Yohane 21:1-25

21  Zimenezi zitatha, Yesu anaonekeranso kwa ophunzirawo kunyanja ya Tiberiyo.* Kuonekera kwakeko kunali motere.  Simoni Petulo, Tomasi wotchedwa Didimo,+ Natanayeli+ wa ku Kana wa m’Galileya, ana a Zebedayo,+ ndi ophunzira ake ena awiri anali pamodzi.  Ndiyeno Simoni Petulo anati: “Ine ndikupita kukapha nsomba.” Enawonso anati: “Ifenso tipita nawe.” Iwo anapitadi ndi kukwera ngalawa, koma mkati mwa usiku umenewo sanaphe kanthu.+  Pamene kunali kucha, Yesu anaimirira m’mbali mwa nyanja, koma ophunzirawo sanazindikire kuti anali Yesu.+  Kenako Yesu anati: “Ana inu, kodi muli ndi chakudya chilichonse?” Iwo anamuyankha kuti, “Ayi!”  Iye anati: “Ponyani ukonde kumbali ya kudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.”+ Pamenepo anaponyadi ukondewo, koma sanathenso kuukoka chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.+  Zitatero, wophunzira amene Yesu anali kumukonda kwambiri uja+ anauza Petulo+ kuti: “Ndi Ambuye!” Pamenepo Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala malaya ake ovala pamwamba, pakuti anali maliseche,* ndipo analumphira m’nyanja.  Koma ophunzira enawo anabwera m’ngalawa yaing’ono akukoka ukonde wa nsomba, pakuti sanali patali kwenikweni ndi kumtunda. Anali pa mtunda wa mamita pafupifupi 90 okha.  Tsopano atafika kumtunda anaona moto wamakala+ uli potero pali nsomba, ndipo anaonanso mkate. 10  Yesu anati: “Bweretsani kuno zina mwa nsomba zimene mwaphazo.” 11  Choncho Simoni Petulo analowa m’ngalawamo ndi kukokera kumtunda ukonde wodzala nsomba zikuluzikulu zokwana 153. Koma ngakhale kuti munali nsomba zochuluka choncho, ukondewo sunang’ambike. 12  Yesu anawauza kuti: “Bwerani mudzadye chakudya cham’mawa.”+ Panalibe ngakhale mmodzi mwa ophunzirawo amene analimba mtima kumufunsa kuti: “Ndinu ndani?” chifukwa anali kudziwa kuti ndi Ambuye. 13  Yesu anapita kukatenga mkate ndi kuwagawira,+ chimodzimodzinso ndi nsomba. 14  Kameneka kanali kachitatu+ kwa Yesu kuonekera kwa ophunzira akewo pambuyo pakuti waukitsidwa kwa akufa. 15  Atatsiriza kudya chakudya cham’mawacho, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?”+ Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.”+ Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.”+ 16  Kenako anamufunsa kachiwiri kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?”+ Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, mukudziwa inunso kuti ndimakukondani kwambiri.” Pamenepo anati: “Weta ana a nkhosa anga.”+ 17  Anamufunsanso kachitatu: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda kwambiri?” Petulo anamva chisoni kumva akumufunsa kachitatu kuti: “Kodi ine umandikonda kwambiri?” Choncho iye anati: “Ambuye, inu mumadziwa zonse,+ mukudziwanso bwino kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anati: “Dyetsa ana a nkhosa anga.+ 18  Ndithudi ndikukuuza iwe, Pamene unali mnyamata, unali kuvala wekha ndi kupita kumene unali kufuna. Koma ukadzakalamba, udzatambasula manja ako ndipo munthu wina adzakuveka,+ ndi kukunyamula kupita nawe kumene iwe sukufuna.”+ 19  Ananena zimenezi pofuna kusonyeza mtundu wa imfa+ imene adzalemekeza nayo Mulungu.+ Choncho atanena zimenezi, anamuuza kuti: “Pitiriza kunditsatira.”+ 20  Petulo atatembenuka, anaona wophunzira amene Yesu anali kumukonda+ akuwalondola. Wophunzira ameneyu ndi amene pa chakudya chamadzulo chija anatsamira pachifuwa cha Yesu ndi kumufunsa kuti: “Ambuye, ndani amene akufuna kukuperekani?” 21  Pamene anamuona, Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, nanga uyu adzachita chiyani?” 22  Yesu anati: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe kufikira ndikadzabwera,+ kodi iwe uli nazo kanthu? Iweyo ungopitiriza kunditsatira.” 23  Atanena choncho, mawu amenewa anafalikira mwa abale, kuti wophunzira ameneyu sadzamwalira. Koma Yesu sanamuuze kuti sadzamwalira, koma ananena kuti: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe+ kufikira ndikadzabwera, kodi iwe uli nazo kanthu?” 24  Wophunzira ameneyu+ ndiye akuchitira umboni zinthu zimenezi. Iyeyu ndi amenenso analemba zinthu zimenezi, ndipo tikudziwa kuti umboni umene akupereka ndi woona.+ 25  Ndipo pali zinthu zinanso zambiri zimene Yesu anachita. Zikanakhala kuti zonse zinalembedwa mwatsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana m’dzikoli.+

Mawu a M'munsi

M’Baibulo, “nyanja ya Tiberiyo” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete, komanso nyanja ya Galileya.
Mawu achigiriki amene tawamasulira kuti “ali maliseche,” angatanthauze kuti “asanavale mokwanira” kapena “atavala zovala zamkati zokha,” osati ali mbulanda kapena asanavale chilichonse.