Yoswa 12:1-24
12 Tsopano awa ndi mafumu amene ana a Isiraeli anagonjetsa n’kulanda madera awo, kumbali yotulukira dzuwa+ ya mtsinje wa Yorodano. Analanda kuchokera kuchigwa* cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba+ konse, kumbali yotulukira dzuwa. Mafumu ake ndi awa:
2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni.+ Dera lomwe anali kulamulira linkayambira pakatikati pa chigwa cha Arinoni kuphatikizapo mzinda wa Aroweli,+ umene unali m’mphepete mwa mtsinje wa Arinoni,+ mpaka hafu ya Giliyadi kukalekezera kuchigwa cha Yaboki,+ kumalire ndi ana a Amoni.
3 Anali kulamuliranso chigwa cha Araba+ mpaka kunyanja ya Kinereti+ kumbali ya kum’mawa kwa nyanjayi, n’kukafikanso kunyanja ya Araba, yomwe ndi Nyanja Yamchere.+ Anali kulamulira kumbali ya kum’mawa kwa nyanjayi, cha ku Beti-yesimoti,+ mpaka kum’mwera, kumunsi kwa Pisiga.+
4 Mfumu ina ndi Ogi+ wa ku Basana yemwe anali mmodzi mwa Arefai+ otsala, ndipo ankakhala ku Asitaroti+ ndi ku Edirei.+
5 Anali kulamulira kuphiri la Herimoni,+ ku Saleka, ndi ku Basana+ konse, mpaka kukafika kumalire a Agesuri+ ndi Amaakati.+ Anali kulamuliranso hafu ya Giliyadi, mpaka kumalire ndi dera limene Sihoni,+ mfumu ya Hesiboni,+ anali kulamulira.
6 Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Isiraeli ndiwo anagonjetsa mafumuwa.+ Atatero, Mose mtumiki wa Yehova anapereka dzikoli kwa Arubeni,+ Agadi,+ ndi hafu ya fuko la Manase,+ kuti likhale lawo.
7 Yoswa ndi ana a Isiraeli anagonjetsa mafumu a kudera la kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera ku Baala-gadi+ kuchigwa cha Lebanoni+ mpaka kuphiri la Halaki,+ limene lili moyang’anizana ndi Seiri.+ Atawagonjetsa, Yoswa anapereka dzikolo kwa mafuko a Isiraeli poligawa m’magawomagawo.+
8 Dzikoli linkaphatikizapo dera lamapiri, dera la Sefela, chigwa cha Araba, malo otsetsereka, chipululu, ndi Negebu.+ Limeneli linali dziko la Ahiti, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi.+ Mafumu awo anali awa:
9 Mfumu ya Yeriko,+ imodzi. Mfumu ya Ai+ pafupi ndi Beteli, imodzi.
10 Mfumu ya Yerusalemu,+ imodzi. Mfumu ya Heburoni,+ imodzi.
11 Mfumu ya Yarimuti,+ imodzi. Mfumu ya Lakisi,+ imodzi.
12 Mfumu ya Egiloni,+ imodzi. Mfumu ya Gezeri,+ imodzi.
13 Mfumu ya Debiri,+ imodzi. Mfumu ya Gederi, imodzi.
14 Mfumu ya Horima, imodzi. Mfumu ya Aradi, imodzi.
15 Mfumu ya Libina,+ imodzi. Mfumu ya Adulamu, imodzi.
16 Mfumu ya Makeda,+ imodzi. Mfumu ya Beteli,+ imodzi.
17 Mfumu ya Tapuwa, imodzi. Mfumu ya Heferi,+ imodzi.
18 Mfumu ya Afeki, imodzi. Mfumu ya Lasaroni, imodzi.
19 Mfumu ya Madoni,+ imodzi. Mfumu ya Hazori,+ imodzi.
20 Mfumu ya Simironi-meroni, imodzi. Mfumu ya Akasafu,+ imodzi.
21 Mfumu ya Taanaki, imodzi. Mfumu ya Megido,+ imodzi.
22 Mfumu ya Kadesi, imodzi. Mfumu ya Yokineamu+ ku Karimeli, imodzi.
23 Mfumu ya Dori kumapiri a Dori,+ imodzi. Mfumu ya Goimu ku Giligala, imodzi.
24 Mfumu ya Tiriza, imodzi. Mafumu onse analipo 31.+