  Iye amene chidaliro chake chimatha,Amene amadalira ulusi* wa kangaude.+ 15  Iye adzatsamira nyumba yake, koma siidzakhala chiimire.Adzaigwira, koma siidzakhalitsa. 16  Iye ali ngati chomera chachiwisi bwino chomwe chikuwombedwa dzuwa.M’munda mwake, nthambi zake zimakula.+ 17  Mizu yake imapiringizanapiringizana pamulu wa miyala.Iye amaona kuti miyalayo ndi nyumba yake. 18  Wina akam’meza pamalo ake,+Malowo adzamukana kuti, ‘Sindinakuonepo.’+ 19  Umu ndi mmene moyo wake umathera,+Ndipo m’fumbimo mumamera zina. 20  Mulungutu sangakane munthu wopanda cholakwa,Ndipo sangagwire dzanja la ochita zoipa. 21  Adzadzaza m’kamwa mwako ndi kuseka,Ndipo milomo yako adzaidzaza ndi mfuu yachisangalalo. 22  Anthu odana nawe adzadzazidwa ndi manyazi,+Ndipo hema wa oipa kudzakhala kulibe.”

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “nyumba.”