Yoswa 18:1-28
18 Kenako khamu lonse la ana a Isiraeli linasonkhana ku Silo,+ ndipo kumeneko anamangako chihema chokumanako,+ popeza anali atagonjetsa dziko lomwe linali pamaso pawo.+
2 Koma mafuko 7 a ana a Isiraeli anali asanagawiridwe cholowa.
3 Choncho Yoswa anafunsa ana a Isiraeli kuti: “Kodi muzengereza mpaka liti osapita kukalanda dziko+ limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani?+
4 Sankhani amuna atatu pafuko lililonse oti ndiwatume apite akayendere dzikolo. Akalembe mmene dzikolo lilili kuti lidzagawidwe monga cholowa cha mafuko awo, akakatero adzabwerere kwa ine.+
5 Ndiyeno adzagawane dzikolo poligawa m’zigawo 7.+ Fuko la Yuda lidzakhalabe kugawo lawo kum’mwera,+ ndipo a nyumba ya Yosefe adzakhalabe kugawo lawo kumpoto.+
6 Koma anthu inu, mukagawe dzikolo m’zigawo 7 ndipo mukazilembe. Mukakatero, mukabwere nazo kuno kwa ine kuti ndidzakuchitireni maere+ pamaso pa Yehova Mulungu wathu.
7 Alevi alibe gawo pakati panu,+ chifukwa cholowa chawo ndi unsembe wa Yehova.+ Fuko la Gadi, Rubeni,+ ndi hafu ya fuko la Manase+ analandira kale cholowa chawo, chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa kutsidya la kum’mawa la Yorodano.”+
8 Choncho amuna opita kukalemba dzikowo ananyamuka kuti azipita, ndipo Yoswa anawalamula+ kuti: “Pitani mukayendere dzikolo n’kulemba mmene lilili. Mukatero mubwerere kwa ine, ndipo ineyo ndidzakuchitirani maere+ pamaso pa Yehova kuno ku Silo.”+
9 Pamenepo amunawo anapitadi kukayendera dzikolo. Anakaligawa+ m’zigawo 7 potsatira mizinda yake, n’kulemba m’buku. Atamaliza, anapita kwa Yoswa kumsasa ku Silo,
10 ndipo Yoswa anawachitira maere pamaso pa Yehova+ ku Silo. Kumeneko Yoswa anagawa dzikolo n’kupereka gawo limodzilimodzi ku mafuko a ana a Isiraeli.+
11 Maere+ oyamba anagwera fuko la ana a Benjamini+ potsata mabanja awo, ndipo gawo limene anapatsidwa linali pakati pa ana a Yuda+ ndi ana a Yosefe.+
12 Malire a gawo lawo kumpoto anayambira ku Yorodano, n’kupitirira kukafika kumalo otsetsereka a kumpoto kwa Yeriko,+ n’kukwera phiri chakumadzulo, n’kukathera kuchipululu cha Beti-aveni.+
13 Malirewo anapitirira kukafika ku Luzi,+ kutanthauza Beteli.+ Anakafika kum’mwera kwa malo otsetsereka otchedwa Luzi, n’kutsetserekera ku Ataroti-adara,+ n’kukadutsa paphiri la kum’mwera kwa Beti-horoni Wakumunsi.+
14 Kumadzulo kwa gawolo, malirewo anakhotera kum’mwera, paphiri loyang’anizana ndi kum’mwera kwa Beti-horoni. Kuchokera pamenepo anakathera ku Kiriyati-baala, kutanthauza Kiriyati-yearimu,+ womwe ndi mzinda wa ana a Yuda. Awa ndiwo malire a kumadzulo a gawo la Benjamini.
15 Malire a kum’mwera a gawolo anayambira kumapeto kwa Kiriyati-yearimu, n’kulowera chakumadzulo, n’kupitirira kukafika kukasupe wa madzi a Nafitoa.+
16 Malirewo anatsetserekera kuphiri loyang’anizana ndi chigwa cha mwana wa Hinomu,+ limene linathera kumpoto kwa chigwa cha Arefai.+ Kenako anatsetserekera kuchigwa cha Hinomu kum’mwera kwa malo otsetsereka otchedwa Yebusi,+ n’kutsetserekabe mpaka ku Eni-rogeli.+
17 Analowera chakumpoto n’kukafika ku Eni-semesi mpaka ku Gelilotu, yemwe ali kutsogolo kwa chitunda cha Adumi.+ Kuchokera pamenepo, anatsetserekera kumwala+ wa Bohani,+ mwana wa Rubeni.
18 Ndiyeno anakafika kumalo otsetsereka a kumpoto amene ali kutsogolo kwa Araba, n’kutsetserekera ku Araba.
19 Malirewo anapitirira mpaka kumalo otsetsereka a kumpoto kwa Beti-hogila,+ n’kukathera kugombe la kumpoto kwa Nyanja Yamchere,+ kumapeto a kum’mwera a mtsinje wa Yorodano. Awa anali malire a kum’mwera a gawo la Benjamini.
20 Kum’mawa, malire ake anali mtsinje wa Yorodano. Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini potsata mabanja awo, ndi malire ake kuzungulira gawo lonse.
21 Mizinda ya fuko la ana a Benjamini potsata mabanja awo inali Yeriko,+ Beti-hogila, Emeki-kezizi,
22 Beti-araba,+ Zemaraimu, Beteli,+
23 Aavi, Para, Ofira,+
24 Kefara-amoni, Ofini, ndi Geba.+ Mizinda 12 ndi midzi yake.
25 Kunalinso Gibeoni,+ Rama, Beeroti,
26 Mizipe,+ Kefira,+ Moza,
27 Rekemu, Iripeeli, Tarala,
28 Zela,+ Ha-elefi, Yebusi, kutanthauza Yerusalemu,+ Gibea,+ ndi Kiriyati. Mizinda 14 ndi midzi yake.
Ichi chinali cholowa cha ana a Benjamini potsata mabanja awo.+