Yohane 7:1-53
7 Zimenezi zitatha, Yesu anapitiriza kuyendayenda mu Galileya. Iye sanafune kumayendayenda mu Yudeya, chifukwa Ayuda anali kufunitsitsa kumupha.+
2 Komabe chikondwerero cha Ayuda, chikondwerero cha misasa+ chinali pafupi.
3 Chotero abale ake+ anamupempha kuti: “Mupite ku Yudeya kuti ophunzira anunso akaone zimene mukuchita.
4 Pakuti palibe amene amachita kanthu mseri koma n’kumafuna kudziwika ndi anthu. Ngati inu mumachita zimenezi, mudzionetsere poyera kudzikoli.”
5 Abale akewo+ sanali kumukhulupirira.+
6 Chotero Yesu anati: “Nthawi yanga yoyenera sinakwanebe,+ koma kwa inu, iliyonse ndi nthawi yanu yoyenera.
7 Dziko lilibe chifukwa chodana ndi inu, koma limadana ndi ine, chifukwa ndimachitira umboni kuti dzikoli ntchito zake ndi zoipa.+
8 Inuyo nyamukani mupite ku chikondwereroko. Ine sindipitako panopa, chifukwa nthawi yanga yoyenera+ sinafike.”+
9 Atawauza zimenezi, iye anatsalira mu Galileya.
10 Koma abale akewo atanyamuka kupita ku chikondwereroko, iyenso ananyamuka payekha. Sanapite moonekera koma mwamseri.+
11 Chotero Ayuda anayamba kumufunafuna+ ku chikondwereroko. Iwo anali kunena kuti: “Kodi munthu ujayu ali kuti?”
12 Ndipo panali manong’onong’o ambiri onena za iye m’khamu lonse la anthulo.+ Ena anali kunena kuti: “Amene uja ndi munthu wabwino.” Ndipo ena anali kunena kuti: “Ayi si munthu wabwino amene uja, iye akusocheretsa anthu ambiri.”
13 Koma panalibe amene anali kulankhula poyera za iye chifukwa choopa Ayuda.+
14 Tsopano chikondwererocho chitafika pakatikati, Yesu analowa m’kachisi ndipo anayamba kuphunzitsa.+
15 Pamenepo Ayudawo anayamba kudabwa ndi kufunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu zolembazi anazidziwa bwanji,+ popeza sanapite kusukulu?”+
16 Yesu anawayankha kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga ayi, koma ndi za amene anandituma.+
17 Ngati munthu akufuna kuchita chifuniro cha amene ananditumayo, adzadziwa za chiphunzitsochi ngati chili chochokera kwa Mulungu,+ kapena ngati ndimalankhula za m’maganizo mwanga.
18 Wolankhula za m’maganizo mwake amadzifunira yekha ulemerero.+ Koma wofunira ulemerero iye amene anamutuma, ameneyu ali woona, ndipo mwa iye mulibe kusalungama.
19 Mose anakupatsani Chilamulo,+ si choncho kodi? Komatu palibe ngakhale mmodzi wa inu amene amamvera Chilamulocho. Nanga n’chifukwa chiyani inu mukufuna kundipha?”+
20 Khamu la anthulo linayankha kuti: “Uli ndi chiwanda iwe.+ Akufuna kukupha ndani?”
21 Poyankha Yesu anati: “Ndangochita chinthu chimodzi chabe,+ ndipo nonsenu mukudabwa.
22 Pa chifukwa chimenechi Mose anakupatsani mdulidwe.+ Sikuti mdulidwewo ndi wochokera kwa Mose ayi, koma ndi wochokera kwa makolo akale,+ ndipo mumachita mdulidwe tsiku la sabata.
23 Ngati munthu amadulidwa tsiku la sabata posafuna kuphwanya chilamulo cha Mose, kodi mukundipsera mtima ine chifukwa ndinachiritsa munthu tsiku la sabata?+
24 Lekani kuweruza poona maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”+
25 Pamenepo anthu ena okhala mu Yerusalemu anayamba kunena kuti: “Si ameneyu kodi akufuna kumupha uja?+
26 Koma taonani! Si uyu akulankhula poyera apa,+ ndipo palibe akunenapo kanthu kwa iye. Olamulirawo sakutsimikiza ngati iyeyo alidi Khristu eti?+
27 Koma ife tikudziwa kumene munthu ameneyu akuchokera.+ Komano Khristuyo akadzabwera, palibe amene adzadziwe kumene wachokera.”+
28 Chotero pamene anali kuphunzitsa m’kachisimo Yesu anafuula kuti: “Inu mukundidziwa ine komanso mukudziwa kumene ndikuchokera.+ Ndipo ine sindinabwere mwa kufuna kwanga,+ alipo ndithu amene anandituma,+ koma inu simukumudziwa.+
