Yohane 7:53–8:59
* Mipukutu ya Codex Sinaiticus, Codex Vaticanus ndi Sinaitic Syriac, inachotsa vesi 53 mpaka chaputala 8, vesi 11. (M’mabuku ambiri Achigiriki mawu a mavesi amenewa amasiyanasiyana.) Ndimezi zili ndi mawu akuti:
53 Zitatero aliyense ananyamuka n’kupita kwawo.
8 Kenako Yesu anapita kuphiri la Maolivi.
2 M’mawa kwambiri, anafikanso kukachisi ndipo anthu onse anayamba kubwera kwa iye. Choncho iye anakhala pansi ndi kuyamba kuwaphunzitsa.
3 Tsopano alembi ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Ndipo atamuimika pakati pawo,
4 anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa akuchita chigololo.
5 M’Chilamulo, Mose analamula kuti akazi oterewa tiziwaponya miyala. Nanga inu mukutipo bwanji?”
6 Iwo kwenikweni anali kunena zimenezi pofuna kungomuyesa, kuti amupeze chifukwa chomuimbira mlandu. Koma Yesu anawerama ndi kuyamba kulemba pansi ndi chala chake.
7 Atalimbikira kumufunsa, iye anaweramuka ndi kuwauza kuti: “Munthu amene ali wopanda tchimo pakati panu, ayambe iyeyo kumuponya mwala mkaziyu.”
8 Kenako anaweramanso ndi kupitiriza kulemba pansi.
9 Koma iwo atamva zimenezi, anayamba kuchoka mmodzimmodzi. Oyamba kuchoka anali akulu, mpaka Yesu anamusiya yekha ndi mkazi amene anali pakati pawo uja.
10 Tsopano Yesu ataweramuka, anafunsa mkaziyo kuti: “Mayi iwe, anthu aja ali kuti? Kodi palibe amene waona kuti ndiwe woyenera kulangidwa?”
11 Mkaziyo anati: “Palibe bambo.” Ndiyeno Yesu anati: “Inenso sindikuona kuti ndiwe woyenera kulangidwa. Pita, kuyambira lero usakachitenso tchimo.”
12 Pamenepo Yesu analankhula nawonso kuti: “Ine ndine kuwala+ kwa dziko. Wonditsatira ine sadzayenda mumdima,+ koma adzakhala nako kuwala kwa moyo.”
13 Chotero Afarisi anauza Yesu kuti: “Iwe umadzichitira wekha umboni koma umboni wakowo si woona ayi.”
14 Poyankha Yesu anati: “Ngakhale kuti ndimadzichitira ndekha umboni,+ umboni wanga ndi woona, chifukwa ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita.+ Koma inu simukudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita.
15 Inu mumaweruza mwa kungoona maonekedwe a munthu.+ Inetu sindiweruza munthu aliyense.+
16 Koma ndikati ndiweruze, chiweruzo changa chimakhala cholungama, chifukwa sindiweruza ndekha, pakuti Atate amene anandituma ali ndi ine.+
17 Ndiponso m’Chilamulo chanu chomwechi analembamo kuti, ‘Umboni wa anthu awiri ndi woona.’+
18 Ineyo pandekha ndimadzichitira umboni, ndipo Atate amene anandituma amandichitiranso umboni.”+
19 Pamenepo iwo anati: “Atate wako ali kuti?” Yesu anayankha kuti: “Inu simukundidziwa ine kapena Atate wanga.+ Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga.”+
20 Ananena mawu amenewa ali m’malo a zopereka+ pamene anali kuphunzitsa m’kachisi. Koma palibe amene anamugwira,+ chifukwa nthawi yake+ inali isanafikebe.
21 Choncho iye anawauzanso kuti: “Ine ndikuchoka ndipo mudzandifunafuna,+ koma mudzafabe m’tchimo lanu.+ Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako.”
22 Pamenepo Ayudawo anayamba kunena kuti: “Kodi akufuna kudzipha? Nanga n’chifukwa chiyani akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita inu simungathe kukafikako?’”+
23 Iye anawauza kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano, ine ndine wochokera kumwamba.+ Inu ndinu ochokera m’dziko lino,+ ine si wochokera m’dziko lino.+
24 N’chifukwa chake ndakuuzani kuti, Inu mudzafa m’machimo anu.+ Pakuti ngati simukhulupirira kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja, mudzafa m’machimo anu.”+
25 Choncho iwo anayamba kunena kuti: “Kodi iwe ndiwe ndani?” Yesu anati: “N’chifukwa chiyani ndikudzivuta kulankhula nanu?
