Yoswa 3:1-17
3 M’mamawa kutacha, Yoswa ndi ana a Isiraeli onse ananyamuka ku Sitimu.+ Anayenda mpaka kukafika kumtsinje wa Yorodano, kumene anagona usiku umenewo asanawoloke.
2 Patatha masiku atatu aja,+ akapitawo+ a anthuwo anapita mumsasa,
3 ndipo anauza anthuwo kuti: “Mukangoona likasa la pangano la Yehova Mulungu wanu litanyamulidwa ndi ansembe achilevi,+ musamuke pamalo panu ndi kulitsatira,
4 koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi likasalo pakhale mtunda wokwana mikono* pafupifupi 2,000.+ Mukatero, mudzadziwa njira yoyenera kuyendamo, pakuti kumeneko simunayambe mwapitako.”
5 Tsopano Yoswa anauza anthuwo kuti: “Mudziyeretse,+ chifukwa mawa Yehova achita zodabwitsa pakati panu.”+
6 Kenako Yoswa anauza ansembe kuti: “Nyamulani likasa la pangano,+ muyende nalo patsogolo pa anthuwa.” Chotero ansembewo ananyamula likasa la panganolo, n’kumayenda nalo patsogolo pa anthuwo.
7 Ndipo Yehova anauza Yoswa kuti: “Lero ndiyamba kukukuza pamaso pa Aisiraeli onse,+ n’cholinga choti adziwe kuti monga mmene ndinakhalira ndi Mose,+ ndidzakhalanso ndi iwe.+
8 Tsopano lamula+ ansembe onyamula likasa la pangano. Uwauze kuti: ‘Mukakangofika kumtsinje wa Yorodano, mukalowe m’madzimo ndi kuima+ m’mphepete mwa mtsinjewo.’”
9 Ndiyeno Yoswa anauza ana a Isiraeli kuti: “Bwerani kuno, mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu.”
10 Atafika, Yoswa anati: “Mukaona zimene zichitike pano, mudziwa kuti Mulungu wamoyo alidi pakati panu.+ Mudziwanso kuti iye adzathamangitsadi pamaso panu Akanani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi.+
11 Taonani! Likasa la pangano la Ambuye wa dziko lonse lapansi liyenda patsogolo panu kulowa mumtsinje wa Yorodano.
12 Tsopano tengani amuna 12 m’mafuko a Isiraeli, mwamuna mmodzi pafuko lililonse.+
13 Zimene zichitike n’zakuti, mapazi a ansembe onyamula likasa la Yehova, Ambuye wa dziko lonse lapansi, akangoponda m’madzi, madzi a mtsinje wa Yorodanowo aduka. Madzi otsika kuchokera kumtunda aima n’kukhala damu limodzi.”+
14 Ndipo zimenezi zinachitikadi. Anthuwo anachotsa mahema awo, n’kunyamuka. Anayandikira Yorodano kuti awoloke, ndipo ansembe onyamula likasa+ la pangano anali patsogolo pawo.
15 Onyamula Likasawo atangofika kumtsinje wa Yorodano, n’kuponda madzi a m’mphepete mwa mtsinjewo (mtsinje wa Yorodano unali kusefukira+ nyengo yonse yokolola),
16 madzi otsika kuchokera kumtunda anayamba kuima. Madziwo anakwera m’mwamba, ndipo anasefukira n’kupanga damu,+ limene linafika kutali kwambiri. Izi zinachitikira ku Adamu, mzinda woyandikana ndi mzinda wa Zeretani.+ Koma madzi omwe anali kutsikira kunyanja ya Araba, imene ndiyo Nyanja Yamchere,+ anaphwa. Choncho, madzi a mtsinjewo anaduka, ndipo anthuwo anawolokera kutsidya lina, pafupi ndi Yeriko.
17 Ansembe onyamula likasa la pangano la Yehova anangoima chilili panthaka youma+ pakati pa mtsinje wa Yorodano. Anaimabe choncho pamene Aisiraeli onse anali kuwoloka panthaka youmayo,+ kufikira mtundu wonse unatha kuwoloka mtsinje wa Yorodano.
Mawu a M'munsi
^ Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.