Yona 3:1-10

3  Yehova analankhula ndi Yona kachiwiri kuti:+  “Nyamuka, upite kumzinda waukulu wa Nineve, ndipo kumeneko ukalalikire+ zimene ndikuuze.”  Pamenepo Yona ananyamuka ndi kupita ku Nineve mogwirizana ndi mawu a Yehova.+ Mzinda wa Nineve unali waukulu pamaso pa Mulungu,+ ndipo mtunda wake unali woyenda masiku atatu.  Kenako Yona analowa mumzindawo ndi kuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye anali kulalikira kuti: “Kwangotsala masiku 40 okha ndipo Nineve awonongedwa.”+  Anthu a ku Nineve anayamba kukhulupirira Mulungu+ ndipo anayamba kulengeza kuti aliyense, popanda wotsala, asale kudya ndipo avale ziguduli.*+  Uthengawo utafika kwa mfumu ya Nineve,+ mfumuyo inanyamuka pampando wake wachifumu ndi kuvula chovala chake chachifumu. Ndiyeno inavala chiguduli ndi kukhala paphulusa.+  Kuwonjezera pamenepo, mfumu ndi akuluakulu ake analamula anthu kuti alengeze mu Nineve kuti: “Munthu aliyense, chiweto, ng’ombe ndi nkhosa iliyonse zisadye chilichonse. Munthu aliyense kapena chiweto zisadye chakudya kapena kumwa madzi.+  Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu ndi mphamvu zawo zonse, ndipo aliyense asiye njira zake zoipa+ ndi zinthu zonse zachiwawa zimene amachita.  Ndani angadziwe? Mwina Mulungu woona satigwetsera tsoka ndipo asintha maganizo+ ndi kubweza mkwiyo wake woyaka moto, moti satiwononga.”+ 10  Ndiyeno Mulungu woona anaona ntchito zawo.+ Anaona kuti alapa ndi kusiya njira zawo zoipa.+ Choncho, Mulungu woona anasintha maganizo ake+ pa tsoka limene ananena kuti awabweretsera, moti sanawabweretsere.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “masaka.”