26 Ndili ndi zambiri zoti ndinene zokhudza inu ndi kuperekerapo chiweruzo. Ndipotu amene anandituma ine amanena zoona. Zimene ndinamva kwa iye, zomwezo ndikuzilankhula m’dzikoli.”+
27 Iwo sanazindikire kuti anali kunena za Atatewo.
28 Pamenepo Yesu anati: “Mukadzamukweza+ Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine amene munali kumuyembekezera uja,+ ndi kutinso sindichita kanthu mongoganiza ndekha.+ Koma ndimalankhula zinthu izi ndendende mmene Atate anandiphunzitsira.+
29 Ndipo amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sandisiya ndekha, chifukwa ndimachita zinthu zomukondweretsa nthawi zonse.”+
30 Pamene anali kulankhula zimenezi, ambiri anakhulupirira mwa iye.+
31 Chotero Yesu anapitiriza kuuza Ayuda amene anamukhulupirirawo kuti: “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse,+ ndiye kuti ndinudi ophunzira anga.
32 Mudzadziwa choonadi,+ ndipo choonadi chidzakumasulani.”+
33 Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu ndife ana a Abulahamu+ ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu.+ Tsopano iwe ukunena bwanji kuti, ‘Mudzamasulidwa’?”
34 Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimo.+
35 Komanso, kapolo sakhala m’banjamo kwamuyaya, mwana ndiye amakhalamo kwamuyaya.+
36 Choncho ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.+
37 Ndikudziwa kuti ndinu ana a Abulahamu, koma mukufuna kundipha,+ chifukwa mawu anga sakukhazikika mwa inu.+
38 Zimene ndinaziona kwa Atate wanga+ ndi zimene ndimalankhula.+ Chotero inunso mumachita zimene mwamva kwa atate wanu.”
39 Poyankha iwo anati: “Atate wathu ndi Abulahamu.”+ Yesu anawauza kuti: “Ngati ndinu ana a Abulahamu,+ chitani ntchito za Abulahamu.
40 Koma tsopano mukufuna kundipha ine, munthu amene ndakuuzani choonadi chimene ndinachimva kwa Mulungu.+ Abulahamu sanachite zimenezi.+
41 Inu mumachita ntchito za atate wanu.” Iwo anati: “Ife sitinabadwe m’chigololo,* tili ndi Atate mmodzi,+ ndiye Mulungu.”
42 Pamenepo Yesu anati: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda,+ pakuti ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano.+ Sindinabwere mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.+
43 N’chifukwa chiyani mukulephera kuzindikira zimene ine ndikunena? N’chifukwa chakuti simukufuna kumvetsera mawu anga.+
44 Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi,+ ndipo mukufuna kuchita zokhumba za atate wanu.+ Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake,+ ndipo sanakhazikike m’choonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.+
45 Koma popeza ine ndimanena zoona, simundikhulupirira.+
46 Ndani wa inu amene angandipeze ndi mlandu wa tchimo? Ndipo ngati ndimanena zoona, n’chifukwa chiyani simundikhulupirira?+
47 Wochokera kwa Mulungu amamvetsera mawu a Mulungu.+ Ndiye chifukwa chake inu simumvetsera, chifukwa sindinu ochokera kwa Mulungu.”+
48 Poyankha Ayudawo anati: “Kodi tikamanena kuti, Ndiwe Msamariya+ ndipo uli ndi chiwanda,+ tikulakwitsa ngati?”
49 Yesu anayankha kuti: “Ndilibe chiwanda ine, ndimalemekeza Atate wanga,+ koma inu mukundinyoza.
50 Komatu ine sindikudzifunira ndekha ulemerero.+ Alipo Wina amene akuufuna ndipo iye ndi woweruza.+
51 Ndithudi ndikukuuzani, ngati munthu akusunga mawu anga, sadzaona imfa.”+
52 Ayudawo anati: “Tsopano tadziwa ndithu kuti uli ndi chiwanda.+ Abulahamu anamwalira,+ ndiponso aneneri.+ Koma iwe ukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga sadzalawa+ imfa.’
53 Kodi iweyo ndiwe wamkulu+ kuposa atate wathu Abulahamu amene anamwalira? Aneneri nawonso anamwalira.+ Ndiye iweyo ukudziyesa ndani?”
54 Yesu anayankha kuti: “Ngati ndikudzilemekeza ndekha, ndiye kuti ulemerero wanga ndi wopanda pake. Atate wanga ndi amene amandilemekeza,+ amene inu mukuti ndi Mulungu wanu,
55 chikhalirecho simukumudziwa.+ Koma ine ndikumudziwa.+ Ngati ndinganene kuti sindikumudziwa ndingakhale wabodza, kufanana ndi inuyo. Koma ndikumudziwa ndithu ndipo ndikusunga mawu ake.+
56 Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezera kuona tsiku langa,+ ndipo analiona moti anakondwera.”+
57 Pamenepo Ayudawo anati: “Zaka 50 zakubadwa sunakwanitse n’komwe, ndiye ukuti unamuona Abulahamu?”
58 Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko, ine n’kuti ndilipo kale.”+
59 Pamenepo anatola miyala kuti amugende nayo,+ koma Yesu anabisala ndi kutuluka m’kachisimo.
Mawu a M'munsi
^ Onani Zakumapeto 7.