Zekariya 3:1-10

3  Ndiyeno Mulungu anandionetsa Yoswa+ mkulu wa ansembe, ataimirira pamaso pa mngelo wa Yehova. Pa nthawiyi Satana+ anali ataimirira kudzanja lamanja la Yoswa kuti azim’tsutsa.+  Kenako mngelo+ wa Yehova anauza Satana kuti: “Iwe Satana, Yehova akudzudzule!+ Yehova amene anasankha Yerusalemu akudzudzule!+ Kodi munthu uyu si chikuni chimene chaphulidwa pamoto msangamsanga?”+  Pa nthawi imene Yoswa anaimirira pamaso pa mngelo, anali atavala zovala zonyansa.+  Ndiyeno mngeloyo anauza amene anaimirira pamaso pake kuti: “Muvuleni zovala zonyansazi.” Kenako anauza Yoswa kuti: “Waona, ndakuchotsera zolakwa zako,+ ndipo wavekedwa mikanjo yapadera.”+  Pamenepo ndinanena kuti: “Auzeni kuti amuveke nduwira* yoyera kumutu kwake.”+ Ndipo anamuvekadi nduwira yoyera kumutu kwake. Anamuvekanso zovala. Apa n’kuti mngelo wa Yehova ataimirira pambali pake.  Mngelo wa Yehova uja anayamba kulimbikitsa Yoswa kuti:  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ukayenda m’njira zanga ndi kusunga malamulo anga,+ udzakhala woweruza wa anthu a m’nyumba yanga+ ndipo uzidzayang’anira mabwalo a nyumba yanga. Ndithu ndidzakulola kumafika pamaso panga limodzi ndi amene aima panowa.’  “‘Tamvera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi pamaso pako, pakuti iwo ndi amuna amene ali ngati zizindikiro zolosera zam’tsogolo.+ Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+  Taonani mwala+ umene ndauika pamaso pa Yoswa. Mwala umenewu uli ndi maso 7.+ Pamwalawu ndilembapo zinthu mochita kugoba,+ ndipo ndidzachotsa zolakwa za dzikoli m’tsiku limodzi,’+ watero Yehova wa makamu. 10  “‘Pa tsiku limenelo mudzaitanizana, aliyense atakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndiponso wa mkuyu,’+ watero Yehova wa makamu.”

Mawu a M'munsi

“Nduwira” ndi chovala chansalu chakumutu chimene amachimanga ngati duku.