29 Ine ndikumudziwa,+ chifukwa ndine nthumwi. Iyeyu anandituma ine.”+
30 Pamenepo anayamba kufufuza njira yomugwirira,+ koma palibe amene anamugwira chifukwa nthawi yake+ inali isanafike.
31 Komabe ochuluka m’khamu la anthulo anakhulupirira mwa iye+ ndipo anayamba kunena kuti: “Akadzafika Khristu, kodi adzachita zizindikiro zochuluka+ kuposa zimene munthu uyu wachita?”
32 Afarisi anamva khamu la anthulo likunong’onezana motero za iye, ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma alonda kuti akamugwire.+
33 Pamenepo Yesu anati: “Ndikhala nanube kanthawi pang’ono ndisanapite kwa iye amene anandituma.+
34 Mudzandifunafuna,+ koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapiteko inu simudzatha kukafikako.”+
35 Chotero Ayudawo anayamba kufunsana kuti: “Ameneyu akufuna kupita kuti, kumene ife sitingathe kukam’peza? Kapena akufuna kupita kwa Ayuda omwazikana+ mwa Agiriki ndi kukaphunzitsa Agirikiwo?
36 Kodi akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mudzandifunafuna, koma simudzandipeza, ndipo kumene ine ndidzapite inu simudzatha kukafikako’?”
37 Tsopano pa tsiku lomaliza, tsiku lalikulu la chikondwererocho,+ Yesu anaimirira ndi kufuula kuti: “Ngati wina akumva ludzu,+ abwere kwa ine adzamwe madzi.
38 Wokhulupirira mwa ine,+ ‘Mkati mwake mwenimwenimo mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo,’ monga mmene Malemba amanenera.”+
39 Pamenepa anali kunena za mzimu umene onse okhulupirira mwa iye anali pafupi kulandira. Pakuti pa nthawiyi n’kuti asanaulandire,+ chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.+
40 Choncho ena m’khamulo, amene anamva mawu amenewa, anayamba kunena kuti: “Ameneyu ndi Mneneri ndithu.”+
41 Ena anali kunena kuti: “Khristu uja ndi ameneyu.”+ Koma ena anati: “Iyayi, kodi Khristu+ angachokere mu Galileya?+
42 Kodi Malemba sanena kuti Khristu adzatuluka mwa ana a Davide,+ komanso mu Betelehemu+ mudzi umene Davide anali kukhala?”+
43 Choncho khamu la anthulo linagawanika pa nkhani ya iye.+
44 Ena a iwo anali kufunitsitsa kumugwira, koma palibe ngakhale mmodzi amene anamukhudza.
45 Tsopano alonda aja anabwerera kwa ansembe aakulu ndi Afarisi. Ndiyeno iwowa anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani simunabwere naye?”
46 Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.”+
47 Pamenepo Afarisiwo anati: “Kodi inunso mwasocheretsedwa?
48 Palibe ndi mmodzi yemwe mwa olamulira kapena Afarisi amene wakhulupirira mwa iye, alipo ngati?+
49 Koma khamu lonseli la anthu osadziwa Chilamulo ndi lotembereredwa.”+
50 Nikodemo, amene m’mbuyomo anabwera kwa iye, komanso anali mmodzi wa iwo, anawauza kuti:
51 “Chilamulo chathu sichiweruza munthu asanafotokoze maganizo ake choyamba+ ndi kudziwa zochita zake, chimatero ngati?”
52 Poyankha iwo anati: “Kodi iwenso ndiwe wochokera ku Galileya eti? Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati m’Galileya mudzatuluka mneneri.”*+
* Mipukutu ya Codex Sinaiticus, Codex Vaticanus ndi Sinaitic Syriac, inachotsa vesi 53 mpaka chaputala 8, vesi 11. (M’mabuku ambiri Achigiriki mawu a mavesi amenewa amasiyanasiyana.) Ndimezi zili ndi mawu akuti:
53 Zitatero aliyense ananyamuka n’kupita kwawo.