Yohane 14:1-31

14  “Mitima yanu isavutike.+ Khulupirirani Mulungu,+ khulupiriraninso ine.+  M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambiri okhalamo.+ Akanapanda kukhalamo, ndikanakuuzani, chifukwa ndikupita kukakukonzerani malo.+  Ndiponso, ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso+ kudzakutengerani kwathu,+ kuti kumene kuli ineko inunso mukakhale kumeneko.+  Ndipo kumene ndikupitako, inu njira yake mukuidziwa.”  Tomasi+ anafunsa kuti: “Ambuye, ife sitikudziwa kumene mukupita.+ Ndiye njira yake tingaidziwe bwanji?”  Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine njira,+ choonadi+ ndi moyo.+ Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.+  Inu mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga. Kuyambira panopa mwawadziwa ndipo mwawaona.”+  Pamenepo Filipo anati: “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo tikhutira.”  Yesu anati: “Anthu inu, ndakhala nanu nthawi yonseyi, koma kodi iwe Filipo sunandidziwebe? Amene waona ine waonanso Atate.+ Nanga iwe bwanji ukunena kuti, ‘Tionetseni Atate’?+ 10  Sukukhulupirira kodi, kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana?+ Zinthu zimene ine ndimanena kwa inu sindilankhula za m’maganizo mwanga, koma Atate amene ali wogwirizana ndi ine ndiye akuchita ntchito zake.+ 11  Khulupirira kuti ine ndi Atate ndife ogwirizana, apo ayi, ingokhulupirira chifukwa cha ntchito zokhazi.+ 12  Ndithudi ndikukuuzani, Wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu+ kuposa zimenezi, chifukwa ine ndikupita kwa Atate.+ 13  Komanso chilichonse chimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzachichita, kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana wake.+ 14  Ngati mutapempha chilichonse m’dzina langa, ine ndidzachichita. 15  “Ngati mumandikonda, mudzasunga malamulo anga.+ 16  Inenso ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani mthandizi wina kuti adzakhale nanu kosatha.+ 17  Mthandizi ameneyo ndi mzimu wa choonadi.+ Mzimu umenewo dziko silingaulandire,+ chifukwa siliuona kapena kuudziwa. Inu mumaudziwa chifukwa umakhala mwa inu, ndipo uli mwa inu.+ 18  Sindikusiyani ngati ana amasiye.+ Ndidzabwera kwa inu. 19  Kwatsala kanthawi pang’ono ndipo dziko silidzandionanso.+ Koma inu mudzandiona,+ chifukwa ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo.+ 20  Pa tsikulo mudzadziwa kuti ine ndili wogwirizana ndi Atate, inunso ndi ine ndife ogwirizana.+ 21  Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda.+ Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.” 22  Yudasi,+ wina osati Isikariyoti, anati: “Ambuye, bwanji mukufuna kudzionetsera bwinobwino kwa ife koma osati ku dzikoli?”+ 23  Yesu anamuyankha kuti: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga+ mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo tidzapita kwa iwo ndi kukakhala nawo.+ 24  Amene sandikonda ine sasunga mawu anga, ndipo mawu amene mukumvawa si anga, koma ndi a Atate amene anandituma.+ 25  “Ndakuuzani zimenezi pamene ndidakali ndi inu. 26  Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera, amene Atate wanga adzatumiza m’dzina langa, adzakuphunzitsani zinthu zonse ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani.+ 27  Ndikusiyirani mtendere, ndikupatsani mtendere wanga.+ Sindikuupereka kwa inu mmene dziko limauperekera ayi. Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha. 28  Mwandimva ndikukuuzani kuti, Ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu. Ngati munali kundikonda, mukanakondwera kuti ndikupita kwa Atate wanga, chifukwa Atate ndi wamkulu+ kuposa ine. 29  Choncho, ndakuuzani zisanachitike,+ kuti zikachitika, mukhulupirire. 30  Sindilankhula nanunso zambiri, pakuti wolamulira+ wa dziko akubwera. Iye alibe mphamvu pa ine,+ 31  koma kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita izi kutsatira lamulo+ limene Atatewo anandipatsa. Nyamukani, tiyeni tichokeko kuno.

Mawu a M'munsi